Kodi Baibulo la Dziko Latsopano Linamasuliridwa Molondola?
Gawo loyamba la Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi linatuluka m’chaka cha 1950. Kuyambira nthawi imeneyo anthu ena akhala akuyamikira Baibulo la Dziko Latsopano a koma ena amalikayikira chifukwa mbali zina limasiyana ndi Mabaibulo ena. Baibuloli limasiyana ndi Mabaibulo ena chifukwa cha mfundo zotsatirazi.
Ndi Lodalirika. Baibulo la Dziko Latsopano linamasuliridwa kuchokera ku mipukutu yakale yodalirika komanso linamasuliridwa mogwirizana ndi zimene akatswiri a Baibulo apeza masiku ano. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo la King James Version la mu 1611 linamasuliridwa kuchokera ku mipukutu yomwe sinali yolondola kwenikweni komanso sinali yakale kwambiri poyerekezera ndi mipukutu yomwe inagwiritsidwa ntchito pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano.
Siliwonjezera kapena kuchotsera mawu. Amene anamasulira Baibulo la Dziko Latsopano sanawonjezere kapena kuchotsera uthenga wouziridwa wochokera kwa Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Omasulira Mabaibulo ambiri samasulira molondola chifukwa chotsatira miyambo ya anthu. Mwachitsanzo amachotsa dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova n’kuikamo mayina ena audindo, monga akuti Ambuye kapena Mulungu.
Ndi lomveka bwino komanso lolondola. Mosiyana ndi Mabaibulo ena amene anamasuliridwa liwu ndi liwu, omasulira Baibulo la Dziko Latsopano ankamasulira liwu ndi liwu pokhapokha ngati kuchita zimenezo sikukanasokoneza tanthauzo lake komanso sikukanachititsa mawuwo kukhala ovuta kuwamva. Kumasulira Baibulo liwu ndi liwu kuli ndi mavuto ake chifukwa omasulirawo angaikemo maganizo awo kapena kuchotsamo mfundo zofunika.
Kusiyana kwa Baibulo la Dziko Latsopano ndi Mabaibulo ena
Mabuku amene mulibe. Mabaibulo amene anamasuliridwa ndi matchalitchi a Katolika komanso Eastern Orthodox ali ndi mabuku ena owonjezera. Komabe anthu amaona kuti mabukuwa sali m’gulu la mabuku opatulika olembedwa ndi Ayuda. Izi zili choncho chifukwa Baibulo limanena kuti Ayuda anali anthu omwe ‘mawu opatulika a Mulungu anaikidwa m’manja mwawo.’ (Aroma 3:1, 2) Chifukwa cha zimenezi, mabuku owonjezera amenewa sanaikidwe mu Baibulo la Dziko Latsopano komanso m’Mabaibulo ena.
Mavesi omwe mulibe. Omasulira Mabaibulo ena anawonjezeramo mavesi komanso mawu amene sapezeka m’mipukutu yakale ya Baibulo. Mosiyana ndi zimenezi Baibulo la Dziko Latsopano silinawonjezere mawu ena aliwonse. Choncho, omasulira Mabaibulo ena masiku ano anachotsa mavesi owonjezera amenewa kapena analemba mawu osonyeza kuti mavesiwo munalibe m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. b
Kugwiritsira ntchito mawu osiyanasiyana. Nthawi zambiri mavesi a m’Baibulo amene amasuliridwa liwu ndi liwu amakhala osamveka bwino. Mwachitsanzo pomasulira liwu ndi liwu mawu a Yesu a pa Mateyu 5:3, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limati: “Odala ali osauka mumzimu.” Anthu ambiri amaona kuti mawu akuti “osauka mumzimu” ndi ovuta kumvetsa ndipo ena amaganiza kuti Yesu ankanena za kufunika kokhala munthu wodzichepetsa kapena wosauka. Komatu apa Yesu ankatanthauza kuti munthu angapeze chimwemwe chenicheni ngati akutsogoleredwa ndi Mulungu. Choncho Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira mawu a Yesu amenewa molondola, ponena kuti “anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3. c
Zinthu zabwino zimene akatswiri a maphunziro omwe si a Mboni ananena zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano
Katswiri wa maphunziro komanso womasulira Baibulo dzina lake Edgar J. Goodspeed analemba mawu otsatirawa ponena za Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, m’kalata yake ya pa December 8, 1950. “Ndimachita chidwi ndi ntchito yanu yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse komanso ndimachita chidwi kwambiri ndi Baibulo lanu lomasuliridwa molondola ndiponso momveka bwino. Ndikuona kuti Baibuloli lingathandize kwambiri munthu amene akufuna kuliphunzira mozama.”
Pulofesa Allen Wikgren wa payunivesite ya Chicago anafotokozapo kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi chitsanzo chabwino cha Baibulo limene linamasuliridwa m’chinenero chamasiku ano. Baibuloli silinamasuliridwe potengera zimene omasulira Mabaibulo ena amachita kawirikawiri “pophatikizamo zikhulupiriro za chipembedzo chawo.”—The Interpreter’s Bible, Volume I, tsamba 99.
