Kodi N’zotheka Kuona Mulungu Yemwe ndi Wosaoneka?
“MULUNGU ndiye Mzimu,” choncho palibe munthu amene angathe kumuona. (Yohane 4:24) Komabe Baibulo limanena kuti, mwa njira inayake, anthu ena anaonapo Mulungu. (Aheberi 11:27) Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Kodi munthu angathedi kuona “Mulungu wosaonekayo”?—Akolose 1:15.
Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tiyerekeze ndi zimene zimachitika kwa munthu wakhungu, woti sanaonanepo chibadwire. Kodi vuto lakeli limam’chititsa kuti asamazindikire chilichonse? Ayi. Munthu wosaona amatha kuzindikira anthu komanso zinthu zina ndipo pali njira zosiyanasiyana zimene zimamuthandiza kuchita zimenezi. Munthu wina wosaona ananena kuti: “Munthu wakhungu saona ndi maso. Iye amaona zinthu ndi maganizo.”
Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti simungathe kuona Mulungu ndi maso anu, mungathe kumuona ndi “maso a mtima wanu.” (Aefeso 1:18) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Tiyeni tione njira zitatu.
‘AMAONEKERA M’ZINTHU ZIMENE ANAPANGA’
Munthu wosaona amatha kuzindikira zinthu pogwiritsa ntchito zimene wamva kapena kukhudza. Nanunso mungathe kugwiritsa ntchito zinthu zimene Mulungu analenga n’kudziwa zokhudza Mulunguyo. Baibulo limati: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.
Mwachitsanzo, taganizirani za dziko lapansili. Dzikoli linapangidwa mwa njira yakuti pazikhala zinthu zamoyo komanso kuti anthufe tizisangalala ndi moyowo. Timasangalala kwambiri ndi zinthu monga kamphepo kayaziyazi, kuwothera dzuwa, zipatso zokoma komanso kulira kwa mbalame. Kodi si zoona kuti zinthu zimenezi zimasonyeza kuti Mlengi wathu ndi wachikondi, wowolowa manja komanso amatiganizira?
Kodi tingaphunzire chiyani zokhudza Mulungu pa zinthu zimene timaona m’chilengedwechi? Chinthu chimodzi chimene tingaphunzirepo n’choti, zinthu zakumwamba zimene anapanga zimasonyeza kuti ndi wamphamvu. Zimene akatswiri asayansi apeza zikusonyeza kuti thamboli likukula ndipo zimenezi zikuchitika mofulumira kwambiri. Tsiku lina usiku mudzayang’ane kumwamba n’kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndani amachititsa kuti zinthu zonsezi ziziyenda mwadongosolo?’ Baibulo limanena kuti Mlengi ali ndi ‘mphamvu zoopsa.’ (Yesaya 40:26) Choncho zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti iye ndi “Wamphamvuyonse” ndipo ali ndi “mphamvu zambiri.”—Yobu 37:23.
“AMENE ANAFOTOKOZA ZA MULUNGU”
Mayi wina amene ali ndi ana awiri osaona ananena kuti: “Chimene chimathandiza kwambiri ana anga kuti aphunzire zinthu, ndi kuwafotokozera zinthuzo. Ndikafika nawo pamalo, ndimafunika kuwauza chilichonse chokhudza zimene ndikuona komanso kumva. Iwo amaona kuti maso awo ndi ineyo.” Mofanana ndi zimenezi, popeza anthufe sitingathe kuona Mulungu, Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, amatifotokozera za Mulunguyo. (Yohane 1:18) Popeza Yesu ndi woyamba kulengedwa komanso Mwana wa Mulungu wobadwa yekha, tingati iye ali ngati “maso” athu otithandiza kuona Mulungu. Yesu ndi amene angatiuze zolondola zokhudza Mulungu, yemwe ndi wosaoneka.
Taonani zina mwa zinthu zimene Yesu ananena zokhudza Mulungu.
