Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BalanceFormcreative/iStock via Getty Images Plus

Muzithandiza Ena Kuti Musamasungulumwe​—Kodi Baibulo Limati Chiyani?

Muzithandiza Ena Kuti Musamasungulumwe​—Kodi Baibulo Limati Chiyani?

 Padziko lonse lapansi anthu akumasungulumwa komanso akumaona kuti sangathe kupeza anzawo apamtima. Akatswiri ena azaumoyo akukhulupirira kuti kuthandiza ena ndi njira yabwino yothana ndi vuto losungulumwa.

  •    “Kuthandiza anthu ovutika kungachititse kuti tikhale ndi moyo watanthauzo komanso kungatithandize kulimbana ndi maganizo odziona kuti tili tokhatokha.”​—U.S. National Institutes of Health.

 M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kudziwa zimene tingachite kuti tizithandiza anthu ena. Kugwiritsa ntchito zimene limanena kungatithandize kuti tithane ndi vuto losungulumwa.

Zimene mungachite

 Musamaumire. Muzipeza nthawi yocheza ndi anthu ena makamaka pamasom’pamaso. Musamanyinyirike kugawira anthu ena zinthu zomwe muli nazo. Mukamachita zimenezi, iwo adzayamikira kwambiri ndipo mudzakhala nawo pa ubwenzi wabwino.

  •    Mfundo ya m’Baibulo: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.”​—Luka 6:38.

 Muzidzipereka kuthandiza ena. Muzifufuza njira zimene mungathandizire anthu ena omwe akuvutika. Zimenezi zikuphatikizapo kuwamvetsera kapenanso kuwathandiza kugwira ntchito zomwe zingawachepetsereko mavuto.

  •    Mfundo ya m’Baibulo: “Mnzako amapezeka kuti akuthandize, pa zochitika zilizonse.”​—Miyambo 17:17, Contemporary English Version.

 Kuti mudziwe zambiri zomwe zingakuthandizeni kupitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi anthu ena, werengani nkhani yakuti “Banja Labwino Komanso Mabwenzi Abwino.”