Tili M’banja la Yehova
Pangani Dawunilodi:
1. M’dzikoli anthu anaipa,
Moti sizophweka kupeza mabwenzi.
Ndinkafunitsitsa n’tapeza anzanga
Odalirika ndi ondikondadi.
2. Lero ndawapeza, ndakhutira.
Gulutu la Yehova lero ndalipeza.
Anthu ake onse amakondana,
N’zosangalatsa, ndapeza gulu labwino.
(VESI LOKOMETSERA)
Ndapeza ’bale ndi alongo, ndi makolonso.
Ndapezatu anzanga osangalatsa
Ochokera m’mitundu ndi mayiko onse.
Timakondana, ndife banja limodzi.
3. Timadziwika ndi chikondi.
M’gulu lapaderali timasangalala.
Ndiye tikamakondana kwambiri
Mulungu wathu amasangalaladi.
(VESI LOKOMETSERA)
Tachokera m’mayiko ndi mitundu yonse.
Timakondana, ndife banja limodzi.
4. Tilitu m’gulu lapaderali,
Yehova watikoka, n’zosangalatsadi.
Tidzalowatu m’dziko latsopano
Mongadi banja la padzikotu lonse.
Monga banjatu limodzidi,
Limodzi,
Limodzi.