Kodi Baibulo Linaneneratu Zotani pa Nkhani ya Zivomerezi Zamphamvu?
Chaka chilichonse kumachitika zivomerezi zambirimbiri. Ngakhale kuti zambiri sizikhala zoopsa, koma zikakhala zamphamvu, zimawononga kwambiri moti anthu amavutika komanso kufa. Nthawi zinanso zimachititsa kusefukira kwa madzi omwe amawononga kwambiri madera a m’mbali mwanyanja. Ndipo zimenezi zikachitika, anthu ambiri amafa. Kodi Baibulo linaneneratu zokhudza zivomerezi zamphamvuzi?
Zimene zili munkhaniyi
Kodi Baibulo linaneneratu zokhudza zivomerezi zomwe zimachitika masiku ano?
Kodi zivomerezi zamasiku ano zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo?
Kodi zomwe Baibulo linaneneratu pa nkhani ya zivomerezi ziyenera kutikhudza bwanji?
Maganizo olakwika omwe anthu ena amakhala nawo pankhani ya maulosi a m’Baibulo komanso zivomerezi
Kodi Baibulo linaneneratu zokhudza zivomerezi zomwe zimachitika masiku ano?
Baibulo linaneneratu zokhudza zivomerezi mu ulosi umene Yesu ananena. Zimene Yesu ananenazi zinalembedwa motere m’mabuku atatu a m’Baibulo:
“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomerezi m’malo osiyanasiyana.”—Mateyu 24:7.
“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina. Kudzakhala zivomerezi m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.”—Maliko 13:8.
“Kudzachitika zivomerezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.”—Luka 21:11.
Yesu ananeneratu kuti kudzachitika “zivomerezi zamphamvu” “m’malo osiyanasiyana” panthawi yomwe kudzakhala kukuchitikanso nkhondo, njala komanso miliri. Zinthu zonsezi ndi zizindikiro za nthawi yomwe imatchedwa kuti “mapeto a nthawi ino” kapena kuti “masiku otsiriza.” (Mateyu 24:3; 2 Timoteyo 3:1) Tikawerengetsa bwino nthawi mogwirizana ndi zomwe Baibulo limanena, “masiku otsiriza” anayamba mu 1914 ndipo panopo tikukhala m’masiku amenewo.
Kodi zivomerezi zamasiku ano zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo?
Inde. Maulosi omwe Yesu ananena kuphatikizapo okhudza zivomerezi, akugwirizana kwambiri ndi zomwe tikuona masiku ano. Kuyambira mu 1914, padzikoli pakhala pakuchitika zivomerezi zamphamvu zopitirira 1,950 zomwe zapha anthu opitirira 2 miliyoni. a Mwachitsanzo, taonani zivomerezi zomwe zachitika m’zaka 100 zapitazi.
Mu 2004—Ku Indian Ocean. Chivomerezi champhamvu zokwana 9.1 chinachititsa kuti madzi asefukire m’mayiko ambiri ndipo anthu pafupifupi 225,000 anafa.
Mu 2008—Ku China. Chivomerezi champhamvu zokwana 7.9 chinawononga midzi ndi matawuni ndipo chinapha anthu pafupifupi 90,000 komanso kuvulaza enanso okwana 375,000. Chinachititsanso kuti anthu mamiliyoni asowe pokhala.
Mu 2010—Ku Haiti. Chivomerezi champhamvu zokwana 7.0 limodzi ndi zivomerezi zina zazing’ono zomwe zinachitika pambuyo pake, zinapha anthu opitirira 300,000 komanso kuchititsa anthu opitirira 1 miliyoni kusowa pokhala.
Mu 2011—Ku Japan. Chivomerezi champhamvu zokwana 9.0 chomwe chinachititsanso kuti madzi asefukire, chinapha anthu pafupifupi 18,500 komanso kuchititsa anthu ambiri kusowa pokhala. Malo opangira mphamvu zamagetsi a Fukushima anawonongeka ndipo mphamvu zokhala ndi poizoni zomwe zimagwiritsidwa ntchito popanga magetsiwa zinayamba kufalikira. Patatha zaka 10, anthu pafupifupi 40,000 sanakwanitsenso kubwerera kunyumba zawo zomwe zinali kufupi ndi malowa chifukwa poizoni uja anali atafalikira dera lonselo.
Kodi zomwe Baibulo linaneneratu pa nkhani ya zivomerezi ziyenera kutikhudza bwanji?
Zomwe Baibulo linaneneratu zokhudza zivomerezi, zimatithandiza kudziwa zomwe zikuyembekezeka kuchitika m’tsogolo. Paja Yesu ananena kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.”—Luka 21:31.
Baibulo limafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni lomwe lili kumwamba ndipo Mfumu yake ndi Yesu. Ufumu umenewo ndi umene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti aziupempherera kuti ubwere.—Mateyu 6:10.
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padzikoli, Mulungu adzathetsa ngozi zam’chilengedwe kuphatikizapo zivomerezi zomwe zimavulaza anthu. (Yesaya 32:18) Sizokhazo, adzachiritsanso anthu omwe anavulala pa zivomerezi zimenezi. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:3, 4) Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?”
a Ziwerengerozi anatulutsa ndi a Global Significant Earthquake Database kuchokera ku United States National Geophysical Data Center.