Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Pa ziganizo zotsatirazi,

NDI CHITI CHOMWE MUKUONA KUTI NDI CHOLONDOLA?

  1. ZAMOYO ZINACHITA KUSINTHA KUCHOKERA KU ZINTHU ZINA

  2. ZAMOYO ZINACHITA KULENGEDWA

 Anthu ena angaganize kuti asayansi anganene kuti chiganizo cholondola ndi choyambacho, pomwe anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu angati cholondola ndi chachiwiricho.

 Komatu si asayansi onse omwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

 Zoona zake n’zakuti pali anthu ambiri ophunzira kuphatikizapo asayansi ena omwe amakayikira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

 Mwachitsanzo, pulofesa wina wa tizilombo dzina lake Gerard, yemwe panthawi imene anali ku koleji anaphunzitsidwa zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, anati: “Polemba mayeso, ndinkalemba zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina koma sikuti ndinkazikhulupirira. Ndinkangolemba zimenezi n’cholinga choti ndikhoze.”

 Koma kodi n’chifukwa chiyani asayansi ena zimawavuta kukhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina? Kuti tiyankhe funsoli, choyamba tiyeni tikambirane mafunso amene amazunguza mutu akatswiri akachita kafukufuku pa nkhaniyi. Mafunso ake ndi awa: (1) Kodi moyo unayamba bwanji? (2) Kodi mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo inachokera kuti?

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

 ZIMENE ANTHU ENA AMANENA. Zinthu zamoyo zinachokera ku zinthu zopanda moyo.

 N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA SAKHULUPIRIRA ZIMENEZI? Panopa asayansi amadziwa zambiri zokhudza mmene zinthu zamoyo zimapangidwira, koma amalephera kumvetsa mmene chinthu chopanda moyo chingasinthire n’kukhala chamoyo. Komanso pali kusiyana kwakukulu pakati pa zamoyo ndi zopanda moyo.

 Akatswiri asayansi sadziwa bwino mmene zinthu padzikoli zinalili zaka mabiliyoni ambiri apitawo. Ndipo amasiyana maganizo pa nkhani ya kumene moyo unayambira. Ena amaganiza kuti unayambira pa chiphalaphala chochokera pansi pa nthaka, pomwe ena amaganiza kuti unayambira pansi pa nyanja. Enanso amakhulupirira kuti moyo unayambira m’mlengalenga ndipo unafika padzikoli kudzera m’miyala yomwe inagwa kuchokera m’mlengalengamo. Koma zimenezi sizikuyankha funso lakuti moyo unayamba bwanji. Zikungosonyeza malo amene asayansi amaganiza kuti moyo unayambira.

 Asayansiwa amaganiza kuti panali tizinthu tinatake totchedwa mamolekyu tomwe tinasintha n’kukhala malangizo okhudza mmene chinthu chiyenera kuonekera. Amakhulupirira kuti mamolekyuwa omwe anali a zinthu zopanda moyo ankatha kusintha komanso kuchulukana paokha. Komabe asayansi amalephera kupeza umboni woti mamolekyuwa analipodi ndipo ayeserapo kupanga mamolekyu ngati amenewa koma alephera.

 Zamoyo n’zosiyana kwambiri ndi zopanda moyo chifukwa zili ndi maselo omwe amatha kusunga ndi kugwiritsa ntchito malangizo. Maselo amatha kusamutsa, kutanthauzira komanso kugwiritsa ntchito malangizo okhudza mmene chinthu chiyenera kuonekera. Asayansi ena amayerekezera malangizowa ndi mapulogalamu a kompyuta, pomwe zinthu zosiyanasiyana zomwe zimapezeka mu selo amaziyerekezera ndi zipangizo zonse za kompyutayo. Koma amene amakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amalephera kufotokoza kuti malangizowa amachokera kuti.

 Kuti selo lizigwira bwino ntchito limafunika mamolekyu okhala ndi mapuloteni. Molekyu iliyonse imakhala ndi tizinthu tinanso ndipo tizinthu timeneti timasanjidwa mogometsa kwambiri. Komanso mamolekyu amenewa amafunika kupindika mwa njira inayake kuti azitha kugwira bwino ntchito. Poona zonsezi asayansi ena amaona kuti sizingangochitika zokha kuti molekyu imeneyi ipangidwe mogometsa chonchi. Wasayansi wina, dzina lake Paul Davies anati: “Popeza kuti selo limafunikira mapuloteni ambirimbiri a mitundu yosiyanasiyana kuti lizigwira bwino ntchito, zingakhale zosamveka kuganiza kuti maselo anangokhalako mwangozi.”

 MFUNDO YAKE. Ngakhale kuti asayansi apanga kafukufuku kwa zaka zambiri m’zinthu zosiyanasiyana, zoona zake n’zakuti zinthu zamoyo zimachokera ku zinthu zamoyo zokha.

Kodi Mitundu Yosiyanasiyana ya Zamoyo Inachokera Kuti?

 ZIMENE ANTHU ENA AMANENA. Zamoyo zosiyanasiyana kuphatikizapo anthufe, zinachokera ku chinthu chamoyo choyambirira chomwe chinkasintha pang’onopang’ono potengera nyengo komanso mmene zinthu zinalili pamalowo.

