Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anthu 500 omwe anasonkhana patsiku lomwe mwambo otsegulira chionetserochi unachitika.

SEPTEMBER 14, 2018
GERMANY

Chionetsero Chokumbukira Kuti Patha Zaka 70 Chichitikireni Msonkhano Wosaiwalika Chinachitika Mumzinda wa Kassel ku Germany

Chionetsero Chokumbukira Kuti Patha Zaka 70 Chichitikireni Msonkhano Wosaiwalika Chinachitika Mumzinda wa Kassel ku Germany

Mu July 1948, a Mboni za Yehova anapanga msonkhano mumzinda wa Kassel ku Germany. Msonkhanowu unali waukulu kwambiri kuchitika ku Europe pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Pokumbukira kuti patha zaka 70 chichitikireni msonkhanowu, a Mboni za Yehova anapanga chionetsero mumzinda wa Kassel. Anthu oposa 2,000 anapezeka pa chionetserochi chomwe chinatenga masiku 12. Wailesi ya kanema ya m’dziko la Germany komanso nyuzipepala zambiri za m’dzikolo zinafalitsa nkhani zokhudza chionetserochi.

A Mboni za Yehova omwe anapanga nawo msonkhano wa mu 1948 akufotokoza zomwe zinachitika pamsonkhanowo.

Pamsonkhano womwe unachitika ku Kassel mu 1948, panali anthu 23,150 kuphatikizapo 1,200 amene anabatizidwa. Anthu ambiri omwe anakamba nkhani komanso kupezeka pamsonkhanowu anali omwe anapulumuka m’ndende zozunzirako anthu. Pa chifukwa chimenechi, a Dr. Gunnar Richter, omwe ndi mkulu wa malo osungirako mbiri yokhudza nkhanza zomwe zinkachitika pandende yozunzirako anthu ku Breitenau, anayankhula chakumayambiriro kwa mwambowu ndipo anafotokoza nkhanza zomwe a Mboni za Yehova anakumana nazo mu ulamuliro wa chipani cha Nazi.

Abale ndi alongo akukonza malo a msonkhano omwe anali ndi maenje oposa 50 omwe anapangidwa chifukwa cha kuphulika kwa mabomba.

Pa chionetserochi panali zithunzi zosonyeza mzinda wa Kassel utatsala pang’ono kuonongeka chifukwa cha nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Abale athu atapanga dongosolo loti akhale ndi msonkhanowu, akuluakulu a boma anawapatsa malo oti achitirepo msonkhanowo omwe anali ndi maenje aakulu amene anapangidwa chifukwa cha kuphulika kwa mabomba. M’bale Kurt Rex yemwe analipo pamsonkhanowu, anafotokoza kuti abale anagwira ntchito yokonza malo ochitira msonkhanowo mwakhama kwa milungu 4. Iwo anati: “Ntchitoyi inali yovuta kwambiri. Choyamba tinkafunika kuchotsa madzi omwe anali m’maenjewo pogwiritsa ntchito mabigili. Titamaliza kuchita zimenezi m’pamene zinali zotheka kuyamba ntchito yeniyeniyo komanso kukwirira maenjewo ndi miyala komanso dothi lochokera kunyumba zogumuka zomwe zinali pafupi. Ntchito yosalaza malowa inalinso yovuta kwambiri chifukwa tinalibe mashini ena alionse kapena zida zosalazira. Nthawi zambiri tinkakhala onyowa chifukwa choti nthawi zonse kunkagwa mvula.” Ngakhale kuti mvula inkagwa tsiku ndi tsiku, abale athu anakwanitsa kututa miyala komanso dothi lambiri.

Ena mwa anthu oposa 23,000 omwe anapanga nawo msonkhanowo.

M’nkhani yomwe anakamba potsegulira chionetserochi, a Wolfram Slupina omwe ndi oimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Germany, anafotokoza zimene zinathandiza abale ndi alongo pamene ankakonzekera msonkhanowo. Iwo anati: “Atamasulidwa m’ndende zozunzirako anthu, iwo sanaganizire kwambiri zinthu zoipa zomwe anakumana nazo kapena kupsa mtima. . . . Kumasulidwa kwawo kunawathandiza kuti ayambenso kugwira ntchito mwakhama.”

Poyankhula kwa anthu omwe anali pachionetserochi, a Esther Kalveram omwe ndi khansala komanso woimira akuluakulu oyang’anira mzinda wa Kassel, anati: “Sikuti msonkhanowu unali wapadera kwa a Mboni za Yehova okha, koma unalinso wapadera kwa anthu okhala mumzinda wa Kassel.”

Msonkhano womwe unachitika ku Kassel mu 1948 komanso chionetsero cha mu 2018 chokumbukira kuti patha zaka 70 chichitikireni msonkhanowu, ndi umboni woti anthu a Yehova ndi okonzeka kusonkhana pamodzi kuti aphunzire Baibulo ngakhale pa nthawi imene akukumana ndi mavuto aakulu.—Salimo 35:18.