“Mukamapemphera Muzinena Kuti, ‘Atate’”
“Mukamapemphera Muzinena Kuti, ‘Atate’”
Kodi mukamva mawu oti “Atate” mumakumbukira chiyani? Kodi mumaganizira za bambo wachikondi amene amaganizira kwambiri za banja lake? Kapena mumaganizira za bambo amene sasamalira banja lake komanso wankhanza? Zimene mungaganize zingatengere zimene bambo anu ankachita.
NTHAWI zambiri Yesu ankagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate” akamalankhula ndi Mulungu komanso akamafotokozera ena za Mulunguyo. * Pamene ankaphunzitsa otsatira ake kupemphera, Yesu anati: “Mukamapemphera muzinena kuti, ‘Atate.’” (Luka 11:2) Koma kodi Yehova ndi Atate wotani? Yankho la funsoli ndi lofunika kwambiri chifukwa tikadziwa kuti Yehova ndi atate wotani, ubwenzi wathu ndi iye umalimba komanso timayamba kumukonda kwambiri.
Palibe amene angatifotokozere momveka bwino za Atate wathu wakumwamba kuposa Yesu. Zili choncho chifukwa chakuti iye Mateyu 11:27) Choncho Yesu ndi amene angatithandize kuti tidziwe bwino Mulungu.
anakhala limodzi ndi Atate wake kwa nthawi yaitali. Yesu ananena kuti: “Palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.” (Ndiyeno kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu zokhudza Atate wathu wakumwamba? Taganizirani mawu awa amene Yesu ananena: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mawu amenewa akusonyeza khalidwe lalikulu la Atate wathu wakumwamba, lomwe ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Yehova amasonyeza kuti amatikonda mwa kusonyeza kuti amasangalala ndi zochita zathu, kutisonyeza chifundo, kutiteteza, kutilangiza, ndiponso kutipatsa zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu.
Atate Amasangalala ndi Zochita Zathu
Ana amalimbikitsidwa akadziwa kuti makolo awo akusangalala ndi zochita zawo. Taganizirani mmene Yesu analimbikitsidwira atamva Atate wake akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mateyu 3:17) Yesu anatitsimikizira kuti Atate amatikonda komanso amasangalala nafe. Iye anati: “Wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso.” (Yohane 14:21) Mawu amenewatu ndi olimbikitsa kwambiri. Komabe Satana amafuna kuti tiziona ngati Mulungu sakusangalala nafe.
Satana amafuna kuti tizikayikira zoti Atate wathu wakumwamba akusangalala nafe. Iye amafuna kuti tiziganiza kuti Mulungu sangatikonde. Satana amachita zimenezi makamaka akaona kuti tafooka kapena tili ndi mavuto ena monga ukalamba, matenda komanso tikakhala kuti takhumudwa ndi zinazake. Taganizirani za mnyamata wina dzina lake Lucas yemwe ankaona ngati Mulungu sangamukonde. Lucas ananena kuti ali mwana, makolo ake anasintha n’kuyamba kuchita zinthu zosiyana ndi zimene ankamuphunzitsa. N’kutheka kuti zimenezi n’zimene zinamuchititsa kuti aziona kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Atate wakumwamba. Komanso popeza Lucas anali wopupuluma, nthawi zambiri ankavutika kuchita zinthu ndi anthu ena. Komabe mkazi wake, yemwe iye amaona kuti ndi dalitso lochokera kwa Mulungu, anamuthandiza kusintha khalidwe lakeli. Lucas anazindikira kuti “Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa.” (1 Timoteyo 1:15) Iye ananena kuti kuganizira kwambiri zoti Mulungu amamukonda komanso amasangalala naye, kunamuthandiza kukhala wosangalala komanso kuyamba kudziona kuti ndi wofunika.
Ngati nthawi zina mumakayikira zoti Yehova amakukondani kapena amasangalala ndi zimene mumachita, mungalimbikitsidwe mutawerenga ndi kusinkhasinkha lemba la Aroma 8:31-39. Palembali mtumwi Paulo anatitsimikizira kuti palibe chimene chingathe “kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” *
Atate Wachifundo Chachikulu
Atate wathu wakumwamba amakhudzidwa tikamavutika. Iye ndi Mulungu ‘wachifundo chachikulu.’ (Luka 1:78) Zimene Yesu ankachita zinasonyeza kuti Atate wake ndi wachifundo kwa anthu opanda ungwiro. (Maliko 1:40-42; 6:30-34) Nawonso Akhristu oona amayesetsa kutsanzira chifundo cha Atate wakumwamba. Iwo amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘tizikhala okomerana mtima ndiponso achifundo chachikulu.’—Aefeso 4:32.