 N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA SAKHULUPIRIRA ZIMENEZI? Chinthu chilichonse chamoyo chimakhala ndi maselo wamba komanso maselo ena ogometsa kwambiri. Buku lina linafotokoza kuti mmene maselo wamba amasinthira n’kukhala maselo ogometsa kwambiri “ndi nkhani inanso yovuta kumvetsa kuwonjezera pa nkhani yakuti zinthu zamoyo zinakhalako bwanji.”

 Asayansi apeza kuti mu selo lililonse muli mamolekyu ogometsa a mapuloteni amene amagwira ntchito zosiyanasiyana zomwe n’zovuta kuzimvetsa. Ntchito zake ndi monga kutumiza chakudya chomwe chagayidwa kumbali zosiyanasiyana zathupi ndiponso kuchisintha kuti chikhale mphamvu, kukonza mbali za maselo zomwe zawonongeka komanso kupereka mauthenga ku selo. Ndiye kodi zingakhale zomveka kunena kuti maselo omwe amachita zinthu zonsezi anachita kusintha kuchokera ku zinthu zina? Ambiri amaona kuti zimenezi n’zosatheka.

 Moyo wa nyama ndi anthu umayambika dzira likakumana ndi umuna. Dziralo limakhala ndi maselo ndipo maselowo amayamba kuchulukana. Zikatere, maselowo amayamba kuoneka mosiyanasiyana ndipo amapanga mbali za thupi. Chikhulupiriro choti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, sichingafotokoze kuti selo lililonse limadziwa bwanji kuti likhale chiwalo chanji komanso kuti liyenera kupita kuti m’thupi la chamoyo chilichonse.

 Panopa asayansi atulukira zoti, kuti nyama isinthe n’kukhala yamtundu wina, pangafunike kuti mamolekyu omwe ali mkati mwa maselo a nyamayo asinthe. Popeza kuti asayansi sangapereke umboni woti selo ”wamba” likhoza kupangika posintha kuchokera ku chinthu chopanda moyo, ndiye kodi zingakhale zomveka kuti nyama zosiyanasiyana zomwe zili padzikoli zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo? Ponena za mmene zinyama zinapangidwira, wasayansi wina dzina lake Michael Behe, ananena kuti ngakhale kuti anthu ochita kafukufuku “anapeza zinthu zogometsa kwambiri zomwe sankayembekezera, palibe amene anapitiriza kufufuza kuti amvetse mmene zinthu zogometsazi zinasinthira zokha popanda munthu wina wanzeru kuzilenga.”

 Anthu amatha kuzindikira zomwe zikuchitika komanso kudziwa bwino mmene alili, amatha kuganiza asanachite zinthu, ndiponso ali ndi makhalidwe monga kuwolowa manja, kudzipereka pothandiza ena, komanso kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera kuchita. Chikhulupiriro choti anthu anachokera ku chamoyo choyambirira chomwe chinkasintha pang’onopang’ono potengera nyengo komanso mmene zinthu zinalili pamalowo, sichingafotokoze kuti zinatheka bwanji kuti anthu akhale ndi makhalidwe apadera amenewa.

 MFUNDO YAKE. Ngakhale kuti asayansi ambiri amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina, asayansi ena sakhutira ndi zimene chiphunzitsochi chimafotokoza pa nkhani yakuti moyo unayamba bwanji komanso kuti mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo inachokera kuti.

Baibulo Lili Ndi Mayankho Ogwira Mtima

 Anthu ambiri akaganizira umboni womwe ulipo amaona kuti payenera kukhala winawake wanzeru amene analenga zonse. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi pulofesa wina dzina lake Antony Flew, yemwe poyamba ankalimbikitsa chikhulupiriro choti kulibe Mulungu. Koma anasintha maganizo ake ataphunzira za kugometsa kwa moyo komanso malamulo amene zinthu za m’chilengedwe zimayendera. Flew analemba mfundo yomwe akatswiri akale anzeru za anthu ankaikhulupirira. Iye anati: “Tiyenera kuvomereza zotsatira za kafukufuku ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zomwe timayembekezera.” Pulofesayu anaona kuti pali umboni wosonyeza kuti pali Mlengi amene anapanga zinthu zonse.

 Gerard, yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino, ananenanso zofanana ndi zimenezi. Ngakhale kuti anaphunzira kwambiri komanso amagwira ntchito yofufuza za tizilombo, iye anati: “Ndimaona kuti palibe umboni wokhutiritsa wosonyeza kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina zopanda moyo. Zamoyo zimachita zinthu mwadongosolo komanso mogometsa kwambiri ndipo zimenezi zimandichititsa kukhulupirira kuti pali winawake amene anazilenga.”

 Munthu akhoza kudziwa zambiri za katswiri wojambula zithunzi poona zimene katswiriyo anajambula. Nayenso Gerard anayamba kuzindikira makhalidwe amene Mulungu ali nawo poona zimene Mulunguyo analenga. Anaphunziranso zambiri kudzera m’Mawu amene Mlengi analemba omwe ndi Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Iye anapeza mayankho ogwira mtima a mmene zinthu zinalili ndi anthu kalekalelo komanso zimene zingathandize anthu kulimbana ndi mavuto omwe akukumana nawo panopa. Zimenezi zinamupangitsa kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawudi a Mulungu.

 Zimene Gerard anapezazi zikusonyeza kuti m’Baibulo muli mayankho ogwira mtima a mafunso osiyanasiyana. Tikukulimbikitsani kuti inunso muliphunzire ndipo mudzapeza mayankho a mafunso osiyanasiyana omwe muli nawo.