Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi a Mboni za Yehova Amalandira Chithandizo Chachipatala?

Kodi a Mboni za Yehova Amalandira Chithandizo Chachipatala?

Yesu ananena kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” (Mateyu 9:12) Pamenepa iye anasonyeza kuti Malemba saletsa munthu kupeza chithandizo chachipatala. Choncho a Mboni za Yehova amamwa mankhwala akuchipatala ndiponso amalandira chithandizo chosiyanasiyana chimene achipatala amapereka. Iwo amafuna kukhala ndi thanzi labwino komanso moyo wautali. Ndipotu mofanana ndi Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi monga Luka, a Mboni za Yehova ena ndi madokotala.​—Akolose 4:14.

Komabe a Mboni za Yehova salandira chithandizo cha mankhwala chimene chimasemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, iwo salola kuikidwa magazi ndipo zimenezi zili choncho chifukwa chakuti Baibulo limaletsa kulowetsa magazi m’thupi la munthu n’cholinga chothandiza thupilo. (Genesis 9:4; Levitiko 17:1-14; Machitidwe 15:28, 29) Mawu a Mulungu amaletsanso mankhwala kapena njira zochizira zokhudzana ndi kugwiritsa ntchito “mphamvu zamatsenga” kapena zamizimu.​—Yesaya 1:13; Agalatiya 5:19-21.

Masiku ano pali madokotala ambiri amene amathandiza odwala pogwiritsa ntchito njira zimene sizisemphana ndi mfundo za m’Baibulo. A Mboni za Yehova amasankha njira zimenezi ndipo kawirikawiri zimakhala zothandiza kwambiri poyerekezera ndi njira zina zosagwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.

N’zoona kuti pa nkhani zaumoyo, anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana. Zimene zingakhale zothandiza kwa munthu wina sizingakhale zothandiza kwa wina. Choncho, anthu amene akufuna kudziwa bwino matenda amene akudwala ndiponso akufuna kulandira thandizo loyenera, angachite bwino kuonana ndi madokotala angapo.​—Miyambo 14:15.

Sikuti a Mboni za Yehova onse angasankhe zofanana pa nkhani ya thandizo lachipatala. Ngati palibe lamulo la m’Baibulo limene likuswedwa, Mawu a Mulungu amalola kuti Mkhristu aliyense asankhe yekha chochita malinga ndi chikumbumtima chake. (Aroma 14:2-4) Choncho munthu aliyense ayenera kufufuza thandizo limene madokotala akufuna kumupatsa. Iye ayenera kuchita zimenezi n’cholinga chakuti adziwe ngati silikutsutsana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo.​—Agalatiya 6:5; Aheberi 5:14.

Posankha chithandizo chamankhwala, wa Mboni amakhala ngati dalaivala amene akuyandikira malo amene misewu inadutsana. Ngati podutsa pamalo amenewa dalaivala akungotsatira galimoto zina ndipo akuthamanga kwambiri, angachite ngozi yoopsa. Dalaivala wanzeru amayendetsa galimoto pang’onopang’ono ndipo amayang’anitsitsa mmene magalimoto ena akuyendera. Mofanana ndi zimenezi, a Mboni samachita zinthu mopupuluma pa nkhani yosankha chithandizo chamankhwala ndipo sachita zinthu pongotsatira zimene anthu ambiri akuchita. M’malomwake, asanasankhe zochita amaganizira mofatsa zimene akufuna kuchitazo ndipo amaganizira kaye zimene Baibulo limanena.

A Mboni za Yehova amaona kuti ntchito imene madokotala komanso anthu ena azachipatala akugwira ndi yofunika kwambiri ndipo amayamikira khama limene anthu amenewa amasonyeza. Iwo amayamikiranso madokotala chifukwa cha mpumulo umene amapeza madokotalawo akawapatsa thandizo pa matenda awo.