Asilikari a Dziko la Russia Alowa M’dziko la Ukraine
M’mawa wa pa 24 February 2022, asilikali a dziko la Russia analowa m’dziko la Ukraine kukachita nkhondo ngakhale kuti atsogoleri a mayiko ambiri anayesetsa kuti nkhondoyi isachitike. Kodi nkhondo imeneyi ikhudza bwanji zochitika padziko lonse? Masiku angapo apitawo, António Guterres, yemwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ananena kuti: “Ndi zovuta kudziwa mmene nkhondoyi ichititsire anthu kuvutika, kuwonongeka kwa katundu komanso mmene ikhudzire chitetezo cha mayiko a ku Europe komanso padziko lonse.”
Kodi Baibulo linanena zotani zokhudza zochitika ngati zimenezi?
Yesu Khristu ananeneratu za nthawi imene “mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Werengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?” kuti muone mmene Baibulo limasonyezera kuti nkhondo zimene zikuchitika masiku ano zikukwaniritsa ulosi umene Yesu ananenawu.
Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limanena za nkhondo yomwe akuiyerekezera ndi munthu wokwera hatchi “yofiira ngati moto” ndipo akuchotsa “mtendere padziko lapansi.” (Chivumbulutso 6:4) Werengani nkhani yakuti “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?” kuti mudziwe momwe nkhondo zomwe zikuchitika masiku ano zikukwaniritsira ulosi umenewu.
Buku la Danieli linaneneratu za chidani chomwe chidzakhalepo pakati pa “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwera.” (Danieli 11:25-45) Onerani vidiyo yakuti Kukwaniritsidwa kwa Maulosi—Danieli Chaputala 11, kuti mudziwe chifukwa chake tinganene kuti dziko la Russia ndi mayiko omwe amagwirizana nalo, ndi amene ali mfumu ya kumpoto. a
Buku la Chivumbulutso limanena za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Komabe, imeneyi si nkhondo ya mayiko ngati imene ikuchitikayi. Werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhondo imeneyi imene ikubwera m’tsogolomu.
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino Kwambiri M’tsogolo?
Baibulo limanena kuti Mulungu adzathetsa “nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Salimo 46:9) Werengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo” kuti mudziwe zambiri zokhudza madalitso amene Mulungu watilonjeza.
Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba lomwe lidzakwaniritse chifuniro cha Mulungu padziko lapansi. Chifuniro cha Mulungu chimenechi chikuphatikizapo kubweretsa mtendere padziko lonse. Kuti mudziwe mmene mungapindulire chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, onerani vidiyo yakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Ku Ukraine kuli a Mboni za Yehova oposa 129,000. Mofanana ndi a Mboni za Yehova onse padziko lonse, iwo amatsatira chitsanzo cha Yesu posalowerera nawo m’nkhani zandale komanso kumenya nkhondo (Yohane 18:36) A Mboni za Yehova padziko lonse akupitirizabe kulalikira ‘uthenga wabwino uwu wa ufumu.’ Iwo amauza anthu kuti Ufumu umenewu ndi umene udzathetse mavuto amene anthu akukumana nawo kuphatikizapo nkhondo. (Mateyu 24:14) Tipezeni kuti mudziwe zambiri za uthenga wopatsa chiyembekezo womwe uli m’Baibulo.
a Kuti mudziwe zambiri za ulosiwu, werengani nkhani zakuti “‘Kodi Mfumu ya Kumpoto’ M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?” komanso yakuti “Kodi Mfumu ya Kumpoto” Ndi Ndani Panopa?”