Dziko Latsopano Lomwe Likubwera
Pangani Dawunilodi:
1. M’maganizo taonani izi:
Mukuona zinthu zochititsa chidwi
Ana ‘kusewera
M’dziko lomwe nkhawa zonse zatha.
Anthu onse okhulupirika
Akusamalira bwino dzikoli.
Kulitu chitetezo—
Ndi mtendere mpaka kalekale.
N’zosangalatsa,
Yesu akulamulira
M’dziko latsopano.
(KOLASI)
Chiyembekezo chathu
Chili ngati nangula wathu,
Chimawala ngatitu dzuwa
Ngatitu tilidi
M’dziko latsopano.
2. Taganizirani malo ake
Mapiri, mitsinje, malo okongola.
Uku ndiye kwanu.
Mukutuluka m’nyumba mwanu,
Pali wina wom’dziwa
Wofunika kum’kumbatira
Tikusangalala—
Padutsa zaka osamuona
Imfa yagonja
N’chikondi chake
M’dziko latsopano.
(KOLASI)
Chiyembekezo chathu
Chili ngati nangula wathu,
Chimawala ngatitu dzuwa
Ngatitu tilidi
M’dziko latsopano.
(VESI LOKOMETSERA)
Mawu onse wanena
Adzakwaniritsidwa ndithu.
N’chifuniro cha Yehova
Watipatsa zonse tinkafuna.
(KOLASI)
Chiyembekezo chathu
Chili ngati nangula wathu,
Chimawala ngatitu dzuwa
Ngatitu tilidi
M’dziko latsopano,
M’dziko latsopano,
M’dziko latsopano,
M’dziko latsopano.