Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | YESU ANATIPULUMUTSA KU UCHIMO NDI IMFA

Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha

Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha

“Khulupirira mwa Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka.”—Machitidwe 16:31.

Mawu osaiwalika amenewa ananena ndi Paulo komanso Sila ndipo ankauza woyang’anira ndende wina wa ku Makedoniya mumzinda wa Filipi. Kodi ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti pali kugwirizana pakati pa kukhulupirira Yesu ndi kupulumuka. Koma kuti timvetse zimenezi tiyenera kudziwa kaye kuti n’chifukwa chiyani anthufe timafa. Tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi.

Mulungu sanafune kuti tizifa

“Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalira. Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’”—Genesis 2:15-17.

Mulungu anaika Adamu, yemwe anali munthu woyamba, m’munda wa Edeni. Mundawu unali ndi nyama komanso mitengo ndi maluwa okongola. M’mundawu munalinso mitengo yambiri ya zipatso zoti Adamu azidya. Koma Yehova Mulungu anamuuza kuti asadye zipatso za mtengo umodzi ndipo anamuchenjeza kuti akadzadya adzafa.

Kodi Adamu anamvetsa bwino lamuloli? Inde. Adamu ankadziwa kuti imfa ndi chiyani chifukwa ankaona nyama zikufa. Zikanakhala kuti Mulungu analenga Adamu kuti pakapita nthawi adzafe, lamulo limeneli silikanakhala loopsa kwambiri. Koma Adamu ankadziwa kuti akamvera lamulo la Mulunguli, saafa ndipo akhala ndi moyo kwamuyaya.

Anthu ena amakhulupirira kuti lamulo la Mulungu loletsa Adamu kuti asadye zipatso za mtengowo, linkaphiphiritsira kuti Mulungu analetsa Adamu ndi Hava kuti asamagonane. Koma izi si zoona. Chifukwatu Yehova ankafuna kuti Adamu ndi mkazi wake Hava, abereke ana, achuluke, adzaze dziko lapansi. (Genesis 1:28) Choncho Mulungu analetsa Adamu kudya zipatso za mtengo weniweni. Yehova anatchula mtengowu kuti “wodziwitsa chabwino ndi choipa” chifukwa unkaimira kuti Yehova yekha ndi amene ayenera kuuza anthu kuti izi n’zabwino ndipo izi n’zoipa. Adamu akanapanda kudya zipatso za mtengowo, akanasonyeza kuti ankamvera Mulungu komanso ankamuyamikira kuti anamulenga n’kumupatsa zinthu zambiri.

Adamu anafa chifukwa sanamvere Mulungu

“Kwa Adamu, Mulungu ananena kuti: ‘Chifukwa . . . wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti, “usadzadye zipatso zake,” . . . udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.’”—Genesis 3:17, 19.

Adamu anadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anamuletsa. Zimene anachitazi linali tchimo loopsa chifukwa anaswa dala lamulo la Mulungu ndipo anasonyeza kusayamikira zinthu zabwino zomwe Mulunguyo anamuchitira. Podya chipatsocho, Adamu anasonyezanso kuti akufuna kuti azidzilamulira yekha osati Yehova azimulamulira. Zotsatira zake zinali zoipa kwambiri.

Monga mmene Yehova ananenera, patapita nthawi Adamu anafa. Popeza Mulungu analenga Adamu kuchokera “kufumbi lapansi,” anamuuza kuti ‘adzabwerera kufumbiko.’ Choncho Adamu atafa sanapite kwinakwake, koma anakhala wopanda moyo ngati mmene fumbi limakhalira.—Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10.

Timafa chifukwa tinachokera kwa Adamu

‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12.

Tchimo la Adamu linabweretsa mavuto ambiri. Adamu anataya mwayi wokhala ndi moyo, osati kwa zaka 70 kapena 80 zokha, koma kosatha. Komanso tchimo lake linachititsa kuti iyeyo komanso ana amene adzabereke asakhale angwiro.

Anthu tonsefe tinachokera kwa Adamu. Choncho iye anatipatsira uchimo ndipo tifune tisafune, timafa chifukwa cha uchimowo. Paulo anafotokoza bwino zimenezi. Anati: “Ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo. Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Kenako anayankha funso lakeli kuti: “Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.”—Aroma 7:14, 24, 25.

