Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima mwa Munthu?

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima mwa Munthu?

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima mwa Munthu?

Papa Benedict wa 16 analemba m’buku lake kuti: “Ufumu wa Mulungu umabwera mwa munthu, munthuyo akakhala ndi mtima womvetsera.” (Jesus of Nazareth) Anthu ena amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi kusintha kumene kumachitika mumtima wa munthu, munthuyo akalandira Yesu Khristu ndiponso akakhala ndi chikhulupiriro. Kodi ndi zoona kuti Ufumu wa Mulungu umangotanthauza kusintha kumene munthu amachita mumtima mwake, kutanthauza kuti ‘umangokhala mumtima mwa munthuyo?’

YESU ankaona kuti Ufumu unalidi chinthu chofunika kwambiri kwa iye. Ndipo Papa Benedict analemba kuti, “mfundo yaikulu ya ulaliki wa Yesu” inali Ufumu wa Mulungu. Pa nthawi yochepa imene Yesu anachita utumiki wake, anayendayenda m’madera ambiri “kulalikira uthenga wabwino wa ufumu.” (Mateyu 4:23) Zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso zozizwitsa zimene anachita, zinasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndipo siumangotanthauza kumvera ndiponso kukhulupirira Mulungu. M’malomwake umaphatikizapo ulamuliro, chiweruzo komanso madalitso osatha amene Ufumuwo udzabweretse.

Ulamuliro Komanso Chiweruzo

Nthawi ina kutatsala masiku ochepa kuti Yesu amalize utumiki wake wa padziko lapansi, amayi a Yakobo ndi Yohane, omwe anali atumwi ake amene ankawakonda kwambiri anauza Yesu kuti: “Lonjezani kuti ana angawa adzakhala, mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu, mu ufumu wanu.” (Mateyu 20:21) Apa n’zoonekeratu kuti mayiyu sankatanthauza kuti Ufumu ndi chinthu chimene chinali mumtima mwa ana akewo. Iye ankadziwa kuti Yesu ndi wolamulira wa Ufumu umenewu ndipo ankafuna kuti ana akewo akalamulire naye. Ndipotu Yesu analonjeza atumwi ake 11 okhulupirika kuti adzakhala mu Ufumu wake ndipo ‘adzakhala m’mipando yachifumu’ ndi “kuweruza” naye limodzi. (Luka 22:30) Zimenezi zikusonyeza kuti otsatira a Yesu ankadziwa kuti Ufumu wa Yesu ndi boma lenileni lolamulira anthu.

Nangano kodi anthu ena onse pa nthawi imeneyo ankaona kuti Ufumu ndi chiyani? Kodi iwo ankaganiza kuti Ufumu umangotanthauza kusintha kumene munthu amapanga, kapena ankaona kuti ndi chinthu chapadera? Pasika wa mu 33 C.E atangotsala pang’ono kuchitika, Yesu analowa mu Yerusalemu atakwera pabulu. Chigulu cha anthu chinamuchingamira ndipo anthuwo ankaimba kuti: “M’pulumutseni Mwana wa Davide!” (Mateyu 21:9) Kodi n’chifukwa chiyani anthuwa anafuula choncho? Chifukwa iwo anazindikira kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa ndipo Mulungu adzam’patsa Ufumu, “mpando wachifumu wa Davide atate wake,” umene sudzatha. Iwo ankayembekezera chipulumutso, mtendere ndiponso chilungamo zimene Ufumu umenewu udzabweretse.​—Luka 1:32; Zekariya 9:9.

Ufumu Udzabweretsa Madalitso Amuyaya

Ngakhale anthu amene ankaoneka kuti analibe chidwi kwenikweni ndi zimene Yesu ankaphunzitsa, ankadziwa kuti iye ankalalikira za Ufumu. Pa nthawi imene Yesu ankaphedwa, munthu wina amene anali chigawenga ndipo anapachikidwa limodzi ndi Yesu anamuchonderera kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Poyankha, Yesu anatsimikizira munthu amene anali atatsala pang’ono kufayo kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”​—Luka 23:42, 43.

