NKHANI YA PACHIKUTO | KODI A MBONI ZA YEHOVA NDI ANTHU OTANI?
Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani?
A Mboni za Yehovafe timakhulupirira kuti, “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Timaphunzira zokhudza Mulungu kudzera m’Baibulo ndipo zinthu zimene timaphunzirazo zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino.
Baibulo limanenanso kuti: “Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Choncho, popeza ndife Mboni za Yehova, timalambira Yehova yekha komanso timathandiza ena kudziwa dzina lakeli.—Yesaya 43:10-12.
Komanso, popeza ndife Akhristu, timakhulupirira kuti Yesu amene ndi “Mwana wa Mulungu,” * m’mbuyomu anabwera padzikoli n’kudzakhala Mesiya. (Yohane 1:34, 41; 4:25, 26) Kenako anaphedwa ndipo Yehova anamuukitsa n’kupita kumwamba. (1 Akorinto 15:3, 4) Patapita nthawi, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15) Ufumu umenewu ndi boma lenileni ndipo udzathandiza kuti dzikoli likhalenso Paradaiso. (Danieli 2:44) Baibulo limati: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11, 29.
Mtsogoleri wina wa Katolika, dzina lake Benjamin Cherayath, anafotokoza m’nyuzipepala ina ya ku Germany, kuti: “A Mboni amakhulupirira kuti Mulungu amawalankhula kudzera m’Baibulo. Moti akakumana ndi vuto linalake amagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kuti adziwe chochita. . . . Amaona kuti mawu a Mulungu ndi amphamvu komanso othandiza.”—Münsterländische Volkszeitung
A Mboni za Yehovafe timakhulupiriranso kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza ngakhale masiku ano. (Yesaya 48:17, 18) Choncho, timayesetsa kutsatira malangizo amenewo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti tiyenera kupewa zinthu zomwe zingasokoneze maganizo athu komanso zomwe zingapangitse kuti tisakhale oyera. N’chifukwa chake sitisuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. (2 Akorinto 7:1) Timapewanso kuchita zinthu zomwe Baibulo limaletsa monga kuledzera, kuchita chiwerewere komanso kuba.—1 Akorinto 6:9-11.
^ ndime 5 Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu” chifukwa ndi amene Mulungu anayambirira kumulenga komanso sanatume aliyense kuti amulenge, koma anamulenga yekha.—Yohane 3:18; Akolose 1:13-15.