Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Chithunzi chojambulidwa mumlengalenga pa 5 July 2024, chosonyeza mphepo yamkuntho ya Beryl yomwe inawomba m’mbali mwa nyanja ku Yucatán m’dziko la Mexico

12 JULY 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Anthu Ambiri Akhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Beryl

Anthu Ambiri Akhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Beryl

Pa 30 June 2024, Mphepo yamkuntho yotchedwa Beryl inadutsa kum’mwera kwa chilumba cha Martinique ku West Indies. Tsiku lotsatira, mphamvu za mphepoyo zinawonjezereka ndipo inawomba komanso kuwononga zinthu m’dera la Windward Islands, lomwe likuphatikizapo ku Barbados, Grenada, Saint Vincent komanso ku Grenadines. Tsiku lotsatira, inawombanso mwamphamvu kwambiri ku Venezuela. Kenako mphepoyi anadutsa m’mbali mwa doko lakum’mwera kwa Jamaica. Pa 5 July, mphepo yamphamvuyi inadutsa ku Yucatán ku Mexico isanawononge kum’mwera kwa United States.

Mphepoyi inkathamanga liwiro la makilomita 270 pa ola ndipo kulikonse komwe inkadutsa kunkagwa chimvula komanso inawononga nyumba, mabizinesi ndi zinthu zina. Mpaka pano, anthu mamiliyoni angapo omwe akukhala m’madera okhudzidwawa alibe magetsi, madzi komanso zinthu zina zofunika. Malipoti akusonyeza kuti anthu oposa 30 anaphedwa.

Mmene Mphepo Yamkunthoyi Yakhudzira Abale ndi Alongo Athu

Martinique (West Indies)

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala

  • Ofalitsa 6 anasamuka m’nyumba zawo

  • Nyumba imodzi inawonongedweratu

  • Nyumba imodzi inawonongedwa kwambiri

  • Nyumba imodzi inawonongedwa pang’ono

  • Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa

Nyumba ya Ufumu imene inawonongedwa ku Windward Islands

Windward Islands

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu yemwe anaphedwa

  • Ofalitsa 7 anavulala

  • Ofalitsa 67 anasamuka m’nyumba zawo

  • Nyumba 39 zinawonongedwa kwambiri

  • Nyumba 31 zinawonongedwa pang’ono

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedweratu

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedwa kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 4 zinawonongedwa pang’ono

Venezuela

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala

  • Ofalitsa 30 anasamutsidwa m’nyumba zawo

  • Nyumba 12 zinawonongedwa kwambiri

  • Nyumba 9 zinawonongedwa pang’ono

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedwa kwambiri

Jamaica

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala

  • Ofalitsa 18 anasamutsidwa m’nyumba zawo

  • Nyuma 24 zinawonongedwa kwambiri

  • Nyumba 75 zinawonongedwa pang’ono

  • Nyumba za Ufumu 19 zinawonongedwa pang’ono

Mexico

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala

  • Ofalitsa 320 anasamutsidwa koma tsopano anabwerera kunyumba zawo

  • Nyumba 11 zinawonongedwa pang’ono

  • Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa

United States

  • Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa

  • Ofalitsa 6 anavulala

  • Ofalitsa 242 anasamutsidwa

  • Nyumba 4 zinawonongedweratu

  • Nyumba 33 zinawonongedwa kwambiri

  • Nyumba 471 zinawonongedwa pang’ono

  • Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa

Ntchito Yopereka Chithandizo

Oyang’anira madera komanso akulu akuthandiza anthu onse okhala m’madera okhudzidwawa powalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza m’njira zina. Kuwonjezera pamenepa, Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi okwana 6 anakhazikitsidwa kuti aziyang’anira ntchito yopereka thandizo.

Pemphero lathu ndi lakuti Yehova apitirize kutonthoza onse omwe akumudalira pa nthawi yovutayi.—2 Akorinto 1:3, 4.