Yesu anapereka moyo wake kuti tidzakhale ndi moyo wosatha

“Atate anatumiza Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko.”—1 Yohane 4:14.

Yehova Mulungu anakonza njira n’cholinga choti atipulumutse ku imfa ndi zotsatira zonse za uchimo. Iye anatumiza Mwana wake wokondedwa kuti adzabadwe ndi moyo wangwiro ngati umene Adamu anali nawo asanachimwe. Mosiyana ndi Adamu, Yesu “sanachite tchimo.” (1 Petulo 2:22) Popeza Yesu anali wangwiro, sakanafa ndipo akanatha kukhala ndi moyo padzikoli kwamuyaya.

Komabe Mulungu analola kuti Yesu aphedwe ndi adani ake. Koma patatha masiku atatu, anamuukitsa ndi thupi lauzimu ndipo kenako anabwerera kumwamba. Kumwambako Yesu analipira kwa Yehova mtengo wa moyo wake kuti awombole moyo wangwiro umene Adamu anataya. Yehova analandira, ndipo izi zinapangitsa kuti onse okhulupirira Yesu akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Aroma 3:23, 24; 1 Yohane 2:2.

Apa ndiye kuti Yesu anabwezeretsa moyo wangwiro womwe Adamu anataya. Iye anatifera kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. Baibulo limati: “Yesu, . . . anazunzika mpaka imfa. Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.”—Aheberi 2:9.

Zimene Yehova anachitazi zikusonyeza kuti Yehova amatsatira mfundo zake zolungama. Malinga ndi mfundozi, zinali zosatheka kuti munthu wochimwa awombole anthu. Komabe popeza Mulungu ndi wachikondi komanso wachifundo, analolera kupereka Mwana wake kuti atiwombole.—Aroma 5:6-8.

Popeza Yesu anaukitsidwa, anthu ambiri adzaukitsidwanso m’tsogolomu

“Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa. Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akorinto 15:20-22.

Ambirife tikudziwa kuti Yesu anabwera padzikoli ndipo kenako anaphedwa. Koma kodi pali umboni wotani woti anaukitsidwa? Umboni wosatsutsika ndi wakuti Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa anthu osiyanasiyana pamalo osiyanasiyananso. Pa nthawi ina anaonekera kwa anthu oposa 500. Patapita nthawi mtumwi Paulo analembera Akorinto kuti anthu ena amene anaona Yesu ataukitsidwa anali adakali moyo. Paulo ananena zimenezi pofuna kusonyeza kuti anthuwo akanatha kupereka umboni woti Yesu anaukitsidwadi.—1 Akorinto 15:3-8.

Komanso pamene Paulo ananena kuti Khristu ndi “chipatso choyambirira,” anasonyeza kuti palinso anthu ena amene adzaukitsidwe. Ndipotu Yesu ananena kuti ‘idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzatuluka.’—Yohane 5:28, 29.

Kuti tidzapeze moyo wosatha tiyenera kukhulupirira Yesu

“Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha”—Yohane 3:16.

Buku la Genesis limatiuza zimene zinachititsa kuti anthu azifa komanso kuti dziko lapansili lisakhalenso Paradaiso. Ndipo buku la Chivumbulutso limatiuza za nthawi imene Mulungu adzathetse imfa n’kubwezeretsa Paradaiso padzikoli. Pa nthawiyo anthu adzakhala ndi moyo wabwino ndipo adzasangalala kosatha. Lemba la Chivumbulutso 21:4 limati: “Imfa sidzakhalaponso.” Pofuna kutsimikizira kuti zimenezi zidzachitikadi, vesi 5 limati: “Mawu awa ndi odalirika ndi oona.” Sitingakayikire zimene Yehova wanena chifukwa amakwaniritsa zonse zomwe walonjeza.

Kodi inuyo mukukhulupirira kuti imfa sidzakhalapodi? Tikukulimbikitsani kuti muphunzire za Yesu Khristu ndi kuyamba kumukhulupirira kwambiri. Kuchita zimenezi kungachititse kuti Yehova azikukondani. Zingachititsenso kuti akudalitseni panopa komanso kuti mukhale ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Pa nthawiyo “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”