Nkhondo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
Padziko lonse lapansi, anthu akukumanabe ndi mavuto osaneneka chifukwa cha nkhondo. Taonani malipoti otsatirawa:
“Chaka chatha, anthu ambiri anamwalira chifukwa cha nkhondo, makamaka zimene zinachitika ku Ethiopia ndi ku Ukraine ndipo chiwerengero cha anthu ophedwa chinaposa omwe anaphedwa zaka 28 zapitazo.”—Peace Research Institute Oslo, June 7, 2023.
“Nkhondo ya ku Ukraine ndi imodzi mwa nkhondo zimene zinali zoopsa kwambiri m’chaka cha 2022. Padziko lonse, nkhanza zimene anthu amachitirana pa zifukwa zandale zinawonjezereka ndi 27% m’chakachi poyerekezera ndi mu 2021 ndipo zimenezi zinakhudza anthu pafupifupi 1.7 biliyoni.”—The Armed Conflict Location & Event Data Project (ACLED), February 8, 2023.
Komabe, m’Baibulo muli uthenga wopatsa chiyembekezo. Limanena kuti “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa.” (Danieli 2:44) Mulungu adzagwiritsa ntchito ufumu kapena kuti boma limeneli, ‘pothetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.