Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka

Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka
  • CHAKA CHOBADWA: 1954

  • DZIKO: CANADA

  • POYAMBA: NDINKABERA ANTHU MWACHINYENGO KOMANSO NDINKATCHOVA JUGA

KALE LANGA:

Ndinakulira m’dera lina losauka mumzinda wa Montreal. M’banja mwathu tinalipo ana 8 ndipo ineyo ndine womaliza. Bambo anga anamwalira ndili ndi miyezi 6 yokha ndipo udindo wosamalira ana tonsefe unatsala ndi mayi.

Anthu a m’dera lathu ankakonda kugulitsa mankhwala osokoneza bongo, kuchita zachiwawa, kutchova juga komanso kuchita zinthu zina zophwanya malamulo. Zimenezi zinachititsa kuti nanenso ndiyambe kuchita makhalidwe oipawa. Ndili ndi zaka 10, ndinayamba kuthandiza anthu obwereketsa ndalama zakatapira komanso mahule. Ndinkakondanso kubera anthu mwachinyengo.

Pamene ndinkakwanitsa zaka 14, n’kuti nditajaira kubera anthu mwachinyengo. Mwachitsanzo ndinkagula mawotchi, zibangili ndi mphete zokhala ndi golide pang’ono. Kenako ndinkazidinda kachizindikiro kosonyeza ngati ndi zopangidwa ndi golide yekhayekha n’kuzigulitsa modula kwambiri. Ndinkazigulitsa mumsewu komanso m’malo oimika magalimoto kunja kwa mashopu akuluakulu. Ndinkasangalala ndi zimenezi chifukwa ndinkapeza ndalama zambiri popanda kukhetsa thukuta. Moti nthawi ina ndinapeza ndalama zokwana madola 10,000 a ku Canada, tsiku limodzi.

Ndili ndi zaka 15, anandichotsa pamalo enaake osungirako ana powathandiza kuti asinthe khalidwe. Izi zinachititsa kuti ndizisowa pokhala moti ndinayamba kumagona m’misewu, m’mapaki ndi kunyumba kwa anzanga.

Chifukwa cha khalidwe langa lobera anthu mwachinyengo, apolisi sankati andigwira liti. Koma popeza sindinkagulitsa katundu wakuba, sankandipititsa kundende. Komabe nthawi zambiri ankandilipiritsa chindapusa, chifukwa chobera anthu mwachinyengo komanso kugulitsa zinthu popanda chilolezo. Ndinali munthu wovuta moti nthawi zina anthu obwereketsa ndalama zakatapira ankandituma kuti ndikawatengere ndalama zawo kwa angongole. Zimenezi zinali zoopsa kwambiri moti pena ndinkayenda ndi mfuti. Nthawi zinanso ndinkagwirizana ndi magulu a zigawenga n’kumabera anthu.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Ndinamva zokhudza Baibulo ndili ndi zaka 17. Pa nthawiyi ndinkakhala ndi mtsikana wina yemwe ndinali naye pa chibwenzi ndipo iyeyo anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Koma ndinkaona kuti mfundo za m’Baibulo n’zovuta kuzitsatira, choncho ndinamusiya. Kenako ndinayamba kukhala ndi mtsikana wina amene ndinali nayenso pa chibwenzi.

Koma patapita nthawi, nayenso anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Atayamba kuphunzira, ndinaona kuti wayamba kusintha. Anayamba kuchita zinthu modekha ndi moleza mtima ndipo zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. Choncho a Mboni atandipempha kuti ndipite ku Nyumba ya Ufumu, ndinapitadi. Zimene ndinaona kumeneko zinali zachilendo kwambiri. Anthu ake anali okoma mtima komanso ovala bwino ndipo anandilandira ndi manja awiri. Ndinakulira m’banja loti aliyense ankangochita zake ndipo sitinkakondana kwenikweni. Koma nditapita ku Nyumba ya Ufumu, ndinaona kuti anthu ake anali achikondi. Choncho atandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo, ndinavomera.

