‘Tetezani Mtima Wanu’
‘Tetezani Mtima Wanu’
Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova
MUTU WA LACHISANU
“Yehova Amaona Mmene Mtima Ulili”—1 SAMUELI 16:7.
MUTU WA LOWERUKA
“Pakamwa Pamalankhula Zosefukira Mumtima”—MATEYU 12:34.
MUTU WA LAMLUNGU
‘M’tumikireni Yehova Ndi Mtima Wathunthu’—1 MBIRI 28:9.
Baibulo limatchula mtima pafupifupi ka 1,000. Kawirikawiri Malemba akamanena za mtima, amanena mtima wophiphiritsira osati weniweni. Kodi mtima wophiphiritsira umenewu ndi chiyani? Nthawi zambiri mawu amenewa amatanthauza zimene munthu amaganiza, mmene amamvera komanso zimene amalakalaka.
N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza mtima wathu wophiphiritsira? Mulungu anauzira Mfumu Solomo kulemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) Kuti tikhale ndi moyo wabwino panopo komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo zimadalira mmene mtima wathu wophiphiritsira ulili. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Mulungu akafuna kudziwa kuti ndife munthu wotani amayang’ana “munthu wobisika wamumtima” kapena kuti zimene zili mumtima mwathu.—1 Petulo 3:4.
Ndiyeno kodi tingateteze bwanji mtima wathu? Funso limeneli lidzayankhidwa pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova. Msonkhano umenewu udzachitika padziko lonse lapansi kuyambira kumayambiriro a mwezi uno. Mukuitanidwa kuti mudzapezeke pa msonkhano umenewu kwa masiku onse atatu. * Zimene mudzaphunzire pa msonkhanowu zidzakuthandizani kuti muzichita zinthu zomwe zingakondweretse mtima wa Yehova Mulungu.—Miyambo 27:11.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Kuti mudziwe malo a kufupi ndi kwanu amene msonkhanowu udzachitikire, onani pa Intaneti pa adiresi iyi: www.dan124.com/ny. Mungathenso kufunsa Mboni za Yehova za m’dera lanu kapena lemberani kalata kwa amene amafalitsa magazini ino.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Photo on right: Aus dem Fundus der MÜNCHNER OLYMPIAPARK GMBH, München