Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Umene Ena Amati Uthenga Wabwino wa Yudasi N’chiyani?

Kodi Umene Ena Amati Uthenga Wabwino wa Yudasi N’chiyani?

MU April 2006, nyuzipepala zambiri padziko lonse zinalemba nkhani imene akatswiri amaphunziro anatulutsa. Nkhani imeneyi inali yonena za kupezeka kwa umene ena amati ndi Uthenga Wabwino wa Yudasi ndipo anthu ambiri anachita nayo chidwi. Akatswiriwo ananena kuti zimenezi zithandiza anthu kusintha mmene amaonera Yudasi, wophunzira amene anapereka Yesu. Uthengawu umati Yudasi anali mtumwi wapadera kwambiri chifukwa ndi amene ankamumvetsa bwino Yesu ndipo anachita kutumidwa ndi Yesuyo kuti amupereke.

Kodi zimene zili mu umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasiwu n’zolondola? Ngati zili zolondola, kodi zingatithandize kudziwa zinthu zina zimene m’Baibulo mulibe zokhudza Yudasi Isikariyoti, Yesu Khristu komanso Akhristu oyambirira? Kodi zimene zili mu mpukutuwu zingatichititse kusintha mmene timaonera Yesu komanso ziphunzitso zake?

KODI UMENE AMATI UTHENGA WABWINO WA YUDASI UNAPEZEKA BWANJI?

Sizikudziwika mmene uthengawu unapezekera komanso anthu amene anaupeza. Koma unangoyamba kupezeka pamisika yogulitsa zinthu zakale chakumapeto kwa zaka za m’ma 1970 kapena koyambirira kwa zaka za m’ma 1980. Mwina uthengawu unapezeka ku Egypt mu 1978 kuphanga, m’manda enaake akale. Uthengawu anaupeza mumpukutu wachikopa momwe munalinso zolemba zina zakale. Mpukutuwo unalembedwa m’Chikoputiki, chomwe ndi chinenero chochokera ku Iguputo.

Mpukutuwu utachotsedwa ku Egypt komwe unasungidwa zaka zambirimbiri, komwenso nyengo yake ndi yotentha, unayamba kuwonongeka. M’chaka cha 1983, mpukutuwu anausonyeza kwa akatswiri angapo amaphunziro koma mtengo wake unali wokwera kwambiri moti akatswiriwo sanathe kuugula. Chifukwa choti mpukutuwu sunasungidwe pamalo abwino komanso sunkasamalidwa, zinapangitsa kuti uziwonongekabe. M’chaka cha 2000, mpukutuwu unagulidwa ndi mayi wina wosunga zinthu zakale wa ku Switzerland. Kenako iye anaupereka kwa akatswiri ena omwe mothandizidwa ndi mabungwe ena oona zinthu zakale, anaukonzanso ndi kubwezeretsa tizidutswa tina ndi tina tomwe tinali titang’ambika.  Akatswiriwa anafufuza nthawi imene mpukutuwu unalembedwa ndipo anaumasulira komanso kufotokoza mfundo zimene zinali mumpukutuwu.

Kafukufuku wina anasonyeza kuti mpukutuwu unalembedwa cha m’ma 200 kapena 300 C.E. Komabe akatswiri ena amaganiza kuti mpukutuwu, womwe poyamba unalembedwa m’Chigiriki chakale, unamasuliridwa m’Chikoputiki, kale kwambiri zisanafike zaka zimenezi. Kodi umene ena amati Uthenga Wabwino wa Yudasi unalembedwa liti, nanga zinthu zinali bwanji pa nthawiyo?

UNALEMBEDWA NDI ANTHU AMPATUKO

Wolemba mabuku wina wa m’zaka za m’ma 100 C.E., dzina lake Irenaeus, yemwe ankati ndi Mkhristu, ndi amene anayamba kutchula za umene ena amati Uthenga Wabwino wa Yudasi. Iye analemba m’buku lake lina (Against Heresies) za magulu ambiri amene ziphunzitso zawo sankagwirizana nazo. Iye ananena kuti: “Anthu amenewa amati Yudasi ankadziwa zinthu zambiri kuposa ophunzira ena, choncho anakwanitsa kugwira ntchito imene Yesu anamuuza yoti amupereke. Yesu anagwiritsa ntchito iyeyo kuchita zinthu zimene anthu ngakhalenso angelo sangathe kuzimvetsa. Anthu amenewa analemba mbiri yabodzayi yomwe anaitchula kuti Uthenga Wabwino wa Yudasi.”