Chigawenga chimenechi chinkadziwa kuti Yesu akafa n’kuukitsidwa, adzapatsidwa Ufumu kapena kuti adzalowa mu Ufumu. Yesu ali ndi mphamvu zotha kuukitsa ndi kusintha munthu ameneyu komanso anthu enanso ambiri. Ndiponso iye ndi wofunitsitsa kuchita zimenezi. Chifukwa cha mphamvu zimene wapatsidwa monga Wolamulira, Yesu adzadalitsa anthu padziko lonse lapansi kwamuyaya kudzera mu Ufumuwo.​—Yohane 5:28, 29.

Ufumu Unali Pakati Pawo

N’zoona kuti Yesu ananena kuti: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu” ndipo mawu amenewa amapezeka pa Luka 17:21. Baibulo lina linamasulira lembali kuti: “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwanu,” ndipo lina linamasulira kuti “uli mkati mwa inu.” (Onani Baibulo la Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero ndi Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani palembali?

Nkhani yonse imasonyeza kuti Yesu ankalankhula ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda otchedwa Afarisi omwe anali anthu amakani ndiponso omva zawo zokha. Afarisi anali ndi mfundo zawo zokhudza Mesiya ndiponso Ufumu wake. Ankakhulupirira kuti Mesiya adzabwera “m’mitambo” monga Mfumu yaulemerero kudzapulumutsa Ayuda kuulamuliro wa Aroma ndi kubwezeretsa ufumu kwa Aisiraeli. (Danieli 7:13, 14) Koma Yesu anasonyeza kuti maganizo a Afarisiwo anali olakwika. Iye anawauza kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi.” Kenako anawauza kuti: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”​—Luka 17:20, 21.

Yesu ankaphunzitsa komanso kuchita zozizwitsa zimene zinasonyezeratu kuti anali Mfumu yolonjezedwa ya Ufumu umenewo. Koma Afarisi anatsutsa zoti Yesu ndi Mesiya chifukwa mitima yawo inali yoipa komanso analibe chikhulupiriro. Iwo anakayikira zoti Yesu angakhaledi Mesiya ndiponso ankatsutsa zimene iye ankanena kuti ndi Mesiya. Choncho iye anawauza mfundo yakuti: Ufumu, umene iye ankayembekezera kudzakhala Mfumu yake, unali ‘pakati pawo.’ Iye sanawauze kuti Ufumuwo uli mu mtima mwawo. * Yesu ndi ophunzira ake anali pakati pa anthuwo. N’chifukwa chake anawauza kuti: “Ufumu wa Mulungu muli nawo pomwe pano.”​—Luka 17:21, Contemporary English Version.

Muziona Kuti Ufumu Ndi Wofunika Kwambiri

Ngakhale kuti Ufumu wa Mulungu sungakhale m’mitima ya anthu ochimwa, tiyenera kuona kuti Ufumuwo ndi wofunika kwambiri. Mwa kuphunzitsa komanso kuchita zozizwitsa, Yesu anayesetsa kuthandiza anthu kukhulupirira kwambiri boma lolungama limene lidzabweretse bata ndi mtendere weniweni. Iye ankafuna kuti iwo akhale ndi chikhulupiriro chimene chingawathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino pa moyo wawo. Ndipo iye anawaphunzitsa kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ambiri mwa anthu amene anamva mawu a Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri ndipo anakhala ndi chikhulupiriro chimene chinawathandiza kuti ayambe kutsatira Yesu. Iwo anachita zimenezi n’cholinga chakuti adzapeze madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse.

Kodi nanunso mumafuna mutakhala ndi chikhulupiriro ngati chimenechi? Ndiye kodi mungatani kuti mukhale nacho? Kumbukirani mawu oyamba amene Yesu ananena pa ulaliki wake wa paphiri. Iye anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” (Mateyu 5:3) Tikukupemphani kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova amene akupatsani magazini ino. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo, m’malo mokhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu umangotanthauza kusintha kumene munthu amachita mumtima mwake. Zingakuthandizeninso kuyamba kukhulupirira kuti Ufumuwo ndi ulamuliro wabwino komanso wolungama ndipo udzabweretsa bata ndi mtendere kwa anthu onse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Popeza kuti Yesu ankalankhula ndi Afarisi, n’zodziwikiratu kuti iye sankatanthauza kuti Afarisiwo anasintha n’kukhala anthu a mitima yabwino.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Kodi Ufumu wa Mulungu unali m’mitima ya anthu achinyengo komanso opha anthu amene ankatsutsa Yesu?