Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Tiyenera Kudziwa pa Nkhani ya Khirisimasi?

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Tiyenera Kudziwa pa Nkhani ya Khirisimasi?

Anthu ambiri amakondwerera Khirisimasi ndipo amachita zimenezi pa zifukwa zosiyanasiyana. Ena amaona kuti imeneyi ndi nthawi yosangalala ndi achibale awo komanso anzawo. Pomwe ena amaona kuti ndi nthawi yolemekeza Mulungu komanso kuthandiza ovutika. Zinthu zimene amachitazi pazokha si zolakwika. Koma vuto ndi loti amachita zinthuzi pa chikondwerero chomwe ndi chosagwirizana ndi Malemba. Tikutero pa zifukwa zotsatirazi.

Choyamba, anthu ambiri amakhulupirira kuti Khirisimasi ndi nthawi yokondwerera kubadwa kwa Yesu. Komabe akatswiri a mbiri yakale amati tsiku limene Yesu anabadwa silidziwika. Komanso buku lina linanena kuti: “Akhristu oyambirira anakana kukhazikitsa tsiku lokondwerera kubadwa kwa Yesu,” chifukwa “ankadziwa kuti anthu osalambira Mulungu ndi amene ankakondwerera masiku a kubadwa ndipo sankafuna kufanana nawo.” (The Christian Book of Why) Komansotu Baibulo silisonyeza kuti Yesu ankakondwerera tsiku la kubadwa kwake kapena kwa munthu wina aliyense. M’malomwake, iye analamula otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake.—Luka 22:19.

Chachiwiri, akatswiri ambiri amaphunziro amavomereza kuti zinthu zambiri zomwe zimachitika pa Khirisimasi zinachokera kwa anthu omwe sanali Akhristu komanso ku miyambo yachikunja. Zina mwa zinthu zimenezi ndi monga, Father Christmas, kugwiritsa ntchito maluwa ndi mitengo ya pa Khirisimasi, kupatsana mphatso, kuyatsa makandulo komanso zokongoletsa zina za pa Khirisimasi. Ponena za zinthu zimenezi, buku lina linati: “Tikamapereka ndi kulandira mphatso za pa Khirisimasi kapena kupachika maluwa a Khirisimasi m’nyumba komanso m’tchalitchi mwathu, ambirife sitidziwa kuti tikuchita miyambo yachikunja.”—The Externals of the Catholic Church.

“Tikamapereka ndi kulandira mphatso za pa Khirisimasi kapena kupachika maluwa a Khirisimasi m’nyumba komanso m’tchalitchi mwathu, ambirife sitidziwa kuti tikuchita miyambo yachikunja.”—The Externals of the Catholic Church

Koma mwina munganene kuti, ngakhale kuti zinthuzi zinachokera ku miyambo yachikunja, pazokha si zoipa, choncho si vuto kuchita zinthuzi. Zimenezi zikutifikitsa pa mfundo yachitatu yakuti, Mulungu safuna kuti anthu aziphatikiza kulambira iyeyo ndi miyambo yachikunja. Kudzera mwa mneneri Amosi, Yehova Mulungu anauza Aisiraeli, omwe anali atasiya kumumvera kuti: “Ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo ndikuzikana, . . .  sindikufuna kumva nyimbo zanu.”—Amosi 5:21, 23.

Koma kodi n’chifukwa chiyani Mulungu ananena mawu amenewa? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione zimene anthu a mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli ankachita. Mfumu yoyamba ya ufumuwu, dzina lake Yerobowamu, inaika mwana wang’ombe wagolide mumzinda wa Dani komanso Beteli. Mfumuyi inakopanso anthu kuti azilambira ana a ng’ombewa m’malo mopita kukachisi wa ku Yerusalemu, komwe ankayenera kukalambirako Yehova Mulungu. Inayambitsanso zikondwerero zosiyanasiyana ndipo inasankha anthu ena kuti akhale ansembe n’cholinga choti azitsogolera anthu akamachita zikondwererozi.—1 Mafumu 12:26-33.

Aisiraeliwa ankaona kuti sakulakwa. Ankaona kuti akulambira Mulungu komanso kumusangalatsa. Koma zimene Mulungu ananena kudzera mwa Amosi komanso aneneri ena, zikusonyeza kuti iye sankasangalala ndi zimenezi. Lemba la Malaki 3:6 limati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” Popeza lembali likuti Mulungu sasintha, ndiye kuti masiku ano amadanabe ndi miyambo yomwe imachitika pa Khirisimasi.

Anthu ambiri akaganizira mfundo zomwe takambiranazi, amaona kuti si bwino kuchita Khirisimasi. Iwo amakonda kucheza ndi achibale, anzawo komanso kuthandiza anthu osauka, koma amachita zimenezi nthawi iliyonse, osati pa Khirisimasi.