“Munthu amene analemba Uthengawu sankamudziwa n’komwe Yudasi ndiponso sunalembedwe mu nthawi ya Yudasi”

Cholinga chachikulu cha Irenaeus chinali kutsutsa ziphunzitso za Akhristu ampatuko amene ankati amatha kudziwa zinthu zapadera. Akhristu ampatukowa alipo a magulu osiyanasiyana ndipo gulu lililonse lili ndi ziphunzitso zake komanso limatanthauzira mosiyanasiyana zokhudza Chikhristu. Ampatukowa analemba mabuku okhudza ziphunzitso zawo ndipo mabukuwa anali ofala kwambiri m’zaka za m’ma 100 C.E.

Mauthenga Abwino a anthu ampatukowa amati atumwi otchuka a Yesu sankamvetsa uthenga wake. Mauthengawa amanenanso kuti pali chiphunzitso china chachinsinsi cha Yesu chomwe anachimvetsa ndi anthu owerengeka chabe amene iye anawasankha. * Ena mwa anthu ampatukowa amakhulupirira kuti dziko lapansili ndi ndende ya anthu, choncho “mulungu amene analenga dziko lapansi,” yemwe amatchulidwa m’Malemba Achiheberi ndi wotsikirapo poyerekezera ndi milungu ina. Iwo amakhulupiriranso kuti munthu akamvetsa chinsinsichi amafufuza njira yoti achokere m’dzikoli.

Umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi unatchulidwa potengera mfundo imeneyi. Uthengawu umayamba ndi mawu akuti: “Chinsinsi chimene Yesu anauza Yudasi Isikariyoti kutatsala masiku atatu kuti achite Pasika.”

Kodi umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasiwu ndi umene Irenaeus anautchula m’buku lake, omwenso anthu amati unali wobisika kwa zaka zambiri? Marvin Meyer yemwe anali nawo m’gulu limene linamasulira mpukutu womwe munali Uthengawu, ananena kuti zimene Irenaeus analemba zinasonyeza kuti “ankanena za umene ena amati Uthenga Wabwino wa Yudasi womwe unalembedwa m’chinenero cha Chikoputiki.”

AKATSWIRI AMASIYANA MAGANIZO PA NKHANI YA YUDASI WOTCHULIDWA MU UTHENGAWU

Umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi umati Yesu ankaseka monyoza kwambiri ophunzira ake akalephera kumvetsa mfundo zina zimene iye ankaphunzitsa. Koma Yudasi yekha ndi amene ankamudziwa bwino Yesu kuposa atumwi ena 11 aja. Choncho Yesu anauza Yudasiyo “zinsinsi zokhudza ufumu.”

Akatswiri amene anamasulira umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi aja, anatsatira kwambiri zimene Irenaeus ananena zokhudza Uthengawu. M’buku lawo limene anamasulirali, likusonyeza kuti Yudasi ankakondedwa kwambiri ndi Yesu chifukwa anali wophunzira yemwe ankamvetsa zinsinsi komanso akanatha “kulowa” mu “ufumu.” Bukuli limasonyezanso kuti, ngakhale kuti ophunzira ena aja anasankha munthu wina yemwe analowa m’malo mwa Yudasi, Yudasiyo anadzakhala “wophunzira wauzimu wa 13” yemwenso “analandira mphoto yoposa  [ophunzira] onse” chifukwa chothandiza Yesu kuchoka m’dzikoli.

