Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Linagamula Kuti Munthu Ali Ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Linagamula Kuti Munthu Ali Ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali

PADZIKO lonse a Mboni za Yehova amadziwika kuti sachita nawo ndale komanso nkhondo. Iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti ayenera ‘kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo’ ndipo sayenera ‘kuphunzira nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Komabe iwo saletsa anthu kulowa usilikali. Koma kodi wa Mboni angatani ngati chikumbumtima chake sichikumulola kulowa usilikali koma m’dziko limene akukhala muli lamulo loti aliyense azilowa usilikali? Izi n’zimene zinachitikira mnyamata wina dzina lake Vahan Bayatyan.

Zimene Zinachititsa Kuti Nkhani Yake Ipite ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya

Vahan anabadwira ku Armenia mu April 1983. Mu 1996, iye ndi anthu ena a m’banja lake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo ali ndi zaka 16, anabatizidwa. Vahan ataphunzira Baibulo anaona kuti zonse zimene Yesu Khristu anaphunzitsa otsatira ake, zomwe zikuphatikizapo kusamenya nkhondo, n’zothandiza. (Mateyu 26:52) Koma pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anabatizidwa, iye anakumana ndi mayesero aakulu.

Malamulo a m’dziko la Armenia amanena kuti mnyamata aliyense akakwanitsa zaka 18, ayenera kulowa usilikali. Akakana, angathe kulandira chilango chokhala kundende zaka zitatu. Vahan ankaona kuti palibe vuto kutumikira anthu a m’dziko lake. Komabe sankafuna kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chake mogwirizana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Choncho kodi iye anachita chiyani?

M’chaka cha 2001 atangokwanitsa zaka 18, Vahan anayamba kulembera makalata akuluakulu a boma la Armenia. M’makalatamo ankafotokoza kuti kulowa usilikali n’kosagwirizana ndi chikumbumtima chake komanso zimene amakhulupirira. Iye anawauza akuluakulu a bomawa kuti angathe kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali.

Chaka chimodzi chinadutsa Vahan akupemphabe kuti akuluakulu abomawo amuganizire pa pempho lake loti asalowe usilikali. Komabe iwo sanavomereze pempho lakelo ndipo mu September 2002 anamumanga. Iye analamulidwa kuti akhale m’ndende chaka chimodzi ndi hafu. Komabe woimira boma pa mlanduwu sanakhutire ndi chigamulocho, choncho patangotha mwezi umodzi anachita apilo kukhoti lalikulu kuti amuwonjezere chilango. Woimira boma pa mlanduyu ananena kuti Vahan alibe chifukwa chomveka chokanira kulowa usilikali ndipo zimenezi zingabweretse mavuto aakulu. Choncho khoti la apilolo linawonjezeradi chilango cha Vahan ndipo anamuuza kuti akhale m’ndende zaka ziwiri ndi hafu.

Vahan anapempha khoti lalikulu kwambiri m’dzikolo kuti liunikenso mlandu wake. Koma mu January 2003 khoti lalikululi linapereka chigamulo chofanana ndi cha khoti loyamba lija. Nthawi yomweyo Vahan anamusamutsira kundende ina komwe kunali akaidi omwe anali ndi milandu yopha anthu, kugwiririra komanso kugulitsa mankhwala osokoneza bongo.

Mmene Nkhaniyi Inaweruzidwira ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya

Kuyambira mu 2001, dziko la Armenia linalowa m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya. Choncho ngati anthu ayesa makhoti onse a m’dzikoli, amakhala ndi ufulu wochita apilo mlandu wawo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Ndipo izi n’zimene Vahan anachita. M’kalata yake yochita apilo, iye ananena kuti chigamulo chimene analandira chifukwa chokana kulowa usilikali, chinali chosemphana ndi Gawo 9 la m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Iye anapempha kuti ufulu wake wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira utetezedwe pogwiritsa ntchito gawo limeneli ngakhale kuti izi zinali zisanachitikepo.

Pa October 27, 2009 Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo pa mlandu wa Vahan. Khotili linanena kuti Gawo 9 la m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya silinena kuti munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake.

