Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 24, 2014
ERITREA

Kodi Anthu Amene Atha Zaka 20 Ali M’ndende ku Eritrea Adzatuluka?

Kodi Anthu Amene Atha Zaka 20 Ali M’ndende ku Eritrea Adzatuluka?

Zaka 20 zapitazo, boma la Eritrea linamanga anyamata atatu ndi kuwatsekera m’ndende ya Sawa, ndipo akukhala mozunzika mpaka pano. Anthuwa akungosungidwa popanda kuwazenga mlandu kukhoti. N’chifukwa chiyani anthuwa akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo chonchi?

Paulos Eyassu, Negede Teklemariam, ndi Isaac Mogos ndi a Mboni za Yehova ndipo anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupilira. Akanaimbidwa mlandu wokana kulowa usilikali, bwenzi atapatsidwa zaka zoti akakhale kundende. Panopa, Paulos ali ndi zaka 41, Negede ali ndi zaka 38 ndipo Isaac alinso ndi zaka 38. Iwowa athera zaka za unyamata zonse ali m’ndende. Zimenezi zachititsa kuti asakhale ndi mwayi wokwatira, wokhala ndi ana, wosamalira makolo awo, wochita zomwe akufuna komanso wolambira ndi Akhristu anzawo.

Anyamatawa anamangidwa pa September 24, 1994 ndipo akhala akuzunzidwa kwambiri ndi oyang’anira ndende ya Sawa. Koma zaka zaposachedwapa, oyang’anira ndendewa asiya kuzunza anyamatawa ndipo kulimba mtima kwawo potsatira zimene amakhulupilira kwapangitsa kuti oyang’anira akaidi aziwalemekeza.

A Mboni enanso akukhala mozunzika kundende

Dziko la Eritrea ndi limene likuzunza kwambiri a Mboni za Yehova kuposa dziko lina lililonse. Ndipotu mmene nkhaniyi inkalembedwa n’kuti a Mboni 73 kuphatikizapo azimayi, ana ndiponso okalamba ali m’ndende. Ambiri mwa anthuwa amakhala mozunzika chifukwa cha nyengo yoipa, kusowa zakudya zamagulu onse, madzi ndiponso kuzunzidwa ndi oyang’anira ndende. A Mboni za Yehova enanso atatu anatsekeredwa m’ndende ya Sawa kwa zaka zoposa 10 koma Paulos, Negede, komanso Isaac ndi a Mboni amene akhala kwambiri m’ndende kuposa a Mboni onse ku Eritrea.

Mayiko ndi mabungwe ena akhala akupempha boma la Eritrea kuti lisiye kuchitira nkhanza zipembedzo

Mayiko ndi mabungwe ena akudziwa bwino zokhudza nkhanza zimene dziko la Eritrea limachitira a Mboni za Yehova komanso zipembedzo zina zing’onozing’ono.

  • Kuyambira mu 2004, dipatimenti yoona za ubale wa dziko la United States ndi mayiko ena yakhala ikunena kuti dziko la Eritrea ndi limodzi mwa ‘mayiko odetsa nkhawa kwambiri,’ zomwe zikutanthauza kuti ndi dziko limene boma lake limaphwanya kapena kulola anthu ena kuphwanya ufulu wa chipembedzo wa anzawo mochita kukonzekera, mwankhanza kwambiri komanso nthawi zonse.

  • Bungwe loona za ufulu wa anthu la United Nations, ndi lokhudzidwa kwambiri chifukwa cha “zimene akuluakulu a dziko la Eritrea akuchita pophwanya mwankhanza ufulu wa anthu omwe ndi nzika zawo zomwe.” Bungweli likupempha boma la Eritrea “kuti lizilemekeza ufulu wa munthu aliyense . . . wonena maganizo ake, wotsatira chikumbumtima, wosankha chipembedzo komanso zimene akufuna kukhulupirira.”

  • Lipoti lapachaka la mu 2014, lomwe linatulutsidwa ndi bungwe lina la ku America loona za ufulu wa zipembedzo, linati: “Ufulu wachipembedzo ukuphwanyidwa kwambiri makamaka kwa . . . A Mboni za Yehova.”

  • Bungwe lina linanena kuti boma la Eritrea likupitiriza kumanga, kutsekera m’ndende ndi kuzunza anthu a zipembedzo zosadziwika bwino koma “amene akuzunzidwa kwambiri ndi a Mboni za Yehova.”—World Report 2013, Human Rights Watch.

  • Mu December 2005, bungwe lina loona za ufulu wa anthu linapanga chigamulo chakuti dziko la Eritrea lizilemekeza ufulu wa anthu. Bungweli linanena kuti dziko la Eritrea “nthawi zonse lizipatsa anthu ufulu wozengedwa mlandu mwachilungamo, wolankhula ndi kunena maganizo awo komanso ufulu wochita misonkhano yachipembedzo mwamtendere.”—African Commission on Human and Peoples’ Rights.

A Philip Brumley, omwe amalankhula poimira Mboni za Yehova, ananena kuti: “Tikukhulupirira kuti boma la Eritrea litulutsa m’ndende akaidi onse a Mboni, kuphatikizapo azibambo atatu amene panopa atha zaka 20 ali m’ndende komanso kuti bomali lisiya kuzunza Akhristu anzathu.”