Moyo wa Anthu Akale—M’busa
“Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.”—YESAYA 40:11.
ABUSA amatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo, kungoyambira m’buku loyamba la Genesis mpaka m’buku lomaliza la Chivumbulutso. (Genesis 4:2; Chivumbulutso 12:5) Anthu otchuka monga Abulahamu, Mose ndi Mfumu Davide anali abusa. Wamasalimo Davide anafotokoza bwino zimene m’busa wabwino ankachita. Komanso salimo limene ena amati analemba ndi Asafu, limatchula Davide monga m’busa amene ankasamalira anthu a Mulungu.—Salimo 78:70-72.
M’nthawi ya Yesu, anthu ankaonabe kuti ntchito yaubusa inali yofunika kwambiri. Yesu ananena kuti iye ndi “m’busa wabwino” ndipo nthawi zambiri ankatchula za makhalidwe a m’busa wabwino pophunzitsa mfundo zofunika. (Yohane 10:2-4, 11) Baibulo limayerekezeranso Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndi “m’busa.”—Yesaya 40:10, 11; Salimo 23:1-4.
Kodi ndi ziweto ziti zimene abusa ankaweta? Ndipo kodi abusawo ankagwira bwanji ntchito yawo? Nanga tikuphunzira chiyani kuchokera kwa abusa akhama amenewa?
Nkhosa ndi Mbuzi
Kale, abusa mu Isiraeli ankaweta nkhosa zimene zina mwa izo zinkakhala ndi michira yonenepa komanso zinkakhala ndi ubweya wambiri. Mtundu wa nkhosa zimenezi unali wochokera ku Siriya. Nkhosa zamphongo za mtundu umenewu zimakhala ndi nyanga ndipo zazikazi sizikhala
nazo. Nkhosazi zimakhala zofatsa kwambiri ndiponso zomvera ndipo nthawi zonse zimadalira m’busa wawo kuti aziteteze ku zilombo.Abusa ankawetanso mbuzi. Nthawi zambiri mbuzizi zinkakhala zakuda kapena zofiirira. Zinkakhalanso ndi makutu ataliatali omwe nthawi zambiri ankakodwa m’minga ndi m’ziyangoyango zikamakwera mapiri kukadya.
Nthawi zambiri m’busa ankakhala ndi ntchito yophunzitsa nkhosa ndi mbuzi zake kuti zizimumvera. Komanso m’busa wabwino ankasamalira nkhosa ndi mbuzi zake ndipo ankatha kuzipatsa mayina kuti akamaziitana zizidziwa mosavuta.—Yohane 10:14, 16.
Zimene Abusa Ankachita
M’nyengo yoti msipu wayamba kuphuka, tsiku lililonse abusa ankapita kumalo apafupi ndi mudzi wawo kukadyetsa ziweto. Nthawi imeneyi ndi imene nkhosa komanso mbuzi zinkakonda kuswana. Pa nthawiyi abusa ankameta ubweya wa nkhosa ndipo imeneyi inkakhala nthawi ya chikondwerero.
Munthu akakhala ndi nkhosa zochepa, ankalemba ganyu m’busa yemwe ali ndi nkhosa zambiri kuti azimuwetera nkhosa zakezo. Koma nthawi zambiri m’busa waganyuyu sankasamalira nkhosa za munthuyo ngati mmene ankachitira ndi nkhosa zake.—Yohane 10:12, 13.
Anthu akamaliza kukolola m’minda yapafupi ndi mudziwo, abusa ankakadyetsa nkhosa m’mindamo ndipo zinkadya zitsamba zimene zikuphukira kumene komanso mbewu zotsalira pokolola. M’nyengo yotentha, abusa ankapita ndi ziweto zawo kumalo okwera komwe kunkakhala kozizirira bwino. Nthawi zambiri abusawa ankadyetsa nkhosa zawo kumapiri kumene kunkakhala msipu wobiriwira ndipo ankagona komweko n’kumayang’anira nkhosa zawozo. Nthawi zina m’busa ankalowetsa nkhosa zake m’phanga usiku, pofuna kuziteteza ku zilombo monga nkhandwe ndi afisi. Ziwetozo zikadzidzimutsidwa ndi kulira kwa fisi, mawu a m’busayo ankachititsa kuti zisachite mantha.
