Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Ayenera Kuphunzitsa Ana Zokhudza Mulungu?

Kodi Ndani Ayenera Kuphunzitsa Ana Zokhudza Mulungu?

Kodi Ndani Ayenera Kuphunzitsa Ana Zokhudza Mulungu?

“Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.”​—LUKA 6:40.

MAKOLO ena amaona kuti sangakwanitse kuphunzitsa ana awo zinthu zokhudza Mulungu. Iwo amaganiza kuti sangaphunzitse bwino ana awo chifukwa iwowo sanaphunzire mokwanira kapenanso sadziwa zambiri pa nkhani zachipembedzo. Choncho makolo amenewa amasiyira wachibale kapena mtsogoleri wachipembedzo ntchito yofunika kwambiri imeneyi.

Koma kodi ndani ayenera kuphunzitsa ana mfundo zachipembedzo komanso za makhalidwe abwino? Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi, ndipo yerekezerani zimenezi ndi zimene akatswiri ofufuza zinthu apeza.

Kodi Bambo Ali Ndi Udindo Wotani?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”​—Aefeso 6:4.

Zimene ofufuza apeza: Kodi abambo amapindula bwanji ngati amakonda kwambiri zinthu zachipembedzo? Nkhani ina, yomwe inalembedwa mu 2009, inati: “Bambo amene amakonda kupembedza, amakhala bambo wabwino chifukwa munthu amene ali ndi chipembedzo amakhala ndi anzake omuthandiza pa zinthu zosiyanasiyana m’moyo ndiponso amakhala ndi mfundo zomuthandiza kukhala ndi khalidwe labwino.”​—Fathers’ Religious Involvement and Early Childhood Behavior.

Baibulo limatsindika kwambiri kufunika kwa udindo umene bambo ali nawo polera ndiponso kuphunzitsa ana. (Miyambo 4:1; Akolose 3:21; Aheberi 12:9) Koma kodi malangizo a m’Baibulo amenewo, onena za udindo wa bambo, akugwirabe ntchito masiku ano? Mu 2009, yunivesite ya Florida inafalitsa nkhani yomwe inafotokoza mmene zochita za abambo zimakhudzira ana awo. Atachita kafukufuku anapeza kuti abambo akamatha nthawi yaitali ali ndi ana awo, anawo amakhala achifundo ndiponso amadziona kuti ndi ofunika. Anyamata ambiri amene amaleredwa moteremu amakhala ndi khalidwe labwino ndipo atsikana ambiri amakhala oganiza bwino. Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti malangizo a m’Baibulo pa nkhani yolera ana akugwirabe ntchito masiku ano.

Kodi Udindo wa Mayi Ndi Wofunika Bwanji?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Usasiye malamulo a mayi ako.”​Miyambo 1:8.

Zimene ofufuza apeza: Mu 2006, buku lina linanena kuti m’mayiko ambiri, amayi ndi amene nthawi zambiri amacheza kwambiri ndi ana awo ang’onoang’ono komanso kuchita nawo zinthu limodzi. (Handbook of Child Psychology) Chifukwa chakuti amayi amatha nthawi yaitali chonchi ali ndi ana awo, zolankhula zawo, zochita zawo ndiponso mmene amaonera zinthu zimakhudza kwambiri kakulidwe ka ana awowo.

Mayi ndi bambo akamachita zinthu mogwirizana pophunzitsa ana awo choonadi cha Mulungu, amakhala kuti akuwapatsa ana awowo mphatso ziwiri zamtengo wapatali. Choyamba, amakhala kuti akuwathandiza anawo kupanga ubwenzi ndi Atate wawo wakumwamba ndipo ubwenzi umenewu ungawathandize moyo wawo wonse. Chachiwiri, anawo amaphunzira kuchokera ku chitsanzo cha makolo awo, zimene mwamuna ndi mkazi wake angachite kuti akwaniritse zolinga zofunika kwambiri. (Akolose 3:18-20) Ngakhale kuti anthu ena angathandize mayi ndi bambo kulera ana, ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana awo za Mulungu ndiponso kuwaphunzitsa zimene Mulungu amafuna kuti banja lizichita n’cholinga choti liziyenda bwino.

Ndiyeno kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo? Kodi njira zabwino kwambiri zowaphunzitsira ndi ziti?