Ulosi wa 6: Ntchito Yolalikira Ikuchitika Padziko Lonse
Ulosi wa 6: Ntchito Yolalikira Ikuchitika Padziko Lonse
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—MATEYU 24:14.
● Vaiatea amakhala pachilumba chinachake chimene chili m’nyanja ya Pacific, chomwe ndi chimodzi mwa zilumba zotchedwa Tuamotu Archipelago. Dera la Tuamotu lili ndi zilumba pafupifupi 80 ndipo zilumba zimenezi zili m’dera lalikulu pafupifupi mahekitala 8.3 miliyoni. Komabe kudera limeneli kumakhala anthu 16,000 basi. Ngakhale kuti Vaiatea ndi anthu amene amakhala nawo pafupi ali kudera lakutali limeneli, iwo analalikidwapo ndi Mboni za Yehova. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Chifukwa chakuti a Mboni za Yehova amayesetsa kulalikira uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu kwa anthu onse ngakhale anthuwo atakhala kuti amakhala kudera lakutali.
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse lapansi. M’chaka cha 2010 chokha, a Mboni za Yehova anatha maola 1.6 biliyoni akulalikira uthenga wabwino m’mayiko 236. Pamenepa ndiye kuti pa avereji, wa Mboni za Yehova aliyense tsiku lililonse ankatha mphindi 30 akulalikira. Pa zaka 10 zapitazi a Mboni za Yehova anatulutsa ndiponso kugawira zinthu zoposa 20 biliyoni zothandiza anthu kuphunzira Baibulo.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Uthenga wa m’Baibulo sunayambe lero kulalikidwa. Uthengawu wakhala ukulalikidwa kwa zaka zambirimbiri.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? N’zoona kuti anthu ambiri akhala akulalikira zinthu zina zokhudza uthenga wa m’Baibulo. Komabe ambiri mwa anthu amenewa anangolalikira kwa nthawi yochepa ndiponso kudera lochepa basi. Koma a Mboni za Yehova akugwira ntchito imeneyi mwadongosolo ndipo akulalikira kwa anthu ambiri padziko lonse lapansi. Iwo akupitirizabe kugwira ntchito yawo yolalikira ngakhale kuti kwa zaka zambiri akhala akutsutsidwa ndi magulu amphamvu komanso ankhanza kwambiri. * (Maliko 13:13) Kuwonjezera pamenepa, a Mboni za Yehova salipidwa pa ntchito yawo yolalikira. M’malomwake iwo amangodzipereka kugwira ntchitoyo ndipo amapatsa anthu mabuku awo kwaulere. Ntchito yawo imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi si zoona kuti ‘uthenga wabwino wa ufumu’ ukulalikidwa padziko lonse lapansi? Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu sikukusonyeza kuti posachedwa padzikoli pachitika zinthu zabwino?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri, onerani mavidiyo achingelezi awa ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova: “Faithful Under Trials,” “Purple Triangles” ndi “Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault.”
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Yehova akalola, ife tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama pogwiritsa ntchito njira iliyonse imene ingathandize kuti anthu amve uthenga wathu.”—2010 YEARBOOK OF JEHOVAH’S WITNESSES.