YANDIKIRANI MULUNGU
“Mwaziulula kwa Tiana”
Kodi mukufuna kudziwa zoona zokhudza Mulungu? Kuti iye ndi ndani, ndi zinthu ziti zimene amakonda, ndi ziti zomwe amadana nazo, ndipo amafuna chiyani? Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, Yehova Mulungu watiuza zonse zokhudza iyeyo. Koma si aliyense amene angawerenge Baibulo n’kumvetsa bwino zimene limanena. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa choti si anthu onse amene angamvetse bwino choonadi cha m’Baibulo koma okhawo amene apatsidwa mwayi umenewo. Tiyeni tikambirane zimene Yesu ananena pa nkhaniyi.—Werengani Mateyu 11:25.
Vesi limeneli limayamba ndi mawu akuti: “Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti.” Choncho zimene Yesu ananena m’vesili, anazinena chifukwa cha zimene zinali zitangochitika kumene. Iye anali atadzudzula anthu amene sanafune kukhala ophunzira ake. Anthu amenewa anali ochokera m’mizinda itatu ya ku Galileya, yomwe Yesuyo anachitamo zozizwitsa zosiyanasiyana. (Mateyu 11:20-24) Mwina mungadabwe kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu oti anaona zozizwitsa zimene Yesu anachita, analephera kukhulupirira zimene iye ankaphunzitsa?’ N’chifukwa chakuti anthu amenewa anali ndi mtima woipa ndiponso wosamvera.—Mateyu 13:10-15.
Yesu ankadziwa kuti pamafunika zinthu ziwiri kuti munthu amvetse choonadi cha m’Baibulo. Zinthu zimenezi ndi thandizo la Mulungu komanso mtima wabwino. Yesu anati: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.” Kodi mwaona chifukwa chake tinganene kuti si onse amene angamvetse bwino choonadi cha m’Baibulo? Popeza Yehova ndi “Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi,” ali ndi ufulu wosankha amene akufuna kuwaululira choonadi cha m’Baibulo chimenechi. Komabe izi sizikutanthauza kuti Mulungu amachita tsankho posankha anthu owaululirawo. Nanga n’chifukwa chiyani iye amaulula choonadi cha m’Baibulo kwa anthu ena pomwe ena sawaululira?
Yehova amakonda anthu odzichepetsa osati odzikweza. (Yakobo 4:6) Iye amabisira choonadi “anthu anzeru ndi ozindikira,” kutanthauza anthu amene amadziona kuti ndi anzeru ndiponso ophunzira m’dzikoli ndipo chifukwa cha kunyada, amaona kuti safunika thandizo la Mulungu. (1 Akorinto 1:19-21) Koma Mulungu amaulula choonadi kwa “tiana,” kutanthauza anthu amene amafunitsitsa kudziwa Mulungu ndipo amasonyeza kudzichepetsa ngati mmene ana amachitira. (Mateyu 18:1-4; 1 Akorinto 1:26-28) Pamene Mwana wa Mulungu, Yesu, anali padziko lapansi anakumanapo ndi anthu a magulu awiri onsewa. Atsogoleri ambiri onyada achipembedzo, omwenso anali ophunzira kwambiri, sanamvetse tanthauzo la zimene Yesu ankaphunzitsa. Koma anthu wamba, omwe anali asodzi anamvetsa mosavuta. (Mateyu 4:18-22; 23:1-5; Machitidwe 4:13) Komabe, panali anthu ena olemera komanso ophunzira omwe anasonyeza kudzichepetsa kwenikweni ndipo anakhala otsatira a Yesu.—Luka 19:1, 2, 8; Machitidwe 22:1-3.
Tiyeni tibwererenso ku funso lomwe lili koyambirira kwa nkhani ino lija: Kodi mukufuna kudziwa zoona zokhudza Mulungu? Ngati mukufuna, muyenera kudziwa kuti Mulungu sasangalala ndi anthu amene amadziona kuti ndi anzeru m’dzikoli. Koma amasangalala ndi anthu omwe dzikoli limawaona ngati anthu wamba. Ngati mutaphunzira Baibulo ndi mtima wabwino komanso maganizo oyenera, mungakhale m’gulu la anthu amene Yehova wawapatsa mphatso ya mtengo wapatali, yomwe ndi kumvetsa choonadi chonena za iye. Kumvetsa choonadi chimenechi kungakuthandizeni kukhala osangalala panopa. Kungakuthandizeninso kudzapeza ‘moyo weniweni’ womwe ndi moyo wosatha m’dziko lopanda mavuto lomwe Mulungu walonjeza limene likubwera posachedwapa. *—1 Timoteyo 6:12, 19; 2 Petulo 3:13.
Mavesi amene mungawerenge mu January
^ ndime 7 A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuphunzira choonadi chonena za Mulungu komanso zimene iye akufuna kuchita. Iwo amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere pogwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?