Mulungu amagwira ntchito nthawi zonse. “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano.”—Yohane 5:17.
Mulungu amadziwa zimene timafunikira. “Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”—Mateyu 6:8.
Mulungu amatipatsa dzuwa ndi mvula mwa chisomo chake. “Atate wanu wakumwamba . . . amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mateyu 5:45.
Mulungu amaona kuti munthu aliyense ndi wofunika. “Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”—Mateyu 10:29-31.
AMENE ANAONETSA MAKHALIDWE A MULUNGU WOSAONEKA
Njira zimene anthu osaona amagwiritsa ntchito kuti azindikire zinthu, n’zosiyana ndi zimene anthu oona amagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo, munthu wosaona amazindikira kuti wafika pamthunzi ngati pamalopo pakumveka pozizira bwino ndipo sipakumveka kutentha kwa dzuwa. Pamene munthu woona amaona chithunzithunzi komanso amaona kuti pamalopo sipakuwala kwambiri kuyerekezera ndi pamalo pomwe pali dzuwa. Mofanana ndi mmene zimakhalira kuti munthu wosaona sangathe kuona mthunzi kapena kuwala kwa dzuwa, ifenso sitikanatha kumvetsa zokhudza Yehova. Choncho pofuna kutithandiza, Yehova anatipatsa munthu amene amatithandiza kudziwa bwinobwino mmene iyeyo alili.
Munthu ameneyu ndi Yesu. (Afilipi 2:7) Yesu anafotokoza zokhudza Atate wake komanso anatithandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wotani. Wophunzira wake wina, dzina lake Filipo, anamupempha kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo.” Yesu anamuyankha kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:8, 9) Kodi tingaone zinthu ziti zokhudza atate kudzera mwa Yesu?
Yesu anali wachikondi, wodzichepetsa komanso wochezeka. (Mateyu 11:28-30) Zimenezi zinachititsa kuti anthu azimukonda kwambiri. Anthu akakhala pa chisoni, Yesu ankamvanso chisoni, ndipo akamasangalala nayenso ankasangalala. (Luka 10:17, 21; Yohane 11:32-35) Mukamawerenga nkhani zokhudza Yesu m’Baibulo, muziyerekeza kuti mukuona zimene mukuwerengazo zikuchitika. Komanso mukamaganizira kwambiri mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu, mungadziwe makhalidwe a Yehova zomwe zingakhale ngati mukumuona. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri Yehova.
MUZIGWIRIZANITSA ZINTHU
Munthu wina wolemba mabuku ananena zinthu zinanso zimene zimathandiza anthu osaona kuzindikira zinthu. Iye anati: “Kuti munthu wosaona azindikire chinthu amagwiritsa ntchito zimene wamva, waona komanso zimene wanunkhiza. Kenako amaphatikiza zonsezo ndipo zimamuthandiza kuzindikira chinthucho.” Mofanana ndi zimenezi, tikamaona zimene Mulungu analenga, tikamawerenga zimene Yesu ananena zokhudza Atate wake komanso tikamaganizira mmene Yesu anasonyezera makhalidwe a Mulungu, tidzatha kuona mmene Yehova alili. Zimenezi zidzatithandiza kuona kuti Yehova ndi weniweni.
Izitu n’zimene zinachitikira munthu wina wotchulidwa m’Baibulo, dzina lake Yobu. Poyamba iye ananena kuti, “ndinalankhula, koma sindinali kuzindikira.” (Yobu 42:3) Koma ataganizira mozama zinthu zodabwitsa zimene Mulungu analenga, ananena kuti: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.”—Yobu 42:5.
‘Ukam’funafuna Yehova, adzalola kuti um’peze’
Izi zingakuchitikireninso inuyo. Baibulo limati: “Ukam’funafuna [Yehova], adzalola kuti um’peze.” (1 Mbiri 28:9) A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuti muphunzire za Mulungu n’kuyamba kumuona, ngakhale kuti ndi wosaoneka.