Akatswiri olemba mabuku monga Bart Ehrman ndi Elaine Pagels, omwenso amadziwa bwino mbiri yachikhristu komanso mmene mpatuko unayambira, anafalitsa mabuku komanso nkhani zawo zonena za umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi. Nkhani zawozi zinali zofanana kwambiri ndi zimene akatswiri oyambirira aja anamasulira. Komabe pasanapite nthawi akatswiri monga April DeConick ndi Birger Pearson sanagwirizane kwenikweni ndi zimene anzawowa analemba. Iwo ananena kuti anzawowa anangothamangira kufalitsa mabuku awowa asanafufuze mokwanira. Anadandaulanso kuti iwo sanachite zonse zofunika koma anangothamangira kutulutsa mabukuwa n’cholinga choti atchuke basi.

Palibe katswiri wamaphunziro amene anavomereza kuti mfundo za mu Uthengawu n’zolondola

DeConick ndi Pearson anafufuza zokhudza mabukuwa payekhapayekha koma onse anapeza kuti akatswiri oyambirira amene anamasulira mpukutu uja sanamasulire bwino mbali zake zikuluzikulu. DeConick pofuna kukonza zimene anzawowo analakwitsa, anamasulira kuti Yesu anatchula Yudasi kuti “Chiwanda cha 13” osati “wophunzira wauzimu wa 13.” * Iye ananenanso kuti Yesu anauza Yudasi mosapita m’mbali kuti sadzalowa mu “ufumu.” Anatinso Yesu sanauze Yudasi kuti anali ‘woposa’ ophunzira ena koma anamuuza kuti: “Iwe udzachita zinthu zoipa kwambiri kuposa ophunzira ena onse chifukwa unandichitira zinthu zoipa.” DeConick ankaona kuti umene ena amati Uthenga Wabwino wa Yudasi ndi zolemba zakale za anthu ampatuko zomwe cholinga chake chinali kunyoza atumwi. DeConick ndi Pearson anapeza kuti Yudasi sanali wophunzira wapadera ngati mmene ena amanenera.

UMBONI WAKUTI BAIBULO NDI LOLONDOLA

Kaya akatswiriwa amati Yudasi anali wapadera kuposa ophunzira ena kapena anali chiwanda, koma mfundo ndi yakuti akatswiri onsewa savomereza kuti umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi ndi wolondola. Bart Ehrman ananena kuti: “Uthenga umenewu sunalembedwe ndi Yudasi kapenanso aliyense amene ankati ndi Yudasi . . . Munthu amene analemba uthengawu sankamudziwa n’komwe Yudasi ndiponso sunalembedwe mu nthawi ya Yudasi . . . Choncho Uthenga umenewu sungatiuze zinthu zomwe zinachitika pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi zimene m’Baibulo mulibe.”

Umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasi n’zolemba za ampatuko zomwe zinalembedwa cha m’ma 100 C.E. m’Chigiriki. Akatswiri ena amati Uthenga umenewu ndi umene Irenaeus anatchula m’buku lake pamene ena amatsutsa mfundo imeneyi. Koma umene ena amati ndi Uthenga Wabwino wa Yudasiwu ndi umboni wakuti Akhristu ampatuko anayambitsa ziphunzitso zawo zimene zinachititsa kuti pakhale magulu ambiri ampatuko. Choncho m’malo mopereka umboni wotsutsa Baibulo, umene amati Uthenga Wabwino wa Yudasiwu, umatsimikizira kuti zimene atumwi ananena zinachitikadi. Mwachitsanzo, Paulo ananena pa Machitidwe 20:29, 30 kuti: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka. . . pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.”

^ ndime 11 Mauthenga amenewa ankawapatsa mayina potengera munthu amene akuona kuti anamvetsa bwino mfundo inayake imene Yesu anaphunzitsa. Zitsanzo za Mauthenga oterewa ndi ngati umene amati Uthenga Wabwino wa Tomasi komanso umene amati Uthenga Wabwino wa Mariya Mmagadala. Mauthenga Abwino oterewa alipo 30.

^ ndime 18 Akatswiri amene amanena kuti Yudasi anali chiwanda, chimene chinkadziwa bwino Yesu kuposa ophunzira enawo, amaona kuti izi n’zofanana ndi zimene ziwanda zotchulidwa mu Uthenga Wabwino weniweni wa m’Baibulo zinkachita. Izo zinanena molondola zokhudza Yesu.—Maliko 3:11; 5:7.