Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Kuwombera M’masukulu—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kuwombera M’masukulu—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pa 24 May 2022, m’tawuni ya Uvalde ku Texas m’dziko United States, munachitika zinthu zoopsa kwambiri. Nyuzipepala ina inanena kuti “munthu wina yemwe anali ndi mfuti anawombera ndi kupha ana 19 komanso aphunzitsi awiri . . . pasukulu ya pulayimale ya Robb Elementary School.”—The New York Times.

 N’zomvetsa chisoni kuti zachiwembu ngati zimenezi zikuchulukirachulukira. Nyuzipepala ina inanenanso kuti ku United States kokha, “chaka chatha ziwembu zowombera ndi mfuti zokwana 249, zinachitika m’masukulu. Chiwerengerochi ndi chokwera kwambiri kuposa zaka zonse za m’mbuyomu kuyambira mu 1970.”—USA Today.

 N’chifukwa chiyani kumachitika zachiwembu ngati zimenezi? Kodi tingatani kuti tipirire zinthu zoipa ngati zimenezi? Kodi tingayembekezere kuti zachiwawazi zidzatha? Baibulo limapereka mayankho.

N’chifukwa chiyani zachiwawa zikuchulukirachulukira?

 Anthu ena amadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu saletsa zinthu zoopsa monga zowombera m’masukulu?’ Kuti mudziwe zomwe Baibulo limanena, werengani nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?

Kodi tingatani kuti tipirire zinthu zoipa ngati zimenezi?

  •     “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa . . . amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.

 Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuti tithe kupirira zinthu zachiwawa zomwe zikuchitika m’dzikoli. Kuti mudziwe zambiri, werengani magazini ya Galamukani! yamutu wakuti, “Kodi Anthu Adzasiya Kuchitirana Zachiwawa?

 Werengani nkhani yakuti, “Kodi Mwana Wanu Amaopa Akamva za Zimene Zachitika? kuti mupeze njira zina zomwe mungathandizire mwana wanu akamachita mantha chifukwa choona kapena kumva zinthu zoopsa.

Kodi zachiwawa zidzathadi?

  •    “Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:14.

  •     “Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Mika 4:3.

 Mulungu adzachita zinthu zomwe anthu akulephera kuchita. Iye adzawononga zida zonse zankhondo komanso kuthetsa zipolowe zonse pogwiritsa ntchito Ufumu wake wakumwamba. Kuti mudziwe zambiri zomwe Ufumu wa Mulungu udzachite, werengani nkhani yakuti, “Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira ‘Padzakhala Mtendere Wochuluka.’”