Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Pakachitika Ngozi Zam’chilengedwe?
Kodi muli m’gulu la anthu mamiliyoni ambiri amene akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe? Ngozi zam’chilengedwe komanso mavuto amene amabwera chifukwa cha ngozizi amakhala osiyanasiyana. Mphepo zamkuntho zingawononge zinthu zambiri komanso kuchititsa kuti madzi asefukire. Mvula ikagwa kwambiri nthaka ikhoza kugumuka komanso kungakhale mphenzi zomwe zingayambitse moto. Chilala, kutentha kwambiri komanso sinowo zingawonongenso zinthu zambiri.
M’madera ambiri, ngozi zam’chilengedwe zikuchulukirachulukirabe. Bungwe lina linati: “Chiwerengero cha anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe chikukwera kwambiri. Chaka chilichonse, ngozi monga kusefukira kwa madzi, mphepo zamkuntho ndi chilala zikuchititsa kuti anthu azivutika kupeza zofunika pa moyo, zikuwononga nyumba zawo komanso zikuwapha kumene.”—International Federation of Red Cross and Red Crescent Societies.
Ngozi ngati zimenezi zikachitika, anthu amakumana ndi mavuto ambiri komanso amavutika maganizo. Mwachitsanzo, nyumba kapena zinthu zawo zikhoza kuwonongeka komanso akhoza kuferedwa.
Ngati mwakhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe, Baibulo lingakuthandizeni. Lathandiza anthu ambiri amene akhudzidwa ndi ngozizi powalimbikitsa, kuwapatsa chiyembekezo komanso malangizo anzeru. (Aroma 15:4) Limayankhanso funso limene lathetsa nzeru anthu ambiri lomwe n’lakuti: N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti zimenezi zichitike? Kodi akundilanga?
Ngozi zam’chilengedwe si chilango chochokera kwa Mulungu
Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu sachititsa kuti anthu azivutika. Limatitsimikizira kuti Mulungu “sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Mfundoyi ikusonyeza kuti Mulungu sachititsa ngozi zam’chilengedwe.
N’zoona kuti Baibulo limanena za nthawi zimene Mulungu ankagwiritsa ntchito mphamvu zam’chilengedwe kuti alange anthu oipa. Koma zimene Mulungu ankachitazi zinali zosiyana ndi ngozi zam’chilengedwe zamasiku ano. Zili choncho chifukwa ngozizi zimabwera mwadzidzidzi ndipo zimapha anthu oipa ndi abwino omwe. Pomwe nthawi zonse, Mulungu ankateteza anthu abwino, ankachenjeza anthu asanawalange ndipo ankafotokoza chifukwa chake akuwalanga. Mwachitsanzo, Mulungu anafotokoza chifukwa chake akubweretsa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa, anachenjeza anthu pasadakhale komanso anateteza Nowa ndi banja lake.—Genesis 6:13; 2 Petulo 2:5.
Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene timadziwira kuti ngozi zam’chilengedwe si chilango chochokera kwa Mulungu, onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?”
Mulungu amamvera chisoni anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe
Baibulo limasonyeza kuti Yehova a Mulungu amatimvera chisoni komanso amatichitira chifundo. Taganizirani mavesi olimbikitsawa:
Yesaya 63:9: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, [Mulungunso] anali kuvutika.”
Mfundo yake: Yehova amakhudzidwa kwambiri akaona anthu akuvutika.
1 Petulo 5:7: “Amakuderani nkhawa.”
Mfundo yake: Yehova amafuna kuti zinthu zikuyendereni bwino.
Yehova amatithandiza chifukwa ndi wachifundo. Iye amatilimbikitsa pogwiritsa ntchito Baibulo lomwe lili ndi malangizo anzeru komanso malonjezo odalirika okhudza nthawi imene sikudzakhalenso ngozi zam’chilengedwe.—2 Akorinto 1:3, 4.
Nthawi imene sikudzakhalenso ngozi zam’chilengedwe
M’Baibulo, Yehova amatilonjeza kuti adzatipatsa “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yeremiya 29:11) Iye amafuna kuti anthu adzakhale padziko lokongola popanda kuopa kuti kungachitike ngozi zam’chilengedwe.—Genesis 1:28; 2:15; Yesaya 32:18.
Mulungu adzachititsa kuti zimenezi zitheke pogwiritsa ntchito Ufumu wake, womwe ndi boma lakumwamba lomwe Yesu ndi Mfumu yake. (Mateyu 6:10) Yesu ali ndi nzeru komanso mphamvu zoletsera ngozi zam’chilengedwe. Paja ali padziko lapansi, anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zolamulira nyengo. (Maliko 4:37-41) Iye adzalamulira momvetsa zinthu komanso mwanzeru ndipo adzaphunzitsa anthu mmene angamasamalirire dzikoli komanso kukhala mwamtendere ndi zinthu zam’chilengedwe. (Yesaya 11:2) Yesu akamalamulira, anthu sadzavutikanso ndi ngozi zam’chilengedwe.
Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndi liti pamene Yesu adzayambe kulamulira nyengo?’ Kuti mupeze yankho la funsoli, onani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?”
Zimene zingatithandize pakachitika ngozi zam’chilengedwe
Malangizo a m’Baibulo angatithandize pasanachitike ngozi zam’chilengedwe, pamene zikuchitika komanso pambuyo pake.
Pasanachitike: Konzekerani kuti mudzachitepo kanthu mwamsanga.
Zimene Baibulo limanena: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miyambo 22:3.
Mfundo yake: Muganizire zimene zingadzachitike kuti mudzachite zinthu mwamsanga poteteza banja lanu.
Zimene ena anakumana nazo: “Tsiku limene tinathawa moto, tinali titakonzekera. Tinali ndi zikwama zathu zokhala ndi zinthu zofunika pakafunika kuthawa mwadzidzidzi. Tinalinso ndi mankhwala athu komanso zovala. Anthu otizungulira ankapanikizika ndipo ankalephera kuganiza bwino. Koma ife tinali ndi zonse zofunika. Ndikuthokoza kwambiri zimenezi.”—Tamara, ku California ku United States
Pamene zikuchitika: Muziganizira zinthu zofunika.
Zimene Baibulo limanena: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
Mfundo yake: Moyo ndi wofunika kuposa zinthu.
Zimene ena anakumana nazo: Pamene mphepo yamkuntho yotchedwa Lawin b inawononga nyumba yathu, ndinathedwa nzeru. Koma ndinapemphera kwa Yehova Mulungu kuchokera pansi pa mtima. Ndinazindikiranso kuti tinangotaya zinthu osati miyoyo yathu.”—Leslie, ku Philippines.
Pambuyo pake: Muziganizira za lero osadera nkhawa za mawa.
Zimene Baibulo limanena: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.
Mfundo yake: Musamadere nkhawa kwambiri za mavuto amene angadzabwere m’tsogolo.
Zimene ena anakumana nazo: Pambuyo poti mphepo yamkuntho yotchedwa Irma inachititsa kuti madzi asefukire m’nyumba yanga, ndinapanikizika kwambiri chifukwa chofunikira kusankha zochita pa nkhani zambiri. Ndinkayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo oti ndisamade nkhawa za mawa. Ndinaona kuti Yehova akandithandiza ndikhoza kupirira zinthu zambiri kuposa mmene ndinkaganizira.”—Sally, ku Florida ku United States.
Kuti mupeze mfundo zina zothandiza, onani nkhani yakuti “Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi.”
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.
b Dzina lina la mphepo yamkunthoyi ndi Haima.