Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi pa Tsiku la Chiweruzo Padzachitika Zotani?

Kodi pa Tsiku la Chiweruzo Padzachitika Zotani?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Tsiku la Chiweruzo limatanthauza chiyani?

Monga tikuonera pachithunzi chili kumanjachi, anthu ambiri amaganiza kuti pa Tsiku la Chiweruzo anthu onse adzaonekera pampando wachifumu wa Mulungu ndipo adzaweruzidwa malinga ndi ntchito zimene anachita. Anthuwa amaganiza kuti ena adzalandira moyo kumwamba ndipo ena adzapita kukazunzidwa kumoto. Koma Baibulo limasonyeza kuti cholinga cha Tsiku la Chiweruzo ndi kupulumutsa anthu ku zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika padzikoli. (Salimo 96:13) Mulungu wasankha Yesu kukhala Woweruza wake amene adzabweretsa chilungamo kwa anthu.​—Werengani Yesaya 11:1-5; Machitidwe 17:31.

2. Kodi Tsiku la Chiweruzo lidzabwezeretsa bwanji chilungamo padzikoli?

Pamene munthu woyamba Adamu anachimwira Mulungu mwadala, anachititsa kuti anthu onse akhale ochimwa, azivutika komanso azifa. (Aroma 5:12) Kuti zinthu zibwererenso mmene zinalili poyamba, Yesu adzaukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira. Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti zimenezi zidzachitika pa nthawi yaulamuliro wa Yesu Khristu wa zaka 1,000.​—Werengani Chivumbulutso 20:4, 11, 12.

Anthu amene adzaukitsidwewo sadzaweruzidwa potengera zimene anachita asanamwalire, koma zimene adzachite ataukitsidwa mogwirizana ndi zimene zidzalembedwe “m’mipukutu” yomwe yatchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 20. (Aroma 6:7) Mtumwi Paulo ananena kuti anthu “olungama ndi osalungama omwe” adzaukitsidwa. Anthu amenewa adzapatsidwa mwayi wophunzira za Mulungu.​—Werengani Machitidwe 24:15.

3. Kodi pa Tsiku la Chiweruzo padzachitika zotani?

Anthu onse amene anamwalira asanaphunzire za Yehova Mulungu ndi kumutumikira, adzapatsidwa mwayi wophunzira za Yehova. Ngati iwo adzasankhe kutumikira Mulungu, ndiye kuti adzakhala kuti ‘anauka kuti alandire moyo.’ Komabe ena mwa anthu oukitsidwawo sadzafuna kuphunzira za Yehova kuti azimutumikira. Anthu oterewa adzakhala kuti ‘anauka kuti aweruzidwe.’​—Werengani Yohane 5:28, 29; Yesaya 26:10; 65:20.

Kumapeto kwa Tsiku la Chiweruzo, lomwe lidzakhale la zaka 1,000, Yehova adzabwezeretsa anthu omvera kukhalanso angwiro monga mmene Adam ndi Hava analili poyamba. (1 Akorinto 15:24-28) Chimenechitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chomwe anthu omvera ali nacho. Kenako, Mulungu adzamasula Satana Mdyerekezi kuphompho komwe adzakhala atamangidwa kwa zaka 1,000. Satana akadzamasulidwa, adzayesa anthu kuti asatumikire Yehova ndipo amene adzakane kusocheretsedwa naye adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Werengani Yesaya 25:8; Chivumbulutso 20:7-9.

4. Kodi ndi tsiku lina liti lachiweruzo limene lidzabweretsa madalitso kwa anthu?

Baibulo limatchulanso tsiku lina lachiweruzo ponena zimene zidzachitika Mulungu akamadzawononga anthu oipa padzikoli. Tsiku lachiweruzo limeneli lidzabwera modzidzimutsa monga mmene chinabwerera Chigumula cha Nowa chimene chinawononga anthu onse oipa. Kuwonongedwa kwa “anthu osaopa Mulungu,” kudzachititsa kuti padzikoli ‘pakhale chilungamo.’​—Werengani 2 Petulo 3:6, 7, 13.