Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 30, 2019
AZERBAIJAN

Msonkhano Wachigawo Wosaiwalika ku Azerbaijan

Msonkhano Wachigawo Wosaiwalika ku Azerbaijan

Kuyambira pa 26 mpaka pa 28 July, 2019, a Mboni za Yehova ku Azerbaijan anapanga msonkhano wawo wapachaka wachigawo pamalo otchedwa Darnagul Ceremony House, omwe ali mumzinda wa Baku lomwe ndi likulu la dzikolo. Pamene chaka chino kukuchitika misonkhano yosaiwalika yamayiko, ku Baku nakonso kunachitika msonkhano wachigawo wosaiwalika. Unali msonkhano wachigawo waukulu kwambiri kuchitika ku Azerbaijan komanso kanali koyamba kuti mipingo ya chinenero cha Chiazerbaijani ndi ya Chirasha ya m’dziko lonselo ichite msonkhano wachigawo pa nthawi imodzi.

Ngakhale kuti ku Azerbaijan kuli ofalitsa pafupifupi 1,500 okha, pamsonkhanowu panali anthu 1,938 ndipo anthu 33 anabatizidwa. M’bale Mark Sanderson anapatsidwa chilolezo chapadera kuti alowe m’dzikolo kukakamba nkhani pamsonkhanowo. Aka kanali koyamba kuti m’bale wa m’Bungwe Lolamulira apezeke pamsonkhano wachigawo ku Azerbaijan. Tikuyamikira kwambiri akuluakulu a boma popereka chilolezo chimenechi.

Mgwirizano wa abale ndi alongo unali ulaliki wamphamvu kwa anthu. Mkulu woyang’anira malo omwe panachitikira msonkhanowu ananena kuti pamene msonkhanowu unkachitika, anaona a Mboni akuchita zinthu mwamtendere, akusonyezana chikondi, akuchita zinthu mokomerana mtima komanso anaona kuti amachitadi zimene amaphunzitsa ena.

Ngakhale kuti ufulu wopembedza wa Mboni za Yehova ukupitirizabe kuphwanyidwa ku Azerbaijan, akuluakulu a boma akhala akupatsa abale athu ufulu wambiri wochita zomwe amakhulupirira. Mu November 2018, boma la Azerbaijan linalemba chipembedzo cha Mboni za Yehova kukhala chovomerezeka ndi malamulo mumzinda wa Baku. Zimenezi zithandiza abale athu kuti azilambira mosabisa mumzindawu.

Tikusangalala limodzi ndi abale ndi alongo athu ku Azerbaijan chifukwa cha zinthu zosangalatsazi, kuphatikizapo msonkhano wachigawo waposachedwapa womwe ndi wosaiwalika m’mbiri ya choonadi m’dzikolo. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa khama lomwe likuchitika pofuna “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino” m’dziko la Azerbaijan komanso padziko lonse.—Afilipi 1:7.