KHALANI MASO
Zimene Zipembedzo Zikuchita pa Nkhondo ya ku Ukraine—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Mfundo zili m’munsizi, zikusonyeza mmene atsogoleri achipembedzo akuonera nkhondo yomwe ikuchitika ku Ukraine:
Nyuzipepala ina ya pa intaneti inati: “Mtsogoleri wa Tchalitchi cha Russian Orthodox, dzina lake Kirill, sananenepo chilichonse chosonyeza kuti sakugwirizana ndi zimene boma la Russia linachita potumiza asilikali ake ku Ukraine. . . . Tchalitchi cha Orthodox chakhala chikufalitsa nkhani zabodza zokhudza dziko la Ukraine ndipo Putin, yemwe ndi pulezidenti wa dziko la Russia, wakhala akuikira kumbuyo nkhondo ya ku Ukraine pogwiritsa ntchito zomwe tchalitchichi chikunena.”—EUobserver, March 7, 2022.
Nyuzipepala ina inati: “Zimene Kirill akumanena zikusonyeza kuti akugwirizana kotheratu ndi zimene asilikali a dziko la Russia anachita pokalowa m’dziko la Ukraine. Iye ananena kuti cholinga cha nkhondoyi ndi kuthetsa zinthu zoipa zomwe zakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali.”—AP News, March 8, 2022.
Nyuzipepala ina inanena kuti: “Lolemba lapitalo, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Ukranian Orthodox, dzina lake Epiphanius I wa ku Kyiv, anadalitsa anthu n’kuwauza kuti ‘ayenera kumenyana ndi asilikali a Russia’ . . . [Iye] ananenanso kuti kupha asilikali a dziko la Russia si tchimo.”—Jerusalem Post, March 16, 2022.
Chikalata chomwe bungwe lina la zipembedzo linalemba chinati: “Ife [a Bungwe la Zipembedzo za ku Ukraine] tikugwirizana ndi asilikali a dziko la Ukraine komanso ena onse omwe akugwira ntchito yoteteza dzikoli. Anthu amenewa tikuwapempherera kuti alandire madalitso chifukwa choteteza dziko la Ukraine kwa asilikali a Russia.”—UCCRO a Statement, February 24, 2022.
Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zipembedzo zomwe zimati zimatsatira Yesu Khristu, ziyenera kumalimbikitsa anthu awo kumenya nkhondo? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?
Mbiri ya zipembedzo pa nkhani ya nkhondo
Mbiri imasonyeza kuti zipembedzo zakhala zikulola, kuikira kumbuyo komanso kulimbikitsa anthu kumenya nkhondo. Zipembedzozi zakhala zikuchita zimenezi kwinaku zikunamiza anthu kuti zimalimbikitsa mtendere. Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akubweretsa poyera chinyengo chimene zipembedzozi zimachita. Mwachitsanzo, taonani nkhani zotsatirazi, zomwe takhala tikufalitsa m’mabuku athu.
Nkhani ya Chingelezi yakuti,“The Crusades—A ‘Tragic Illusion’” inafotokoza kuti Tchalitchi cha Katolika chili ndi mlandu pa nkhani ya kuphedwa kwa anthu ambirimbiri pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso Khristu.
Nkhani yakuti, “Tchalitchi cha Katolika mu Afirika” inasonyeza mmene zipembedzo zinalepherera kuthetsa nkhondo zapachiweniweni komanso kuphedwa kwa anthu ambirimbiri osalakwa.
Nkhani zakuti, “Kodi Zipembedzo N’zimene Zikusokoneza Mtendere?,” “Mbali ya Chipembedzo m’Nkhondo za Anthu,” komanso yakuti, “Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina,” zinafotokoza mmene atsogoleri a Tchalitchi cha Katolika, Orthodox komanso Achipulotesitanti anathandizira mbali zonse zomwe zinkamenyana pa nkhondo zambirimbiri m’mbuyomu.
Kodi Akhristu ayenera kumenya komanso kuthandiza nawo nkhondo?
Zimene Yesu anaphunzitsa: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) “Pitirizani kukonda adani anu.”—Mateyu 5:44-47.
Taganizirani izi: Kodi zingakhale zomveka kuti chipembedzo chomwe chimati chimamvera zomwe Yesu analamula chizilimbikitsa anthu achipembedzocho kuti akaphe anzawo kunkhondo? Kuti mupeze yankho la funsoli, werengani nkhani yakuti, “Akhristu Oona ndi Nkhondo” komanso yakuti, “Kodi N’zotheka Kukonda Adani Athu?”
Zimene Yesu ananena: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe.” (Yohane 18:36) “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”—Mateyu 26:47-52.
Taganizirani izi: Ngati Yesu anakaniza ophunzira ake kumenyana ndi anthu omwe ankafuna kumugwira, kodi zingakhale zomveka kuti Akhristu azimenya nkhondo pa zifukwa zina? Werengani nkhani yakuti, “Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?” kuti muone mmene Akhristu oyambirira anasonyezera kuti anali okhulupirika potsatira chitsanzo cha Yesu komanso zomwe anawaphunzitsa.
Kodi n’chiyani chidzachitikire zipembedzo zomwe zimalimbikitsa nkhondo?
Baibulo limanena kuti Mulungu amadana ndi zipembedzo zomwe zimangonena ndi pakamwa pokha kuti zimatsatira Yesu, koma osamachita zomwe anaphunzitsa.—Mateyu 7:21-23; Tito 1:16.
Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti Mulungu amaona kuti zipembedzo zomwe zimachita zimenezi zili ndi mlandu wa “magazi a aneneri, a oyera, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:21, 24) Kuti mudziwe chifukwa chake, werengani nkhani yakuti, “Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?”
Yesu anasonyeza kuti zipembedzo zonse zomwe Mulungu amadana nazo, zidzawonongedwa ngati mmene zimakhalira ndi mtengo womwe umabala zipatso zowola. Paja mtengo woterewo “amaudula ndi kuuponya pamoto.” (Mateyu 7:15-20) Kuti mudziwe mmene zidzakhalire, werengani nkhani yakuti, “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira.”
Photo credits, left to right: Photo by Sefa Karacan/Anadolu Agency/Getty Images; Maxym Marusenko/NurPhoto via Getty Images
a M’Bungwe la Zipembedzo za ku Ukraine (UCCRO), muli zipembedzo zokwanira 15. Zina mwa zipembedzozi ndi monga Orthodox, Akatolika a Chiroma ndi Chigiriki, Apulotesitanti, magulu atchalitchi cha Evangelical, Ayuda komanso Asilamu.