Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 11, 2018
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Anasonyeza Chikondi Pothandiza Akhristu Anzawo ku Zilumba za Caribbean

A Mboni za Yehova Anasonyeza Chikondi Pothandiza Akhristu Anzawo ku Zilumba za Caribbean

Vidiyo ili m’munsiyi ikusonyeza mmene ntchito yothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi Mphepo za Mkuntho zotchedwa Irma komanso Maria inayendera m’madera amene amayang’aniridwa ndi nthambi za Barbados, France, ndi United States. Vidiyoyi ikufotokoza khama limene abale ndi alongo ambiri ongodzipereka anasonyeza pothandiza Akhristu anzawo ndipo ikusonyezanso mwachidule ulendo wa M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira ndiponso M’bale Gary Breaux, wothandiza mu Komiti ya Utumiki omwe anakayendera abale amene anakhudzidwa ndi ngoziyi.