Kodi Mukudziwa?
Kodi Akhristu anathawa mu Yudeya, mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe mu 70 C.E.?
“Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo.” (Luka 21:20, 21) Amenewa anali malangizo okhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu, omwe Yesu anapereka kwa ophunzira ake. Kodi pali umboni woti ophunzira akewo anamveradi malangizowa?
Patapita nthawi kuchokera pamene Yesu anamwalira, asilikali achiroma, motsogozedwa ndi Cestius Gallus, anapita ku Palesitina kukaletsa Ayuda amene ankaukira boma la Roma. Wolemba mbiri wina wachiyuda wa m’nthawi imeneyo, dzina lake Josephus, analemba zosonyeza kuti zimenezi zinachitikadi. Asilikali achiroma anazungulira mzinda wa Yerusalemu ndipo ankaoneka kuti akonzekera kulanda mzindawu. Koma mwadzidzidzi, Gallus anawalamula kuti abwerere. Malinga ndi zimene wolemba mbiri yachipembedzo wina, dzina lake Eusebius, analemba, Akhristu anaona kuti umenewu unali mwayi wawo ndipo anatuluka mu Yudeya n’kuthawira ku Pela, mzinda wamapiri wa ku Dekapoli.
Patapita zaka zingapo, mu 70 C.E., gulu lina la asilikali achiroma, lotsogoleredwa ndi Titus, linabweranso n’kuzungulira Yerusalemu, likulu la Yuda. Pa nthawiyi asilikaliwa anawononga mzinda wa Yerusalemu. Anthu amene anali mumzindawu sanathenso kutuluka ndipo ambiri anaphedwa.
Kodi “ana a aneneri” anali ndani?
Nkhani za m’Baibulo zonena za mneneri Samueli, Eliya ndi Elisa zimatchula za amuna ena omwe ankatchedwa “ana a aneneri.” Mwachitsanzo, pamene Yehova anasankha Yehu kukhala mfumu ya Isiraeli, Elisa anatuma “mmodzi wa ana a aneneri” kuti akadzoze Yehuyo.—2 Mafumu 9:1-4.
Akatswiri amaphunziro amakhulupirira kuti mawu amenewa sakunena za ana omwe bambo awo anali aneneri koma akunena za anthu amene ankakhala komanso kugwira ntchito limodzi ndi aneneri. Malinga ndi zimene inanena magazini ina (Journal of Biblical Literature), anthu amenewa “ankadzipereka kwambiri kutumikira Yahweh [Yehova] motsogoleredwa ndi mneneri yemwenso . . . ankamutenga ngati bambo awo.” (2 Mafumu 2:12) Ndipotu nkhani yonena za kudzozedwa kwa Yehu imatchula munthu amene anatumidwa ndi Elisa kuti “mtumiki wa mneneri.”—2 Mafumu 9:4.
Zikuoneka kuti “ana a aneneri” sankakhala moyo wapamwamba. Baibulo limasonyeza kuti anthu ena oterewa a m’nthawi ya Elisa anamanga okha malo awo okhala ndipo anagwiritsa ntchito nkhwangwa yobwereka. (2 Mafumu 6:1-5) Ena mwa anthu amenewa anali okwatira, chifukwa Baibulo limatchula za mkazi wina wamasiye yemwe anali mmodzi wa akazi a “ana a aneneri.” (2 Mafumu 4:1) Aisiraeli okhulupirika ankaona kuti ntchito zomwe ana a aneneri ankagwira zinali zofunika kwambiri. M’Baibulo muli nkhani imene imasonyeza kuti nthawi zina Aisiraeli okhulupirika ankapatsa chakudya ana a aneneriwa.—2 Mafumu 4:38, 42.