TAPANI VIITALA | MBIRI YA MOYO WANGA
Kukwaniritsa Cholinga Changa Chofuna Kuthandiza Anthu Avuto Losamva
Nditangokumana ndi a Mboni za Yehova kwa nthawi yoyamba, anandionetsa lonjezo la m’Baibulo lomwe limati “makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.” (Yesaya 35:5) Koma chifukwa choti ndinabadwa ndi vuto losamva, zinkandivuta kuyerekezera kuti phokoso limamveka bwanji. Chifukwa cha zimenezi, lonjezoli silinandifike pamtima. Koma zinandikhudza mtima kwambiri pomwe anandionetsa kuchokera m’Baibulo kuti Ufumu wa Mulungu udzachotsa zinthu zonse zopanda chilungamo, nkhondo, matenda komanso imfa. Patapita nthawi, ndinayamba kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuuza anthu ena avuto ngati langali zomwe ndinaphunzirazi.
Ndinabadwa m’chaka cha 1941 ku Virrat m’dziko la Finland. Makolo anga komanso achibale athu ambiri kuphatikizapo azing’ono anga analinso ndi vuto losamva. Tinkalankhulana pogwiritsa ntchito chilankhulo chamanja.
Ndinaphunzira Nkhani Zosangalatsa M’Baibulo
Kusukulu yaboding’i yomwe ndinkaphunzira, sankatilola kulankhula ndi manja. Sukuluyi inali pamtunda wa makilomita 240 kuchokera kwathu. Nthawi imeneyo, sukulu za anthu avuto losamva za ku Finland zinkakakamiza anthu kuti azilankhula ndi pakamwa komanso kuyang’anitsitsa mmene pakamwa pakuyendera. Aphunzitsi akangotipeza tikulankhulana ndi manja, ankatimenya kwambiri ndi lula kapena ndodo moti zala zathu zinkakhala zotupa kwa masiku angapo.
Nditamaliza sekondale, ndinapita kukoleji yophunzitsa zaulimi. Makolo anga anali ndi famu ndiye ndinkafuna kuphunzira zokhudza ulimi. Nditabwerera kunyumba pa holide, ndinapeza magazini a Nsanja ya Olonda komanso Galamukani! patebulo. Bambo anandiuza kuti magazini amenewa ali ndi nkhani zosangalatsa za m’Baibulo. Anandiuzanso kuti iwowo ndi amayi ankaphunzitsidwa Baibulo ndi banja lina. Popeza banjali linkamva komanso kulankhula bwinobwino, powaphunzitsa, ankachita kulemberana papepala.
Bambo anandiuza kuti Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, dzikoli lidzakhala lokongola ndipo akufa adzaukitsidwa. Koma ine zomwe ndinkadziwa ndi zakuti anthu akafa amapita kumwamba. Choncho ndinaganiza kuti bambo sanamvetse zomwe Amboniwo ankanena chifukwa sankalankhula nawo m’chilankhulo chamanja.
Banja lija litabweranso kudzaphunzira ndi makolo anga, ndinawafunsa zomwe bambo anandiuza zija. Iwo ananditsimikizira kuti zomwe bambo anandiuzazo zinalidi zoona. Kenako anandionetsa zomwe Yesu ananena zokhudza kuukitsidwa kwa akufa pa Yohane 5:28, 29. Anandilongosolera mmene Mulungu adzachotsere zinthu zoipa padzikoli. Anandiuzanso kuti anthu adzakhala padzikoli kwamuyaya, mwamtendere komanso ndi moyo wathanzi.—Salimo 37:10, 11; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:1-4.
Ndinkafuna kudziwa zambiri. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Wamboni wina dzina lake Antero yemwe ankamva komanso kulankhula bwinobwino. Antero sankadziwa chilankhulo chamanja, choncho ndinkayankha mafunso a m’buku lomwe tinkaphunziralo pochita kulemba papepala. Iye akawerenga mayankhowo, ankalembanso mafunso ena kapena ndemanga. Antero ankandiphunzitsa moleza mtima kwa maola awiri wiki iliyonse.
