Masoka Achilengedwe Adzatha
NGATI munthu wina atakuuzani kuti, “Posachedwapa, masoka achilengedwe adzatha,” kodi mungatani? Mwina mungamuuze kuti, “Inutu simukudziwa chimene mukunena, chifukwa masoka achilengedwe angokhala mbali ya moyo tsopano.” Kapena mwina mungangoganiza mumtima mwanu kuti, ‘Kodi iyeyu akuona ngati akunamiza mwana eti?’
Ngakhale kuti masoka achilengedwe amaoneka ngati sadzatha, pali zifukwa zomveka zoyembekezera kuti zinthu zidzasintha. Koma sikuti anthu ndi amene adzasinthe zinthuzo. Anthu samvetsa bwino zifukwa zimene zimachititsa kuti masoka achilengedwe azichitika, ndiponso momwe masokawo amachitikira. Ndipo sangathe kulamulira kapena kusintha zinthu zimenezi. Mfumu Solomo ya ku Isiraeli, yomwe inali yotchuka chifukwa chomvetsa bwino zinthu ndiponso chifukwa cha nzeru zake, inalemba kuti: “Anthu amalephera kudziwa ntchito imene yachitika padziko lapansi pano. Kaya anthu ayesetse bwanji kuifufuza, safika poidziwa. Ngakhale atanena kuti ali ndi nzeru zokwanira zodziwira zinthu, sangathe kuidziwa.”—Mlaliki 8:17.
Ngati anthu sangathe kuletsa masoka achilengedwe, kodi ndani angathe? Baibulo limafotokoza kuti Mlengi wathu ndi amene adzachite zimenezi. Iye ndi amene anakhazikitsa ndondomeko zosiyanasiyana zachilengedwe zimene zimachitika padzikoli, monga kayendedwe ka madzi amene amasintha n’kukhala nthunzi, mitambo, kenako mvula. (Mlaliki 1:7) Ndipo mosiyana kwambiri ndi anthu, Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire zimene angathe kuzigwiritsa ntchito. Potsimikizira mfundo imeneyi, mneneri Yeremiya anati: “Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu yanu ndi dzanja lanu lotambasula. Nkhaniyi si yovuta kwa inu.” (Yeremiya 32:17) Popeza Mulungu analenga dziko lapansi komanso zinthu zonse zimene zili mmenemo, m’pomveka kuti akudziwa mmene angayendetsere zinthu m’njira yoti anthu azikhala padzikoli mwamtendere ndiponso motetezeka.—Salimo 37:11; 115:16.
Koma kodi Mulungu adzasintha bwanji zinthu? Mungakumbukire kuti nkhani yachiwiri ija inafotokoza kuti zinthu zambiri zoopsa zimene zikuchitika padzikoli masiku ano zikupanga “chizindikiro” chosonyeza kuti tili m’nyengo ya “mapeto a nthawi ino.” Yesu anafotokoza kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” (Mateyu 24:3; Luka 21:31) Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lakumwamba la Mulungu, udzasintha zinthu kwambiri padzikoli, ndipo udzachititsa kuti mphamvu za m’chilengedwe zisamayambitse masoka. Ngakhale kuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zoti angachite yekha zimenezi, iye anapereka udindo umenewu kwa Mwana wake. Mneneri Danieli anafotokoza za Mwana ameneyu kuti: “Anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.”—Danieli 7:14.
Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, wapatsidwa mphamvu zomuthandiza kusintha zinthu n’cholinga choti dzikoli likhale malo abwino kwambiri. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo pamene Yesu anali padziko lapansi, anatipatsa chitsanzo chosonyeza kuti angathe kulamulira mphamvu za m’chilengedwe. Pa nthawi ina pamene anali ndi ophunzira ake m’ngalawa panyanja ya Galileya, “kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba ngalawayo, mwakuti ngalawayo inangotsala pang’ono kumira.” Ophunzira ake anachita mantha kwambiri. Poopa kuti akhoza kufa, iwo anapempha Yesu kuti awathandize. Kodi Yesu anatani? Iye anangodzudzula “mphepoyo ndi kuuza nyanjayo kuti: ‘Leka! Khala bata!’ Chotero mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.” Zitatero, ophunzira akewo anadabwa kwambiri ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, chifukwa ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera?”—Maliko 4:37-41.
