KHALANI MASO
Kodi Aramagedo Idzayambira ku Isiraeli?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Baibulo likamatchula za Aramagedo, limanena za nkhondo yomwe maboma a padziko lonse adzamenyane ndi Mulungu, osati nkhondo yongochitika dera linalake padzikoli.
“Mauthenga ouziridwa ndi ziwanda . . . akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitse pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse. Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼChiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16.
Mawu akuti “Aramagedo,” anachokera ku mawu a Chigiriki akuti Har Meghid·dohnʹ omwe amatanthauza “Phiri la Megido.” Megido, unali mzinda womwe unkapezeka m’chigawo china cha dziko la Isiraeli. Pa chifukwa chimenechi, anthu ena amakhulupirira kuti nkhondo ya Aramagedo idzachitikira ku Isiraeli. Komatu m’dera la Megido kapenanso ku Middle East konse, kulibe dera lomwe “mafumu a dziko lonse lapansi” ndi magulu awo ankhondo angakwaneko.
Buku la Chivumbulutso linalembedwa pogwiritsa ntchito “zizindikiro” kapena kuti mawu ophiphiritsa. (Chivumbulutso 1:1) Choncho Aramagedo si malo enieni, koma ndi mawu oimira nkhondo imene mayiko a padziko lonse adzachite zinthu zolimbana ndi ulamuliro wa Mulungu komaliza.—Chivumbulutso 19:11-16, 19-21.