Mu 1960, ndinapita kumsonkhano wa Mboni za Yehova womwe unkamasuliridwa m’chilankhulo chamanja. Lachisanu masana, kunaperekedwa chilengezo choti ubatizo uchitika mawa lake. Choncho Loweruka m’mawa, ndinatenga zovala zanga zosambirira komanso thaulo ndipo ndinabatizidwa. a Patapita nthawi yochepa, makolo anga komanso azing’ono anga nawonso anabatizidwa.
Kuuza Ena Choonadi cha M’Baibulo
Ndinkafuna kuti zomwe ndaphunzirazo ndiziuzakonso anthu ena avuto losamva. Ndipo njira yosavuta yowauzira inali kugwiritsa ntchito chilankhulo chamanja. Poyamba, ndinkachita khama kulalikira anthu a m’dera lathu.
Posakhalitsa ndinasamukira kutauni yaikulu ku Tampere. Kumeneko ndinkayenda khomo ndi khomo kusakasaka anthu avuto losamva. Ndikapeza eni khomo ndinkawafunsa ngati akudziwako munthu aliyense wavutoli. Mwanjira imeneyi, ndinayambitsa maphunziro a Baibulo ndipo patangotha zaka zochepa, ku Tampere kunali ofalitsa avuto losamva opitirira 10.
Mu 1965, ndinakumana ndi mlongo wabwino kwambiri dzina lake Maire ndipo tinakwatirana m’chaka chotsatira. Maire anaphunzira chilankhulo chamanja mofulumira kwambiri ndipo kwa zaka 50 zomwe tinatumikira Yehova limodzi, iye anali mnzanga wokhulupirika komanso wakhama kwambiri.
Patatha zaka ziwiri titakwatirana, tinakhala ndi mwana wamwamuna dzina lake Marko ndipo sanabadwe ndi vuto losamva. Iye ankalankhula Chifinishi komanso Chilankhulo Chamanja cha ku Finland. Marko anabatizidwa ali ndi zaka 13.
Pamene nthawi inkapita, anthu ambiri analowa m’gulu la chilankhulo chamanja ku Tampere. Choncho pofika chaka cha 1974, tinasamukira mumzinda wa Turku komwe kunalibe Amboni avuto losamva. Kumenekonso tinayamba kupita khomo ndi khomo kufufuza anthu avutoli. Pa zaka zomwe tinali ku Turku, anthu 12 omwe tinkaphunzira nawo Baibulo anabatizidwa.
Kutumikira M’mayiko Ena a ku Europe
Mu 1987, Marko anaitanidwa kuti akatumikire pa Beteli. Gulu lathu la chilankhulo chamanja la ku Turku linali litakhazikika ndiye tinaganiza zosamukiranso dera lina.
Pa nthawiyi, ku Europe kunali magawo ambiri omwe ankafunikira kulalikidwa. Choncho mu January 1992, ine ndi m’bale wina wavuto losamva tinapita ku Tallinn m’dziko la Estonia.
Kumeneko tinakakumana ndi mlongo wina amene mchimwene wake anali ndi vuto losamva. Ngakhale kuti mchimwene wakeyo sanachite chidwi ndi uthenga wa Ufumu, iye anatithandiza kwambiri kuti tikumane ndi anthu ambiri avuto losamva ku Estonia. Usiku woti tinyamuka mawa lake, iye anatitengera kumsonkhano womwe ankachititsa ndi a Bungwe la Anthu Avuto Losamva ku Tallinn. Tinafika mofulumira ndipo tinadzaza patebulo ndi magazini komanso mabuku a Chiesitoniya ndi Chirasha. Tinagawira mabuku 100 ndi magazini 200 komanso tinalemba maadilesi a anthu pafupifupi 70. Uku kunali kuyambika kwa utumiki wa m’chilankhulo chamanja ku Estonia.
Patangotha nthawi yochepa, ine ndi Maire tinayamba kumapita ku Estonia pafupipafupi. Tinachepetsa nthawi yomwe tinkagwira ntchito n’kuyamba kuchita upainiya wokhazikika. Mu 1995, tinasamukira chakufupi ndi ku Helsinki kuti tisamavutike tikafuna kupita ku Tallinn pa sitima. Utumiki wa ku Estonia unali wokoma kwambiri kuposa mmene tinkaganizira.
