Germany
Mboni za Yehova ku Germany
● Mboni za Yehova—???
● Mipingo—???
● Chiwerengero cha anthu opezeka pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu—???
● Pa anthu ??? alionse m’dzikoli pali wa Mboni za Yehova m’modzi
● Chiwerengero cha anthu—???
Chionetsero Chokumbukira Nkhanza Zomwe a Mboni za Yehova Anakumana Nazo ku Germany
Chionetsero chomwe chikuchitika m’malo osiyanasiyana chikusonyeza kuti a Mboni za Yehova anazunzidwa ndi chipani cha Nazi komanso ulamuliro wa German Democratic Republic chifukwa cha chikhulupiriro chawo chomwe chinali champhamvu kwambiri.
Chionetsero Chokumbukira Kuti Patha Zaka 70 Chichitikireni Msonkhano Wosaiwalika Chinachitika Mumzinda wa Kassel ku Germany
A Mboni za Yehova mumzinda wa Kassel anapanga chionetsero chokumbukira kuti patha zaka 70 chichitikireni msonkhano waukulu kwambiri womwe a Mboni anapanga pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.
Mwambo Wokumbukira a Max Eckert Unachititsa Kuti Anthu Ambiri Awadziwe
Ngakhale kuti ndi anthu ochepa okha omwe ankamudziwa M’bale Eckert asanamwalire, panopa amadziwidwa ndi anthu ambiri monga munthu yemwe anali ndi chikhulupiriro champhamvu.
Makhoti a ku Germany Amaona Misonkhano Ikuluikulu ya Mboni za Yehova Monga Maholide Achipembedzo
Misonkhano ya chigawo ya a Mboni tsopano imaonedwa monga maholide a chipembedzo, ndipo zimenezi zikusonyeza ufulu umene makolo ali nawo wophunzitsa ana awo zinthu zimene amakhulupirira.
Bambo Wina ndi Mwana Wake Analandira Mendulo Yaulemu Chifukwa Chopulumutsa Anthu pa Ngozi ya Galimoto
A Andreas Bonk, omwe ndi a Mboni za Yehova, ndi mwana wawo Jorim analandira mendulo yaulemu chifukwa chakuti anachita zinthu molimba mtima komanso mosaganizira moyo wawo.
Ku Sachsenhausen Kunachitika Mwambo Wokumbukira wa Mboni za Yehova Yemwe Anaphedwa ndi Chipani cha Nazi
Pa September 16, 2014, Bungwe la Brandenburg Memorials Foundation linachita mwambo wokumbukira kuti patha zaka 75 kuchokera pamene a August Dickmann anaphedwa kundende ya Sachsenhausen. Iwowa anali oyamba kuphedwa anthu ena akuona, pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndi chipani cha Nazi chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.
Bambo Richard Rudolph, Omwe Anapulumuka M’ndende Zozunzirako Anthu ku Germany, Amwalira Ali ndi Zaka 102
Bambo Richard Rudolph, omwe anali a Mboni za Yehova anamangidwa kwa zaka zoposa 19 chifukwa cha chikhulupiriro chawo.
Mwambo Wokhazikitsa Chipilala Chokumbukira wa Mboni za Yehova Amene Anapulumuka Nkhanza ku Germany
Kodi n’chiyani chinathandiza Bambo Max Liebster, omwe anali a Mboni za Yehova, kupirira pamene ankazunzidwa kundende 5 zosiyanasiyana?
Dziko la Germany Lapereka Mendulo Yaulemu kwa Mayi Wina wa Mboni za Yehova Poyamikira Ntchito Yake Yotamandika
Mathilde Hartl analandira mendulo yaulemu imene boma la Germany limapereka kwa anthu okhawo amene achita zinthu zazikulu. Anapereka menduloyi ndi nduna yaikulu ya chigawo cha Bavaria.