Anaima Kuti Andithandize
Tsiku lina a Bob ankayendetsa galimoto ku Alberta, m’dziko la Canada ndipo ankathamanga paliwiro la makilomita 100 pa ola. Pa tsikuli kunkazizira, kunali mphepo yamphamvu ndi mvula ndipo mwadzidzidzi tayala lakumbuyo la galimotoyo linaphulika. Poyamba a Bob sankadziwa zomwe zinachitika ndipo anaganiza zopitiriza kuyendetsa kuti akafike kunyumba yawo yomwe inali pamtunda wa makilomita 5.
M’kalata yomwe analembera mpingo wa Mboni za Yehova m’deralo, a Bob anafotokoza zomwe zinachitika. Iwo analemba kuti: “Anyamata atatu ndi atsikana awiri anali m’galimoto yomwe inkayenda pafupi ndi yanga ndipo anatsitsa windo la galimoto yawo. Iwo anandiuza kuti tayala la galimoto yanga laphulika. Kenako tinaimitsa magalimotowo m’mphepete mwa msewu ndipo ananena kuti andisinthira tayalalo.” Pa nthawiyi sindinkadziwa ngati ndinali ndi tayala lina kapena jeke. Koma iwo atasuzumira pansi pa galimotoyo anapeza tayala lina ndi jeke ndipo anandisinthira tayalalo. Apa n’kuti nditakhala pa njinga yanga ya olumala m’mbali mwa msewu. Pa tsikuli kunkazizira kwambiri ndiponso kunkagwa sinowo. Ngakhale kuti anali atavala zovala zabwino, anandisinthira tayalalo ndipo ndinatha kupitiriza ulendo wanga. Sindikanakwanitsa kuchita zimenezi ndekha.
“Ndikuthokoza kwambiri achinyamata 5 a Mboni omwe anandithandiza. Iwo anapezeka m’derali chifukwa ankalalikira m’nyumba za anthu. Achinyamata amenewa amachitadi zomwe amalalikira. Ndikuwayamikira kwambiri chifukwa akanapanda kundithandiza ndikanavutika kwambiri pa ulendowu. Zinangokhala ngati Mulungu wawatumiza kuti akumane ndi ine pa tsikuli.”