Kuteteza Akazi—Zimene Baibulo Limanena
Azimayi ndi atsikana mamiliyoni ambirimbiri padziko lonse amachitiridwa nkhanza. Kodi nanunso munachitiridwapo nkhanza? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amaona kuti muyenera kutetezedwa komanso zimene adzachite pothetsa nkhanza zonse zimene anthu amachitira akazi.
“Ndili mwana, mchimwene wanga ankandimenya komanso kundilankhula mawu achipongwe tsiku lililonse. Nditakwatiwa, apongozi anga aakazi nawonso ankandichitira nkhanza. Iwo limodzi ndi apongozi anga aamuna ankachita nane zinthu ngati ndine kapolo. Zimenezi zinachititsa kuti ndikhale ndi maganizo ofuna kudzipha.”—Madhu, a India.
Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linatsimikizira kuti: “Padziko lonse, akazi ambiri amachitiridwa nkhanza.” Malinga ndi bungweli, pafupifupi mkazi mmodzi pa atatu aliwonse anachitiridwapo nkhanza zokhudza kugonana kapena nkhanza zina pa nthawi inayake pa moyo wake.
Ngati zimenezi zinakuchitikiranipo, mungamakhale ndi mantha oti kulikonse komwe mungapite anthu akhoza kukuchitirani nkhanza zokhudza kugonana kapena nkhanza zina. Nkhanza zimene anthu amachitira akazi zingakuchititseni kuyamba kuganiza mmene anthu ambiri amaganizira kuti ‘Akazi ndi osafunika.’ Koma kodi Mulungu amaona kuti akazi ndi ofunika?
Kodi Mulungu amaona bwanji akazi?
Lemba la m’Baibulo: “[Mulungu] anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Genesis 1:27.
Zimene lembali likutanthauza: Mulungu analenga amuna ndi akazi. Iye amaona kuti onse ndi oyenera kupatsidwa ulemu. Komanso, iye amayembekezera kuti mwamuna “azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha,” osati kumulamulira, kumulankhula mawu achipongwe kapenanso kumuchitira nkhanza. (Aefeso 5:33; Akolose 3:19) Uwu ndi umboni woti Mulungu amafuna kuti akazi azikhala otetezeka.
“Ndili mwana, achibale ankandigwiririra. Nditakwanitsa zaka 17, amene anandilemba ntchito ankandiopseza kuti andichotsa ntchito ngati ndingakane kugonana naye. Nditakula mwamuna wanga, makolo anga komanso maneba sankachita nane zinthu mwaulemu. Koma kenako ndinaphunzira zokhudza Mlengi wathu Yehova. b Iye amaona kuti akazi ndi oyenera kupatsidwa ulemu. Zimenezi zinanditsimikizira kuti amandikonda komanso amandiona kuti ndine munthu wofunika.”—Maria, Argentina.
N’chiyani chingakuthandizeni kuti muyambe kudziona moyenera?
Lemba la m’Baibulo: “Pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”—Miyambo 18:24.
Zimene lembali likutanthauza: Mnzanu weniweni amakhala wokonzeka kukuthandizani. Ngati n’zotheka, uzani munthu amene mumamudalira mmene mukumvera mumtima mwanu.
“Kwa zaka 20, sindinauze aliyense zoti ndinachitiridwa nkhanza zokhudza kugonana. Zimenezi zinachititsa kuti pamene ndinkakula ndizikhala wosasangalala, ndizikhala ndi nkhawa komanso ndizivutika maganizo. Koma nditafotokozera munthu wina yemwe ankafunitsitsa kundimvetsera, ndinamva ngati ndatula chimtolo cholemera.”—Elif, Türkiye.
Lemba la m’Baibulo: ‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, chifukwa amakufunirani zabwino.’—1 Petulo 5:7.
Zimene lembali likutanthauza: Mulungu amamvetsera mwatcheru mukamapemphera. (Salimo 55:22; 65:2) Popeza kuti amakuderani nkhawa, iye amafuna muzidziwa kuti ndinu ofunika kwambiri.
“Kuphunzira za Yehova kunandithandiza kuchepetsa ululu wa mumtima womwe ndinali nawo. Panopa ndimafotokozera Mulungu mmene ndikumvera kudzera m’pemphero. Iye ali ngati mnzanga amene amandimvetsa bwino.”—Ana, Belize.
Kodi Mulungu adzathetsa nkhanza zimene anthu amachitira akazi?
Lemba la m’Baibulo: ‘Yehova . . . adzaweruza mwachilungamo mwana wamasiye komanso anthu oponderezedwa, kuti munthu wamba wochokera kufumbi asadzawachititsenso mantha.’—Salimo 10:17, 18.
Zimene lembali likutanthauza: Posachedwapa, Mulungu adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo kuphatikizapo nkhanza zimene anthu amachitira akazi.
“Kudziwa kuti posachedwapa Yehova adzathetsa nkhanza zimene anthu amachitira atsikana ndi azimayi kuli ngati mankhwala ochiritsa ululu wa mumtima umene ndimamva. Panopa ndili ndi mtendere wamumtima.”—Roberta, Mexico.
Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene Baibulo lingakuthandizireni kukhala ndi chiyembekezo, chifukwa chake mungakhulupirire malonjezo ake komanso mmene a Mboni za Yehova angakuthandizireni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa, pemphani munthu kuti adzakuyendereni ndipo simudzalipira ndalama iliyonse.
Pangani dawunilodi nkhaniyi kuti muthe kupulinta pepala lake.
a Mayina ena asinthidwa.
b Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”