Tinapeza anthu ambiri omwe tinkaphunzira nawo Baibulo. Ndipo 16 mwa anthu amenewa anapita patsogolo mpaka kubatizidwa. Anthuwa akuphatikizapo alongo awiri a pa chibale omwenso anali ndi vuto losamva komanso kuona. Pophunzira nawo Baibulo, ndinkawalankhula ndi manja kwinaku nditawagwira mikono.
Kuphunzira ndi anthu avuto losamva inali ntchito yaikulu chifukwa panthawiyo kunalibe zinthu zophunzirira za m’chilankhulochi. Ndiye kuti ndikwanitse kuwaphunzitsa, ndinkagwiritsa ntchito kwambiri buku lapadera lomwe ndinamatamo zithunzi za m’mabuku athu.
Ofesi ya nthambi ya ku Finland, inandipempha kuti ndipite ku Latvia ndi ku Lithuania kuti ndikafufuze zomwe tingachite pofuna kuthandiza anthu avuto losamva opezeka m’mayiko amenewa. Tinapita m’mayikowa maulendo angapo kuti tikathandize abale ndi alongo kufufuza anthu avuto losamva. Pafupifupi dziko lililonse linali ndi chilankhulo chakechake chamanja. Choncho ndinaphunzira chilankhulo chamanja cha ku Estonia, Latvia ndi ku Lithuania kuphatikizaponso Chilankhulo Chamanja cha ku Russia chomwe chimalankhulidwa ndi nzika za ku Russia zokhala m’mayikowa.
N’zomvetsa chisoni kuti pambuyo popita ku Estonia mobwerezabwereza kwa zaka 8, mkazi wanga Maire anamupeza ndi matenda a muubongo opha ziwalo. Choncho tinaima kaye utumiki wathu.
Njira Yothandizira Anthu Avuto Losamva
Mu 1997, gulu lomasulira zinthu m’chilankhulo chamanja linakhazikitsidwa pa Nthambi ya Finland. Chifukwa choti tinkakhala chapafupi, ine ndi Maire tinkathandiza nawo kukonza zinthu za m’chilankhulochi ndipo ndimachitabe zimenezi mwa apo ndi apo. Tinkagwiranso ntchito ndi mwana wathu Marko. Patapita nthawi, iye ndi mkazi wake Kirsi, anayamba kuphunzitsa magulu omasulira zilankhulo zamanja m’mayiko ena.
Kuwonjezera pamenepa, ofesi ya nthambi inakonza zoti iziphunzitsa abale ndi alongo omwe alibe vuto losamva kuti adziwe chilankhulo chamanja. Chifukwa cha maphunzirowa, anthu ambiri anayamba kusonkhana m’mipingo ya chilankhulochi ndipo akuthandiza pa ntchito yolalikira, kutsogolera misonkhano komanso kukhala ndi maudindo.
Ndidakali ndi Mtima Wofuna Kuthandiza
Mu 2004, ine ndi Maire tinathandiza nawo pa ntchito yokhazikitsa mpingo woyamba wa chilankhulo chamanja ku Helsinki m’dziko la Finland. Pambuyo pa zaka zitatu, mpingowu unali ndi abale ndi alongo ambiri akhama komanso apainiya ambiri.
Kenako tinaganizanso zosamukira kudera lina lomwe linkafunika olalikira ambiri. Mu 2008, tinasamukira chakufupi ndi mzinda wa Tampere ndipo tinabwereranso ku gulu la chilankhulo chamanja lomwe tinalisiya zaka 34 m’mbuyomo. Patatha chaka, gululi linakhala mpingo wachiwiri wa chilankhulo chamanja ku Finland.
Panthawiyo, thanzi la Maire linayamba kufookerafookera. Ndinayesetsa kumusamalira mpaka pamene anamwalira mu 2016. Ngakhale kuti ndimamusowa kwambiri, ndikuyembekezera kudzakumana nayenso m’dziko latsopano momwe simudzakhalanso kudwala.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4.
Ndidakali ndi mtima wofuna kulalikira anthu avuto losamva omwe ndimakhala nawo pafupi. Ndipo imeneyi ndi ntchito yomwe ndakhala ndikugwira kwa zokwanira 60.
a Panthawiyi dongosolo loti akulu azikumana kaye ndi munthu amene akufuna kubatizidwa lisanayambe.