Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Angayankhe Bwanji Funso Limeneli?

Kodi Yesu Angayankhe Bwanji Funso Limeneli?

Kodi Yesu Angayankhe Bwanji Funso Limeneli?

Anthu ambiri opemphera amaona kuti chipembedzo ndi ndale ziyenera kuyendera limodzi. Iwo amakhulupirira kuti chipembedzo chingathandize kwambiri pothetsa mavuto a anthu. Komabe, palinso anthu ena opemphera amene amaona kuti chipembedzo ndi ndale ndi zinthu zosiyana ndipo siziyenera kuyendera limodzi. Kodi inuyo panokha mumaona kuti ndi bwino kuti chipembedzo chizithandizira nawo pa ndale? Kodi chipembedzo ndi ndale ziyenera kuyendera limodzi?

MUNTHU wina ananena kuti zimene Yesu Khristu “anaphunzitsa zimakhudza maganizo a anthu ambiri pa nkhani ya chipembedzo.” Ndiye zikanakhala zotheka kumufunsa Yesu kuti, Kodi chipembedzo ndi ndale ziyenera kuyendera limodzi? Kodi mukuganiza kuti akanayankha kuti chiyani? Iye ali padziko lapansi, anayankha funso limeneli mwa mawu komanso zochita zake. Mwachitsanzo, mu ulaliki wake wotchuka wa paphiri, Yesu anapereka mfundo zimene zingathandize otsatira ake kudziwa zimene ayenera kuchita pa nkhaniyi. Tiyeni tikambirane mfundo zina za mu ulaliki wotchuka umenewu.

Akhristu Ayenera Kuchitira Ena Zabwino

Yesu anafotokoza khalidwe limene otsatira ake ayenera kusonyeza kwa anthu ena. Iye anati: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja kumene anthu akaupondaponda. Inu ndinu kuwala kwa dziko. . . . Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:13-16) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ophunzira ake ali ngati mchere komanso kuwala?

Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti otsatira ake ali ngati mchere, osati kwa kagulu kochepa ka anthu, koma kwa anthu onse. Akusonyezanso kuti iwo ali ngati kuwala, osati kwa anthu ochepa, koma kwa onse ofuna kuona zinthu bwinobwino. Pogwiritsa ntchito mawu amenewa Yesu anasonyeza kuti sankafuna kuti ophunzira ake azikhala kwaokha. Kodi tikutero chifukwa chiyani?

Taganizirani izi: Kuti mchere uthandize kuti zakudya zisawonongeke, uyenera kusakanizidwa ndi zakudyazo. Komanso nyale singathandize kuti m’chipinda muwale ngati nyaleyo sinaikidwe m’chipindacho. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu sanalamule ophunzira ake kuti asamuke n’kukakhala kwaokhaokha. Komanso iye sanauze ophunzira ake kuti azipeweratu kuchita zinthu ndi anthu a m’dera lawo. M’malomwake, mofanana ndi mmene mchere umayenera kusakanizidwa ndi chakudya ndiponso mmene nyale imafunikira kuikidwa mu mdima, Akhristu amayenera kuchita zinthu ndi anthu ena.

“Sali Mbali ya Dziko”

Komabe, malangizo a Yesu oti otsatira ake azichita zinthu ndi ena akutipangitsa kukhala ndi funso lofunika kwambiri lokhudza zimene Akhristu ayenera kuchita pa nkhani ya ndale. Tikutero chifukwa Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa, anapempherera otsatira ake kuti: “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16) Komano kodi zingatheke bwanji kuti Akhristu asakhale mbali ya dziko koma n’kumachitira limodzi zinthu zina ndi anthu a m’dera lawo? Kuti tipeze yankho la funso limeneli, tiyeni tikambirane mafunso enanso atatu awa:

• Kodi Yesu ankachita nawo ndale?

• Kodi Akhristu ayenera kulowerera ndale?

• Kodi zimene Akhristu amaphunzitsa zimathandiza bwanji anthu a m’dera lawo?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Yesu anasonyeza kuti sankafuna kuti ophunzira ake azikhala kwaokha