Madzulo alionse, m’busayo ankawerenga nkhosa zake komanso kuona ngati iliyonse ili bwino. M’mamawa ankaitana nkhosazo akamapita nazo kukazidyetsa ndipo zinkamutsatira. (Yohane 10:3, 4) Masana abusa ankapita ndi ziweto zawo kumtsinje kuti zikamwe madzi. Mitsinje ikauma abusa ankapita ndi nkhosazo kuzitsime komwe ankakazitungira madzi kuti zimwe.
Nyengo yotentha ikamapita kumapeto, abusa ankatenga ziweto zawo n’kupita nazo kuzigwa. Nyengo yozizira ikayamba iwo ankatenga ziwetozo n’kubwereranso kumudzi. Ankachita zimenezi poopa kuti ziwetozo zingafe chifukwa cha mvula, matalala komanso kuzizira kwambiri. Kuyambira November mpaka m’nyengo yoti msipu
wayamba kuphuka, abusa sankatulutsa ziweto zawo kupita nazo kutchire kukazidyetsa.M’busa Ankakhala Wachikwanekwane
Zovala za m’busa sizinkakhala zochita kusokedwa mwaluso. Komabe zinkakhala zokhuthala n’cholinga choti zizimuteteza ku mphepo. Abusa ankakonda kuvala chovala chopangidwa ndi chikopa cha nkhosa ndipo ankachivalira mkati. Mkati mwa chovala chimenechi ankavalamo kamalaya kodula manja. Abusa ankavalanso nkhwayira zimene zinkateteza mapazi awo ku miyala ndi minga ndipo kumutu kwawo ankavala chinsalu cholukidwa ndi ubweya.
Nthawi zambiri m’busa ankagwiritsa ntchito zinthu izi: Thumba lachikopa lomwe ankaikamo zakudya monga mkate, maolivi, zipatso zouma ndi tchizi (1); ndodo yotalika mita imodzi yooneka ngati chibonga yomwe inkakhala yaikulu mbali imodzi (2); mpeni (3); ndodo, imene inkamuthandiza poyenda komanso pokwera mapiri (4); botolo lachikopa lotengera madzi akumwa (5); chotungira madzi chachikopa, chotheka kupinda chomwe ankatungira madzi pachitsime chakuya (6); gulaye, imene ankaigwiritsa ntchito pothamangitsa zilombo zolusa komanso ankaigwiritsa ntchito poponya miyala kutsogolo kwa ziweto pofuna kuti zibwerere pagulu la zinzake (7); chitoliro chimene ankaimba kuti azisangalala komanso azisangalatsa ziweto zake (8).
M’busa amene ankasamalira bwino ziweto zake ankatha kupeza mkaka komanso nyama kuchokera ku ziwetozo. M’busa ankapezanso ndalama akagulitsa ubweya ndi zikopa za nkhosa ndipo ankagwiritsanso ntchito zikopa ndi ubweya kupanga zovala ndi mabotolo. Ubweya wa mbuzi ankapangiranso nsalu ndipo nkhosa ndi mbuzi zomwe, zinkagwiritsidwa ntchito kupereka nsembe.
Chitsanzo Choyenera Kutsatira
Abusa abwino anali olimba mtima, anzeru komanso odziwa bwino ntchito yawo. Nthawi zina iwo ankafika poika miyoyo yawo pachiswe kuti apulumutse ziweto zawo.—1 Samueli 17:34-36.
Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti Yesu ndi ophunzira ake anagwiritsa ntchito abusawa ngati zitsanzo zimene akulu mumpingo ayenera kutsatira. (Yohane 21:15-17; Machitidwe 20:28) Mofanana ndi mmene abusa akale ankachitira, akulu mumpingo ayenera kuyesetsa ‘kuweta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwawo, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.’—1 Petulo 5:2.