Tiyeni tione zimene zinachitikira bambo wina dzina lake Felipe. Tsiku lina akupita kuntchito, anangomva ululu kumsana ngati wabaidwa ndi mpeni. Anthu anathamangira naye kuchipatala. Atamuyeza kwa maola 8, madokotala anapeza kuti mtsempha wake waukulu wotenga magazi kuchokera ku mtima waduka. Madokotalawo ananena kuti iye amwalira pakangotha mphindi 25, choncho palibe chifukwa chom’pangira opaleshoni.
Pa nthawi imene ankamuuza zimenezi anthu ena amene amapemphera naye limodzi analinso pomwepo ndipo chifukwa cha chifundo
anaganiza zoyesa njira ina. Mwamsanga anakonza zopita naye kuchipatala china komwe anam’panga opaleshoni mwamsangamsanga ndipo anzake aja anamudikirira pa nthawi yonse ya opaleshoniyi. Mwamwayi, Felipe anachira. Akakumbukira zimene zinamuchitikirazi, Felipe amayamikira kwambiri chifundo chimene anzakewo anamusonyeza. Komabe iye amakhulupirira kuti Atate wakumwamba ndi amene anachititsa kuti anzakewo amusonyeze chifundo choterechi. Felipe anati: “Ndinkangoona ngati Mulungu ali pambali panga n’kumandilimbikitsa ngati mmene Atate wachikondi amachitira.” Zimenezi zikusonyezeratu kuti nthawi zambiri Yehova amagwiritsa ntchito atumiki ake padziko lapansi kusonyeza chifundo chake.Atate Wathu Amatiteteza
Mwana akaona zinthu zoopsa amathawira kwa bambo ake. Bambo akewo akamugwira dzanja, iye amaona kuti ndi wotetezeka. Yesu nayenso ankakhulupirira kuti Yehova ndi amene angamuteteze. (Mateyu 26:53; Yohane 17:15) Nafenso tingatetezedwe ndi Atate wathu wakumwamba. Koma chitetezo chimene Yehova amapereka masiku ano, nthawi zambiri chimakhala chauzimu. M’mawu ena tingati iye amatiteteza ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kudzera m’malangizo a m’Baibulo. Tikalandira malangizo amenewa zimakhala ngati Yehova akuyenda m’mbuyo mwathu n’kumatiuza kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”—Yesaya 30:21.
Taganizirani chitsanzo cha mnyamata wina dzina lake Tiago komanso azichimwene ake Fernando ndi Rafael, omwe anali m’bandi ina yoimba nyimbo zolimbikitsa chiwawa. Iwo anasangalala kwambiri atasankhidwa kuti akaimbe nawo m’holo ina yotchuka kwambiri mumzinda wa São Paulo, ku Brazil chifukwa anaona kuti umenewu ndi mwayi waukulu. Komabe munthu wina amene amapemphera naye anawachenjeza za kuopsa kocheza ndi anthu akhalidwe loipa. (Miyambo 13:20) Pofuna kuwathandiza kumvetsa kuopsa kwa zimenezi, anawafotokozera zimene zinachitikira mchimwene wake. Mchimwene wakeyo anachita tchimo linalake chifukwa chocheza ndi anthu olakwika. Tiago ndi azichimwene ake anaganiza zosiya kuimba ndipo panopa akutumikira Mulungu nthawi zonse. Iwo amakhulupirira kuti kumvera malangizo a m’Mawu a Mulungu kunawateteza ku zinthu zimene zikanawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu.
Atate Wathu Wakumwamba Amatilangiza
Bambo wachikondi amalangiza ana ake chifukwa amafuna kuti anawo akadzakula adzakhale anthu odalirika. (Aefeso 6:4) Bambo wotereyu amaonetsetsa kuti ana ake akutsatira malangizo komabe sachita zimenezi mwankhanza. Mofanana ndi bambo wotere, nthawi zina Atate wathu wakumwamba angaone kuti tikufunika kulangizidwa. Koma nthawi zonse Mulungu amatilangiza mwachikondi ndipo satichitira nkhanza. Mofanana ndi Atate wake, Yesu sanali wankhanza, ngakhale pamene ophunzira ake ankachedwa kuyamba kutsatira malangizo amene anawapatsa.—Mateyu 20:20-28; Luka 22:24-30.
Taonani zimene zinachitikira mnyamata wina dzina lake Ricardo zomwe zinam’thandiza kuzindikira kuti Yehova anamulangiza mwachikondi. Bambo ake a Ricardo anamuthawa iye ali ndi miyezi 7. Atapitirira zaka 13 Ricardo anayamba kulakalaka chikondi cha bambo ake. Iye anayamba kuchita makhalidwe oipa ndipo chikumbumtima chake chinkamuvutitsa. Ataona kuti zimene ankachitazi zinali zosagwirizana ndi mfundo zachikhristu, anapempha akulu a mu mpingo mwawo kuti amuthandize. Akuluwo anamupatsa malangizo amphamvu a m’Baibulo koma anachita zimenezi mwachikondi. Ricardo anatsatira malangizowo komabe ankasowa mtendere chifukwa cha zoipa zimene anachita moti nthawi zina ankalephera kugona, ankalira komanso ankavutika maganizo. Pomalizira pake iye anazindikira kuti malangizo amene analandirawo unali umboni wakuti Yehova amamukonda. Ricardo anakumbukira lemba la Aheberi 12:6 limene limati: “Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.”
