Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzachitika Liti?
Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzachitika Liti?
“Nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse. . . Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu.”—CHIVUMBULUTSO 7:9, 14.
ZIMENE zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti nkhondo ya Aramagedo yangotsala pang’ono kuyamba. N’chifukwa chiyani tikutero?
Panopa pali kale anthu omwe akutumikira Yehova komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo anthu amenewa akupezeka padziko lonse lapansi. Mulungu akuthandiza anthu amenewa, omwe ndi ochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chinenero chilichonse kuti akhale ogwirizana komanso okondana. Anthu okondana ndiponso ogwirizana chonchiwa ndi a Mboni za Yehova.—Yohane 13:35.
Posachedwapa, Satana adzasonkhanitsa magulu ake ankhondo ndipo adzaukira anthu amtendere amenewa amene amaoneka ngati alibe chitetezo. (Ezekieli 38:8-12; Chivumbulutso 16:13, 14, 16) Kodi mungatsimikize bwanji kuti zimenezi zidzachitikadi? Baibulo limatchula maulosi amene angatithandize kudziwa nthawi imene Aramagedo idzachitike. Ambiri mwa maulosi amenewa akukwaniritsidwa panopa.
Maulosi Amene Akukwaniritsidwa Panopa
Ophunzira a Yesu anamufunsa kuti anthu adzadziwa bwanji “mapeto a nthawi ino” akadzafika. (Mateyu 24:3) Poyankha zimenezi, Yesu anatchula zinthu zimene zidzachitike. Iye anati: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” Kenako iye ananenanso kuti: “Zonsezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.” (Mateyu 24:7, 8) Mtumwi Paulo anatchulanso nthawi imeneyi kuti ndi “masiku otsiriza,” ndipo ananena kuti imeneyi idzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kodi inuyo simukuona kuti maulosi amenewa akunena za zinthu zimene zikuchitika masiku ano?
N’chifukwa chiyani nthawi imeneyi ili yovuta kwambiri? Mtumwi Yohane analemba chifukwa Chivumbulutso 12:7-12) Kodi si zoona kuti anthu padziko lonse masiku ano amakhala olusa komanso okonda chiwawa?
chake. Iye analosera kuti kwa “kanthawi kochepa” Satana ndi ziwanda zake adzakhalapobe padziko lapansi. Baibulo linalosera kuti pa nthawi imeneyi Satana adzakhala “ndi mkwiyo waukulu.” (Yesu ananenanso kuti pa nthawi yovuta imeneyi, padzikoli pazidzachitika ntchito yofunika kwambiri. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu [wa Mulungu] udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Masiku ano, a Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 235, m’zinenero zoposa 500. Magazini awiri amene iwo amafalitsa, omwe ndi Nsanja ya Olonda komanso Galamukani!, amafalitsidwa kwambiri kuposa magazini ena alionse padziko lapansi. A Mboni za Yehova anamasuliranso Baibulo m’zinenero pafupifupi 100. Ntchito yawo yolalikira imagwiridwa ndi anthu ongodzipereka ndipo ndalama zolipirira ntchitoyi zimachokera pa zopereka zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ntchito yolalikira imene iwo amagwirayi ikukwaniritsa ulosi wa Yesu.
Baibulo limanenanso za zinthu zimene zidzayambitse nkhondo ya pakati pa Yehova Mulungu ndi anthu amene amamutsutsa. Taonani maulosi atatu awa amene akwaniritsidwe posachedwapa.
Maulosi Amene Akwaniritsidwe Posachedwapa
Ulosi Woyamba. Baibulo limanena kuti maboma a anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” Pa nthawi imeneyo, iwo adzaganiza kuti atsala pang’ono kuthetseratu mavuto akuluakulu m’dzikoli. Komabe, zotsatira zake sudzakhala mtendere ngati mmene iwo amaganizira.—1 Atesalonika 5:1-3.
Ulosi Wachiwiri: Kenako, maboma ambiri adzaganiza zothetsa magulu azipembedzo m’dzikoli. M’Baibulo maboma amenewa amaimiridwa ndi chilombo, ndipo zipembedzo zonyenga zimaimiridwa ndi mkazi amene wakwera pamsana pa chilombocho. (Chivumbulutso 17:3, 15-18) Chilombo chophiphiritsa chimenechi chidzawononga zipembedzo zonse zomwe zimanamizira kuti zimaimira Mulungu ndipo Mulungu ndi amene adzachititse kuti chilombochi chichite zimenezi.
Mtumwi Yohane anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa pofotokoza zimene zidzachitikezi. Iye anati: “Nyanga 10 waziona zija, komanso chilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto. Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake.”—Chivumbulutso 17:16, 17.
Ulosi Wachitatu: Satana akadzaona kuti wakwanitsa kuwononga chipembedzo chonyenga, adzachititsanso kuti maboma aukire anthu amene amalambira Yehova Mulungu.—Chivumbulutso 7:14; Mateyu 24:21.
Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?
Ngati inuyo simunaphunzirepo Baibulo bwinobwino, zingakuvuteni kukhulupirira kuti zinthu zimene tafotokozazi zidzachitikadi. Koma pali chifukwa chomveka chokhulupirira kuti maulosi onse adzakwaniritsidwa ndipo zinthu zimene tafotokozazi zichitika posachedwapa. Umboni wa zimenezi ndi maulosi ambiri a m’Baibulo omwe akwaniritsidwa kale. *
Tikukupemphani kuti mupeze nthawi yophunzira ndi a Mboni za Yehova kuti mudziwe chifukwa chake iwo amakhulupirira kuti ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ ili pafupi komanso chifukwa chake simuyenera kuopa nkhondo imeneyi. Mukambirane nawo kuchokera m’Baibulo zimene muyenera kuchita kuti mukhale m’gulu la anthu amene Yehova Mulungu amawateteza. (Chivumbulutso 16:14) Zimene mungaphunzirezo zingakuthandizeni kuti musamaope zimene zidzachitike m’tsogolo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Kuti mupeze umboni wakuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa, werengani mutu 2 ndi 9 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Ntchito yolalikira imene a Mboni za Yehova akugwira ikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo