Baibulo Longomvetsera Lomwe Linawerengedwa Ndi Anthu Ambirimbiri
“Ndi lomveka bwino komanso losangalatsa kwambiri.”
“Mmene analiwerengera, zimakhala ngati zinthuzo zikuchitikadi.”
“Landigometsa kwambiri. N’koyamba kumvetsera Baibulo lowerengedwa mokoma chonchi.”
Ambiri akumanena zangati zimenezi akamvetsera buku la Mateyu, lomwe linajambulidwa kuti anthu azingomvetsera. Bukuli ndi laulere ndipo likupezeka pawebusaiti yachingelezi ya jw.org.
A Mboni za Yehova anayamba kujambula Baibulo la Dziko Latsopano lachingerezi kuti likhale longomvetsera mu 1978. Patapita nthawi, anamaliza ntchitoyi ndipo kenako anayambanso kujambula Baibulo lonse kapena mbali yake m’zinenero zinanso zokwana 20.
Koma m’chaka cha 2013, Baibulo la Dziko Latsopano lachingerezi linakonzedwanso. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale ntchito yowerenga Baibuloli kuti likhalenso longomvetsera. Komabe mosiyana ndi loyamba lija, lomwe linali ndi owerenga atatu basi, Baibulo latsopanoli linkayenera kudzawerengedwa ndi anthu oposa 1,000.
Pa anthu onsewa, aliyense ankayenera kudzawerenga mawu a munthu winawake wa m’Baibulo. Anaona kuti njira imeneyi ndi yothandiza kwambiri chifukwa munthu akamamvetsera, amakhala ngati akuona anthu komanso zomwe zikuchitika pamalopo. Komabe, sikuti bukuli linawerengedwa ngati sewero lomwe limakhala ndi nyimbo komanso zinthu zina zokometsera.
Kujambula buku lowerengedwa ndi anthu ambirimbiri kumafuna kukonzekera bwino. Ndiye asanayambe kujambula Baibuloli, anthu ena anachita kafukufuku. Anthuwa anawerenga Baibuloli mozama kwambiri n’cholinga choti adziwe amene ananena mawu alionse omwe akupezeka m’Baibulo, tanthauzo la zimene ankanenazo komanso mmene anthuwo ankamvera. Mwachitsanzo, ngati mtumwi wina anayankhula koma sanatchulidwe dzina, ankafunika kuzindikira kuti ndi mtumwiyo ndi ndani. Choncho akaona kuti mawu amene anayankhulawo akumveka okayikira, ankawerengetsa munthu yemwe anasankhidwa kuti awerenge mawu a Tomasi. Koma ngati akumveka kuti ayankhulidwa mopupuluma, ankawerengetsa munthu amene anawerenga mawu a Petulo.
Akamasankha munthu woti awerenge mawu a munthu winawake wa m’Baibulo, ankaganiziranso msinkhu wake. Mwachitsanzo, munthu amene anawerenga mawu a Yohane ali mnyamata analinso mnyamata. Koma amene anawerenga mawu a Yohane yemweyo atakalamba, analinso wachikulire.
Komanso, anthuwa ankafunika kupeza owerenga abwino. Anthu ambiri amene anasankhidwa anali omwe amatumikira pa ofesi ya Mboni za Yehova ya ku United States. Kuti adziwe ngati angakwanitsedi kuwerenga bwino, ankawapatsa ndime ya m’magazini a Galamukani! kuti aikonzekere. Kenako ankawauza kuti aiwerenge. Ankawauzanso kuti awerenge nkhani zina za m’Baibulo. Nkhani zake zinkakhala zosonyeza munthu wina atakwiya, atakhumudwa, akusangalala kapena atafooka ndipo owerengawo ankafunika kusonyeza zimenezi akamawerenga. Zimenezi zinathandiza kuti anthu aja apeze owerenga abwino komanso kuti adziwe malo amene aliyense angawerenge bwino.
Kenako anthu aja ankauza aliyense mawu amene adzawerenge ndipo nthawi zina ankayeserera nawo n’kumawathandiza kuti akonze momwe sakuwerenga bwino. Kenako ankapita kumasitudiyo athu a ku Brooklyn, ku Patterson kapena Wallkill kuti akajambule mawu ake. Akamajambula, anthu aja ankaonetsetsa kuti wowerengayo akuwerenga momveka bwino komanso moyenerera. Anthuwa komanso owerengawo ankakhala ndi mapepala pomwe panali mawu omwe akufunika kuwerengedwawo. Mapepalawo anakonzedwa mwapadera kuti athandize munthu kudziwa malo amene akufunika kupuma komanso kutsindika. Baibulo lakale lachingerezi lomwe linajambulidwa kuti anthu azingomvetsera linathandizanso anthuwa kuti adziwe mmene angawerengere mawu ena.
Akangojambula mawu a munthu, ogwira ntchito kusitudiyoko ankadula komanso kuchotsa mbali zina pofuna kuti mawuwo amveke bwino. Nthawi zina ankajambula chiganizo chimodzi kangapo, ndipo kenako ankasankhapo mawu amene amveka bwino kwambiri.
Sitikudziwa kuti patenga nthawi yaitali bwanji kuti amalize kujambula Baibulo la Dziko Latsopano lomwe linakonzedwanso mu 2013. Komabe, buku lililonse la m’Baibulo likamalizidwa kujambulidwa, liziikidwa pa intaneti patsamba lakuti, “Mabuku a M’Baibulo.” Pafupi ndi dzina la bukulo pazikhala kachizindikiro kosonyeza kuti bukulo liliponso lomvetsera.