Ponenapo za Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, katswiri wina wa Baibulo wa ku Britain, dzina lake Alexander Thomson, analemba kuti: “Baibuloli linamasuliridwa m’Chingelezi kuchokera m’Chigiriki. Akatswiri omwe amasulira Baibuloli anayesetsa kulimasulira molondola komanso momveka bwino.”—The Differentiator, April 1952, tsamba 52.
Wolemba mabuku wina dzina lake Charles Francis Potter analemba mawu otsatirawa okhudza Baibulo la Dziko Latsopano ngakhale kuti ankaona zoti mawu ena m’Baibuloli ndi achilendo. Iye anati: “Amene anamasulira Baibuloli, omwe sanafune kuti maina awo atchulidwe, anamasulira malemba achiheberi komanso achigiriki mwaukadaulo.”—The Faiths Men Live By, tsamba 300.
Bambo Robert M. McCoy ananena kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi labwino kwambiri ngakhale lili ndi mawu ena achilendo. Pofotokoza mmene akuonera Baibuloli, bambowa anamaliza ndi mawu akuti: “Mmene Chipangano Chatsopano anachimasulirira ndi umboni wakuti m’gulu la a Mboni za Yehova muli akatswiri amene ali ndi luso lothana ndi mavuto ambiri omwe Mabaibulo ena ali nawo.”—Andover Newton Quarterly, January 1963, tsamba 31.
Pulofesa S. MacLean Gilmour anayamikira Baibulo la Dziko Latsopano ngakhale kuti sagwirizana ndi mawu ena amene ali m’Baibuloli. Iye anafotokoza kuti anthu amene anamasulira Baibuloli “ankachidziwa bwino kwambiri Chigiriki.”—Andover Newton Quarterly, September 1966, tsamba 26.
Pulofesa Thomas N. Winter anafotokozapo zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano lomwe lili mbali ya Baibulo lachingelezi la Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures. Iye anati: “Baibuloli lomwe omasulira ake sanadzitchule maina, ndi lolondola komanso likugwirizana kwambiri ndi mmene anthu akulankhulira masiku ano.”—The Classical Journal, April-May 1974, tsamba 376.
M’chaka cha 1989, pulofesa wina wa ku Israel dzina lake Benjamin Kedar, yemwe ndi katswiri wa Chiheberi ananena kuti: “Ndikamachita kafukufuku wa zinenero za Mabaibulo achiheberi komanso a zinenero zina, nthawi zonse ndimadalira Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi. Kuchita zimenezi kumandithandiza kutsimikizira ndi mtima wonse kuti Baibuloli ndi lolondola komanso n’losavuta kumvetsa.”
Pulofesa wina wamaphunziro a zipembedzo dzina lake Jason David BeDuhn, anachita kafukufuku wokhudza Mabaibulo achingelezi okwana 9 ndipo analemba kuti: “Baibulo la Dziko Latsopano ndi lolondola kwambiri kuposa Mabaibulo ena onsewo.” Ngakhale kuti akatswiri ena a Baibulo komanso anthu ambiri amanena kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi losiyana ndi Mabaibulo ena chifukwa chakuti omasulira ake anaikamo zikhulupiriro za chipembedzo chawo, pulofesayu ananena kuti: “Baibuloli limasiyana kwambiri ndi Mabaibulo ena chifukwa chakuti linamasuliridwa molondola komanso linamasuliridwa potengera mmene zilili m’mipukutu yoyambirira ya Chipangano Chatsopano.”—Truth in Translation, tsamba 163 ndi 165.
a Zimenezi zikukhudza Mabaibulo achingelezi a Baibulo la Dziko Latsopano omwe anasindikizidwa chaka cha 2013 chisanafike.
b Mwachitsanzo onani Baibulo la New International Version komanso Baibulo la Akatolika la New Jerusalem Bible. Mavesi amene anawonjezeramowo ndi Mateyu 17:21; 18:11; 23:14; Maliko 7:16; 9:44, 46; 11:26; 15:28; Luka 17:36; 23:17; Yohane 5:4; Machitidwe 8:37; 15:34; 24:7; 28:29 ndiponso Aroma 16:24. M’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu ndiponso la Douay-Rheims palemba la 1 Yohane 5:7, 8, pali mawu osonyeza kuti pali milungu itatu imene yapanga mulungu mmodzi. Mawu amenewa anawonjeredwa patadutsa zaka mahandiredi ambiri kuchokera pamene Baibulo linalembedwa.
c Mofanana ndi zimenezi, Baibulo la J. B.Phillips linamasulira vesili kuti, “amene amazindikira kuti akufunikira Mulungu,” ndiponso Baibulo la The Translator’s New Testament linamasulira vesili kuti “amene amazindikira kuti akufunikira zinthu zauzimu.”