Zimenezi zinachitika kalekale ndipo panopa Yesu anakwezedwa kumwamba n’kupatsidwa mphamvu ndi udindo waukulu. Popeza iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo wapatsidwa udindo waukulu, adzasintha zinthu n’cholinga choti anthu azikhala mwamtendere ndiponso motetezeka padzikoli.
Komabe, monga mmene taonera, anthu ndi amene amayambitsa mavuto ambiri ndiponso masoka. Iwo amayambitsa kapena kulimbikitsa mavuto amenewa chifukwa cha mtima wodzikonda ndiponso wadyera. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kwa anthu amene akupitirizabe kusonyeza mtima umenewu ndipo safuna kusintha? Baibulo limanena kuti Ambuye Yesu akadzabwera “kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu m’moto walawilawi, . . . pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango kwa anthu osadziwa Mulungu ndi kwa anthu osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.” Zoonadi, iye ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’—2 Atesalonika 1:7, 8; Chivumbulutso 11:18.
Kenako Yesu Khristu, yemwe ndi “Mfumu ya mafumu,” adzachititsa kuti mphamvu zonse za m’chilengedwechi zisadzayambitsenso masoka. (Chivumbulutso 19:16) Iye adzaonetsetsa kuti nzika za Ufumu wa Mulungu sizikuvutikanso ndi masoka achilengedwe. Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake poyendetsa zinthu za m’chilengedwechi n’cholinga choti nyengo izisintha bwinobwino mokomera anthu. Zimenezi zikadzachitika, zomwe Yehova Mulungu analonjeza anthu ake kale kwambiri zidzakwaniritsidwa. Iye anati: “Ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake. Nthaka idzakupatsani chakudya, ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.” (Levitiko 26:4) Anthu azidzamanga nyumba popanda nkhawa yoti mwina zingathe kuwonongeka ndi masoka achilengedwe. Izi zili choncho chifukwa Baibulo limati: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—Yesaya 65:21.
Kodi Inuyo Muyenera Kuchita Chiyani?
Mofanana ndi anthu ambiri, n’zosakayikitsa kuti inunso mukufunitsitsa kudzakhala m’dziko limene simudzakhala masoka alionse. Koma kodi mungatani kuti mudzakhalemo? “Anthu osadziwa Mulungu” komanso “anthu osamvera uthenga wabwino” sadzakhala nawo m’dziko lomwe likubweralo, momwe simudzakhala masoka achilengedwe. Choncho, n’zoonekeratu kuti munthu amene akufuna kudzakhala m’dzikolo ayenera kuphunzira za Mulungu ndi kugwirizana ndi ulamuliro wake padziko lapansili. Mulungu akufuna kuti timudziwe ndiponso timvere uthenga wabwino wonena za Ufumu umene iye waukhazikitsa kudzera mwa Mwana wake.
Njira yabwino kwambiri yodziwira zimenezi, n’kuphunzira Baibulo mosamala kwambiri. Izi zili choncho chifukwa Baibulo lili ndi malangizo amene angathandize munthu kuti ayenerere kudzakhala nawo m’dziko lopanda masoka achilengedwe mu Ufumu wa Mulungu. Bwanji osapempha a Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kuphunzira zimene Baibulo limanena? Iwo ndi okonzeka kuphunzira nanu Baibulo. Ndipotu chinthu chimodzi chotsimikizirika, chomwe chingachitike ngati mutaikirapo mtima kuti mudziwe Mulungu ndi kumvera uthenga wabwino, n’choti mawu a pa Miyambo 1:33 adzakwaniritsidwa pa inu. Lembali limati: “Koma munthu wondimvera adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”