Ndikuona kuti zimene ndinaphunzira m’Baibulo ndi zomwe zachititsa kuti ndikhale ndi moyo mpaka pano. Mwachitsanzo, ndisanayambe kuphunzira Baibulo, nthawi ina ndinagwirizana ndi anzanga kuti tikabe kwinakwake. Ndinkafuna kupeza ndalama zoposa madola 50,000 kuti ndilipire ngongole yomwe ndinali nayo chifukwa chotchova juga. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinasintha maganizo ndipo sindinapite ndi anzangawo kokaba. Ndikuona kuti ndinachita bwino chifukwa anzangawo atapita, anakumana ndi zokhoma. Wina anaphedwa ndipo wina anamangidwa.

Zimene ndinkaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kudziwa kuti panali zambiri zomwe ndinkafunika kusintha. Mwachitsanzo ndinadziwa kuti, “akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:10) Nditawerenga lembali, ndinagwetsa misozi poona kuti zimenezi ndi zimene ndinkachita. Ndinali waukali, wachiwawa ndipo bodza linali kudya kwanga. Choncho ndinazindikira kuti ndinkafunika kusintha kwambiri moyo wanga.—Aroma 12:2.

Komabe ndinaphunziranso kuti Yehova ndi wachifundo komanso amakhululuka. (Yesaya 1:18) Choncho ndinapemphera kwambiri, kumuchonderera Yehova kuti andithandize kuti ndisiye makhalidwe omwe ndinkachita. Yehova anandithandizadi ndipo patapita nthawi, ndinasiyiratu makhalidwe oipawa. Chinthu chofunikanso kwambiri chimene ndinachita n’choti ine ndi mkazi amene ndinkakhala naye uja, tinakalembetsa ukwati wathu kuboma.

Kutsatira mfundo za m’Baibulo n’komwe kwandithandiza kuti ndikhale ndi moyo mpaka pano

Pa nthawiyi, n’kuti ndili ndi zaka 24 ndipo ndinali ndi ana atatu. Ndinafunika kupeza ntchito kuti ndizitha kusamalira banja langa. Koma ndinali wosaphunzira komanso ndinalibe mapepala alionse omwe akanandithandiza kupeza ntchito. Choncho ndinamupemphanso Yehova kuti andithandize, ndipo ndinayamba kufufuza ntchito. Ndinkauza mabwana kuti ndikuyesetsa kusintha moyo wanga ndipo akandilemba ntchito, ndizigwira mokhulupirika. Nthawi zina, ndinkawafotokozeranso kuti ndikuphunzira Baibulo ndipo ndikufuna kukhala nzika yabwino. Komabe mabwana ambiri ankakana kundilemba ntchito. Koma tsiku lina nditapita kukafunsidwa mafunso ndi abwana a pakampani inayake yomwe ndinafunsirapo ntchito, ndinawafotokozera mbiri yanga. Pomaliza, bwanawo anati: “Ndaganiza kuti ndikulembe ntchito, ngakhale kuti sindikudziwa kuti n’chiyani chandipangitsa kuganiza zimenezi.” Ndinaona kuti apa Mulungu wayankha pemphero langa. Patapita nthawi, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Ndikuona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’komwe kwandithandiza kuti ndikhale ndi moyo mpaka pano. Panopa ndili ndi banja labwino ndipo ndine wosangalala chifukwa chodziwa kuti Yehova anandikhululukira zoipa zomwe ndinkachita.

Kwa zaka 14 tsopano, ndakhala ndikuthera maola 70 mwezi uliwonse ndikuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Ndipo posachedwapa mkazi wanga anayambanso kuchita utumikiwu. Pa zaka zoposa 30 ndathandiza anzanga akuntchito okwana 22, kuti nawonso ayambe kutumikira Yehova. Nthawi zina ndimapita m’malo oimika magalimoto kunja kwa mashopu akuluakulu koma sindipita kukabera anthu. Ndimapita kukawauza za uthenga wabwino woti posachedwapa sikudzakhalanso anthu akuba mwachinyengo.—Salimo 37:10, 11.