Pa nthawiyi, n’kuti Vahan atatuluka kalekale kundende, atakwatira komanso ali ndi mwana. Chigamulochi chinamukhumudwitsa kwambiri Vahan. Choncho iye anali ndi ufulu wochitanso apilo nkhaniyi ku Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya kapena kungoisiya. Vahan anasankha kuchitanso apilo. Komiti Yaikuluyi imavomereza kuunikanso milandu yochepa komanso yapadera kwambiri, choncho Vahan anasangalala kwambiri atamva kuti komitiyi yavomereza pempho lake.

Pa July 7, 2011, Komiti Yaikuluyi inapereka chigamulo chake. Komitiyi ili ndi oweruza 17 ndipo 16 mwa oweruzawa anapeza kuti boma la Armenia linaphwanya ufulu wa Vahan Bayatyan pamene linamupeza ndi mlandu n’kumutsekera m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali. Woweruza mmodzi yekha, amene anatsutsana ndi chigamulochi, anali wochokera m’dziko la Armenia.

Kodi n’chifukwa chiyani chigamulochi chili chofunika kwambiri? Chifukwa chakuti aka kanali koyamba kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya livomereze kuti Gawo 9 la m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya limateteza ufulu wa munthu wokana kugwira ntchito zausilikali malingana ndi chikumbumtima chake. Choncho khotili linaona kuti m’dziko la Armenia, momwe muli ufulu wa demokalase, boma limaphwanya ufulu wa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Zimene khotili linanena zokhudza Mboni za Yehova monga anthu amene amakanitsitsa kuchita zinthu zotsutsana ndi chikhulupiriro chawo ndi zochititsa chidwi kwambiri. Khotili linati: “Motero, khoti lino silingakayikire chilichonse kuti munthu wodandaula pa mlanduwu anakana kulowa usilikali chifukwa cha zikhulupiriro za m’chipembedzo chake. Iye amatsatira kwambiri zikhulupiriro zimenezo, zomwe ndi zotsutsana kwambiri ndi kugwira ntchito zausilikali.”

Zimene Zinachitika Chigamulo Chitaperekedwa

Pa zaka zoposa 20 zapitazi, m’dziko la Armenia a Mboni za Yehova oposa 450 amene anakana kulowa usilikali anatsekeredwa m’ndende. Pa nthawi imene nkhani ino inkalembedwa, anyamata 58 a m’dzikoli anali m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali malinga ndi zimene amakhulupirira. Anyamata asanu mwa amenewa anamangidwa chigamulo chokhudza mlandu wa Vahan Bayatyan chitaperekedwa kale. * Mmodzi wa anyamatawa anapempha boma kuti litseke mlandu wake wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira koma woimira boma pa mlanduwu anakana. Pomuyankha, woimira bomayo ananena kuti: “Chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya pa mlandu wa Vahan chimene chinaperekedwa pa July 7, 2011 sitingachigwiritse ntchito pa mlandu wakowu chifukwa milanduyi ndi yosiyana.”

Kodi n’chifukwa chiyani woimira bomayu ananena zimenezi? Pa nthawi imene mlandu wa Vahan Bayatyan unkaweruzidwa, panalibe ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali zimene anthu okana kulowa usilikali akanagwira. Tsopano boma la Armenia linakhazikitsa lamulo lakuti anthu onse amene akukana kulowa usilikali angathe kumagwira ntchito zina. Komabe popeza ntchito zimenezi zimagwirizana ndi ntchito zausilikali, zimakhala zovuta kuti anthu amene akana kulowa usilikali agwire ntchitozi.

Vahan Bayatyan anasangalala ndi chigamulo cha nkhani yake ndipo zimenezi zingathandize kuti zinthu zisinthe ku Armenia. Chigamulochi chipangitsa kuti boma la Armenia lisiye kumanga anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

A Mboni za Yehova sauza boma kuti lisinthe malamulo ake. Komabe monga mmene Vahan Bayatyan anachitira, iwo amaonetsetsa kuti ufulu wawo sukuphwanyidwa mogwirizana ndi malamulo a m’mayiko awo. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Amachita zimenezi n’cholinga choti apitirize kukhala mwamtendere komanso kuti azitsatira zonse zimene Mtsogoleri wawo Yesu Khristu anawalamula.

^ ndime 17 Awiri a anyamata amenewa chigamulo chawo chinaperekedwa pa July 7, 2011, tsiku lomwenso Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula mlandu wa Vahan.