KHALANI MASO
Anthu Sakumvera Malamulo Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Zigawenga zachititsa kuti ku Haiti kuzichitika zachiwawa zoopsa kwambiri. Zinthu zachiwawa komanso uchigawenga zikuchitika kwambiri ku South Africa, Mexico ndiponso m’mayiko ena a ku Latin America. Ngakhale m’madera amene zachiwawa sizikuchitika kwambiri, anthu amakhala mwamantha chifukwa cha kuchuluka kwa umbava.
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya kusamvera malamulo komwe kukuchita padziko lonse?
Zimene Baibulo linaneneratu zokhudza kusamvera malamulo
Baibulo linaneneratu kuti kusamvera malamulo kudzakhala chizindikiro cha “mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 24:3) Pofotokoza zinthu zimene zidzachitike monga mbali ya chizindikirochi, Yesu Khristu ananena kuti:
“Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”—Mateyu 24:12.
Baibulo linaneneratunso kuti mu “masiku otsiriza” anthu adzakhala “osadziletsa, oopsa [komanso] osakonda zabwino.” (2 Timoteyo 3:1-5) Makhalidwe amenewa ndi amene akuchititsa kuti anthu ambiri masiku ano asamamvere malamulo.
Komabe, tili ndi zifukwa zomveka zoyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino. Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa sikudzakhalanso anthu osamvera malamulo.
“Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
Phunzirani zambiri zokhudza uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo komanso chifukwa chake muyenera kukhulupirira kuti zinthu zimene zikuchitika padzikoli, zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Onani nkhani zotsatirazi.
“Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo”
“Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi ‘ya Mapeto’ N’chiyani?”
“Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?”