Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ntchito Yomasulira M’chinenero cha Manja cha ku Quebec Yathandiza Anthu Ambiri

Ntchito Yomasulira M’chinenero cha Manja cha ku Quebec Yathandiza Anthu Ambiri

M’madera ambiri a ku m’mawa kwa dziko la Canada kumene amayankhula Chifulenchi, anthu ambiri omwe ali ndi vuto losamva amagwiritsa ntchito Chinenero Chamanja cha ku Quebec (LSQ). * Chifukwa choti anthu omwe ali ndi vuto losamva alipo 6,000 okha, pali mavidiyo ndi zinthu zina zochepa za Chinenero Chamanja cha ku Quebec. Komabe, pofuna kuthandiza anthu kumvetsa Baibulo, posachedwapa a Mboni za Yehova akhala akugwira ntchito mwakhama n’cholinga choti azipanga mavidiyo komanso zinthu zina za Chinenero Chamanja cha ku Quebec. Zinthu zonsezi zimapangidwa m’njira yapamwamba kwambiri ndipo anthu akhoza kuzipeza kwaulere.

Nkhani ya a Marcel itithandiza kumvetsa chifukwa chake khama pa ntchito yomasulirayi lili lofunika kwambiri. Iwo anabadwa mu 1941 m’chigawo cha Quebec ku Canada. Ali ndi zaka ziwiri, anayamba kudwala matenda oumitsa khosi ndipo anasiya kumva. A Marcel ananena kuti: “Ndili ndi zaka 9, ndinayamba kupita kusukulu ya anthu a vuto losamva kumene ndinakaphunzira Chinenero Chamanja cha ku Quebec. Ngakhale kuti panali mabuku ophunzirira chinenero chamanja, panalibe mavidiyo ndi zinthu zina za m’chinenero chamanja.”

N’chifukwa chiyani kupanga mavidiyo ndi zinthu zina za Chinenero Chamanja cha ku Quebec kuli kofunika? A Marcel akuyankha kuti: “Anthu omwe ali ndi vuto losamva amafuna kuphunzira komanso kudziwa zinthu m’chinenero chimene angathe kuchimva bwino, m’malo molimbana ndi chinenero chimene sakuchidziwa. Zikakhala kuti palibe mavidiyo ndi zinthu zina za Chinenero Chamanja cha ku Quebec, timadalira zilankhulo zolankhula ndi pakamwa ndipo zimenezi zimachititsa kuti tisamapindule kwambiri.”

Pofuna kuthandiza a Marcel komanso anthu ena omwe ali ndi vuto losamva amene amagwiritsa ntchito Chinenero Chamanja cha ku Quebec, a Mboni za Yehova anatulutsa vidiyo yoyamba ya m’chinenerochi mu 2005. Posachedwapa, iwo anakulitsa ofesi ya omasulira zinthu yomwe ili ku Montreal ku Quebec. Pa ofesiyi tsopano pali anthu ogwira ntchito 7 komanso ena ongothandiza oposa 12. Anthuwa anagawidwa m’magulu atatu ndipo ali ndi masitudiyo awiri omwe ali ndi zipangizo zapamwamba kwambiri zojambulira mavidiyo a Chinenero Chamanja cha ku Quebec.

Anthu omwe amagwiritsa ntchito Chinenero Chamanja cha ku Quebec amayamikira kwambiri mavidiyo omwe a Mboni za Yehova amapanga chifukwa ndi abwino kwambiri. A Stéphan Jacques, omwe ndi wothandiza kwa mkulu woyendetsa bungwe la Association des Sourds de l’Estrie, * anati: “Mavidiyo omwe a Mboni amapangawa ndi abwino kwambiri. Zimene amanena sizivuta kumva, ndipo mmene amachitira manja ndi nkhope zimasangalatsa kwambiri. Komanso ndikuyamikira kwambiri kuti anthu amene amajambulidwa m’mavidiyowa amavala bwino.”

^ ndime 2 LSQ, lomwe ndi dzina lochokera ku mawu a Chifulenchi oti Langue des signes québécoise, ndi mtundu wapadera wa chinenero chamanja ngakhale kuti umafananako ndi Chinenero Chamanja cha ku America chomwe chimagwiritsidwa ntchito m’mayiko ambiri.

^ ndime 6 Bungweli limathandiza anthu a vuto losamva ku Quebec.

Magazini ya Nsanja ya Olonda imagwiritsidwa ntchito pamisonkhano ya Mboni za Yehova mlungu uliwonse padziko lonse. Panopa magaziniyi ikupezeka mu Chinenero Chamanja cha ku Quebec ndipo imagwiritsidwa ntchito m’mipingo 5 ndi magulu awiri ndipo muli a Mboni okwana 220. Kuonjezera pamenepa, a Mboni akupitiriza kupanga mavidiyo osiyanasiyana a Chinenero Chamanja cha ku Quebec omwe amaikidwa pa intaneti. Iwo akupanganso nyimbo zochokera m’Baibulo zomwe zimalimbikitsa anthu.

Magazini yoyamba ya Nsanja ya Olonda yophunzira ya Chinenero Chamanja cha ku Quebec inali ya January 2017.

A Marcel, omwe tawatchula poyamba aja, ndi osangalala kwambiri chifukwa choti pali mavidiyo ambiri a Chinenero Chamanja cha ku Quebec. Iwo amayamikira kwambiri mavidiyowa, koma makamaka opangidwa ndi a Mboni za Yehova. Iwo ananena kuti: “N’zosangalatsa kwambiri kuona mavidiyo ambiri a Chinenero Chamanja cha ku Quebec pa jw.org. Ndimasangalalanso kwambiri ndikaona zinthu zonse zomwe zili m’chinenero changa.”