Ndi bwino kukumbukira kuti kulanga munthu amene wachita zoipa sikumangotanthauza kukhaulitsa kapena kudzudzula mwamphamvu. Baibulo likamanena za kulanga limatanthauzanso kuphunzitsa. Choncho Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi, nthawi zina amalola kuti tikumane ndi zotsatira zoipa za zochita zathu. Baibulo limasonyeza kuti zimenezi zimathandiza kuti tiphunzirepo kanthu n’kuyamba kuchita zoyenera. (Aheberi 12:7, 11) Atate wathu wakumwamba amatifunira zabwino ndipo amatilangiza n’cholinga chakuti zinthu zitiyendere bwino.
Atate Wathu Amatipatsa Zofunika pa Moyo
Bambo wachikondi amayesetsa kupezera banja lake zinthu zofunika pa moyo. Yehova amachitanso chimodzimodzi. Yesu ananena kuti: “Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” (Mateyu 6:25-34) Yehova amatilonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5.
Mayi wina, dzina lake Nice, anazindikira kuti mawu amenewa ndi oona. Iye anasiya ntchito n’cholinga chakuti azisamalira ana ake komanso kuti azikhala ndi nthawi yokwanira yotumikira Mulungu. Koma pasanapite nthawi, mwamuna wake anachotsedwa ntchito ndipo izi zinachititsa kuti banjali lisowe mtengo wogwira. Zitatero, Nice anapemphera kwa Yehova kuti awathandize. Tsiku lotsatira, mwamuna wake anapita kumene ankagwira ntchito kuja kuti akatenge zinthu zake. Koma anadabwa kwambiri abwana ake atamuuza kuti akhoza kumulembanso ntchito chifukwa papezeka ntchito ina. Choncho tingati mwamuna wake wa Nice anangokhala lova tsiku limodzi lokha, tsiku lotsatira n’kupezanso ntchito. Nice ndi mwamuna wake anayamikira Atate wakumwamba chifukwa chowathandiza. Zimene zinawachitikirazi, zikutikumbutsa kuti Yehova saiwala atumiki ake okhulupirika.
Mmene Tingasonyezere Kuyamikira
N’zosatheka kufotokoza njira zonse zimene Atate wathu wakumwamba amasonyezera kuti ndi wachikondi. Komabe tikaganizira njira zimene takambirana m’nkhani ino, zomwe ndi kutisonyeza kuti akusangalala ndi zochita zathu, kutisonyeza chifundo, kutiteteza, kutilangiza ndiponso kutipatsa zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu, timaona kuti iye ndi Atate wabwino kwambiri.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chikondi chimene Atate wathu wakumwamba amatisonyeza? Tingachite zimenezi mwa kuyesetsa kuphunzira zambiri za iye ndiponso cholinga chake. (Yohane 17:3) Komanso tingayesetse kuti tizichita zinthu zogwirizana ndi zimene iye amafuna. (1 Yohane 5:3) Tingatsanzirenso chikondi chake posonyeza chikondi kwa ena. (1 Yohane 4:11) Tikamachita zonsezi tingasonyeze kuti timaona Yehova monga Atate wathu ndipo timayamikira kukhala ana ake.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mfundo yoti Yehova ndi Atate imatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate” kokwanira ka 65 m’Mauthenga Abwino a Mateyu, Maliko ndi Luka komanso ka 100 mu Uthenga Wabwino wa Yohane. Nayenso Paulo anatchula Mulungu kuti “Atate” maulendo 40 m’makalata ake. Yehova ndi Atate wathu chifukwa ndi amene anatipatsa moyo.
^ ndime 9 Onani mutu 24 wakuti “Palibe Chikhoza ‘Kutisiyanitsa Ife ndi Chikondi cha Mulungu’” m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Tikadziwa kuti Yehova ndi atate wotani, ubwenzi wathu ndi iye umalimba komanso timayamba kumukonda kwambiri
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Tingasonyeze kuti timaona Yehova monga Atate wathu ndipo timayamikira kukhala ana ake
[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]
YEHOVA AMASONYEZA KUTI NDI ATATE WACHIKONDI M’NJIRA ZOSIYANASIYANA
AMASANGALALA NAFE
AMATICHITIRA CHIFUNDO
AMATITETEZA
AMATILANGIZA
AMATIPATSA ZOFUNIKA PA MOYO