A Mboni za Yehova ku Nigeria Amanga Nyumba za Ufumu Zokwana 3,000
Loweruka pa March 1, 2014, a Mboni za Yehova okwana 823 anasonkhana pa Nyumba yochitiramo misonkhano mumzinda wa Benin ku Nigeria. Cholinga cha msonkhanowu chinali kusangalala kuti m’dzikoli mwamangidwa Nyumba za Ufumu 3,000. M’chaka cha 1999, a Mboni za Yehova anakhazikitsa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka, ndipo amanga Nyumba za Ufumu zokwana 3,000 m’dziko la Nigeria.
Pamsonkhanowu panafotokozedwa mbiri yachidule yokhudza zimene zinkachitika kuyambira m’ma 1920 pofuna kupeza malo oti mipingo ya m’dziko la Nigeria izilambiriramo. Poyamba a Mboni ankasonkhana m’nyumba za anthu kapenanso kuchita lendi maholo. Mu 1935, anamanga nyumba yawo ya Ufumu yoyamba mumzinda wa Ilesa. Kuyambira m’chaka cha 1938 mpaka 1990, chiwerengero cha mipingo chinakwera kwambiri kuchoka pa 14 kufika pa 2,681 ndipo zimenezi zinachititsa kuti a Mboni ambiri azisowa malo ochitiramo misonkhano. M’madera ena mipingo 6 inkachitira misonkhano pamalo amodzi ndipo inkasinthana nthawi. Ndipo m’madera ena anthu ankadzaza kwambiri moti ena ankaima kunja m’mawindo n’kumamvetsera. Ngakhalenso masiku ano m’mipingo ina ya m’dzikoli, a Mboni amasonkhanabe m’nyumba za anthu ndiponso m’makalasi.
Mu 1990, ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko la Nigeria inayamba kupereka ndalama m’mipingo kuti imangire Nyumba za Ufumu ndipo mipingoyo inkabweza pang’onopang’ono ndalamazo. Ofesiyi inachita izi pofuna kuthandiza kuti m’dzikolo mukhale malo ambiri olambiriramo. Pofika chaka cha 1997, Makomiti Oyang’anira Ntchito ya Zomangamanga m’dzikolo komanso m’mayiko ena, anathandiza mipingo 105 kumanga kapena kukonzanso Nyumba za Ufumu. Kuyambira mu 1997 mpaka mu 1999, panamangidwa Nyumba za Ufumu 13 ndipo nyumbazi zinkamangidwa kwa masiku 7 mpaka 15 basi.
Ngakhale kuti malo olambirirawa ankamangidwa mwachangu chonchi, mipingo ina inkasowabe Nyumba za Ufumu. Mu April 1998, ofesi ya nthambi inanena kuti m’dzikoli mukufunika Nyumba za Ufumu zokwana 1,114.
Pamsonkhano wapaderawu womwe unachitikira mumzinda wa Benin, a Don Trost, omwe ndi a m’Komiti ya Nthambi ya dziko la Nigeria ananena kuti: “Ntchitoyi inali yaikulu kwambiri. Moti tinkangodzifunsa kuti, ‘Kodi ntchito imeneyi tiikwanitsa?’” Koma podzafika m’chaka cha 1999, funsoli linayankhidwa chifukwa panali Magulu Omanga Nyumba za Ufumu okhala ndi anthu 6 kapena 8 omwe ankathandiza mipingo ya m’dzikoli. Abalewa ankagwiritsa ntchito mapulani amakono omwe ndi osavuta ndipo akhala akumanga Nyumba za Ufumu 17 mwezi uliwonse pa zaka 14 zapitazi.
A Trost anayamikira anthu omwe anali pamsonkhanowo chifukwa cha ntchito yomwe anagwira ndipo anawauza kuti padakali ntchito yambiri yoti igwiridwe. M’chaka cha 2013, chiwerengero cha Mboni za Yehova ku Nigeria chinawonjezeka ndi anthu oposa 8,000. A Trost ananenso kuti: “Popeza kuti chiwerengero chathu chikukula kwambiri, m’tsogolomu tizidzafunika kumanga Nyumba za Ufumu 100 chaka chilichonse.” M’chaka cha 2013, mipingo ya Mboni za Yehova ku Nigeria inalipo 5,700 ndipo a Mboni onse analipo 351,000.