Funso Loyamba: Kodi Cholinga cha Moyo Wanga N’chiyani?
ROSALIND, yemwe anakulira ku England ankafunitsitsa atadziwa yankho la funso limeneli. Iye ankafunanso kudzagwira ntchito yothandiza anthu. Atamaliza sukulu, anayamba ntchito yapamwamba ndipo ankathandizanso anthu osowa pokhala komanso anthu olumala. Ngakhale kuti iye anali pa ntchito yabwino ndiponso yandalama zambiri, ananena kuti: “Kwa zaka zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengeranji anthufe? Nanga kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’”
N’chifukwa chiyani anthu amafunsa funso limeneli?
Anthufe timasiyana ndi nyama chifukwa timatha kuphunzira kuchokera ku zinthu zakale, kukonza tsogolo lathu komanso kukhala ndi cholinga pa moyo wathu.
Kodi anthu ena amayankha bwanji funsoli?
Anthu ambiri amaganiza kuti cholinga chachikulu pa moyo wawo ndi kupeza chuma komanso kutchuka chifukwa amaona kuti zimenezi zingawapangitse kuti azisangalala.
Kodi mayankho amenewa akusonyeza kuti anthu ambiri ali ndi maganizo otani?
Anthuwa amaona kuti zofuna zawo ndiye zofunika kwambiri. Kwa iwo zofuna za Mulungu si zofunika kwenikweni.
Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?
Mfumu Solomo inali ndi chuma chambiri komanso inkaona kuti inkasangalala ndi moyo, koma pamapeto pake inaona kuti zinthu zimenezi sizithandiza munthu kukhala ndi chisangalalo chenicheni. Solomo anapeza chimene chingathandize munthu kukhaladi wosangalala ndipo analemba kuti: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” (Mlaliki 12:13) Kodi tingatani kuti tizisunga malamulo a Mulungu?
Cholinga china cha Mulungu n’choti tizisangalala ndi moyo. Solomo analemba kuti: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Ineyo ndaona kuti zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.”—Mulungu amafunanso kuti tizikonda anthu a m’banja lathu ndiponso kuwasamalira. Taonani malangizo osavuta kuwatsatira komanso othandiza awa, opita kwa amuna, akazi komanso ana.
-
“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo.”—Aefeso 5:28.
-
“Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.
-
“Ananu, muzimvera makolo anu.”—Aefeso 6:1.
Ngati titatsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi, tidzakhala ndi moyo wosangalala komanso waphindu. Komabe chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kuchita ndi kuphunzira za Mlengi wathu komanso kukhala naye pa ubwenzi. Ndipotu Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tiyandikire Mulungu.’ Limatiuzanso kuti ‘iyenso adzatiyandikira.’ (Yakobo 4:8) Ngati mutachita zimene lembali likunena, mudzakhala wosangalala komanso moyo wanu udzakhala waphindu.
Rosalind, yemwe tamutchula poyamba uja, tsopano akuona kuti anapeza cholinga cha moyo. Patsamba 10 m’magazini ino, mungawerenge zimene zinachititsa kuti asinthe maganizo amene anali nawo poyamba.