Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 7, 2014
GERMANY

Bambo Richard Rudolph, Omwe Anapulumuka M’ndende Zozunzirako Anthu ku Germany, Amwalira Ali ndi Zaka 102

Bambo Richard Rudolph, Omwe Anapulumuka M’ndende Zozunzirako Anthu ku Germany, Amwalira Ali ndi Zaka 102

SELTERS, Germany—Bambo Richard Rudolph, omwe anali a Mboni za Yehova, anamwalira pa January 31, 2014 ali ndi zaka 102. Bambowa anapirira ulamuliro wankhanza wachipani cha Nazi ndipo anaponyedwa m’ndende 5 zozunzirako anthu. Ulamuliro wa chipanichi utatha, bambowa anapitirizabe kuzunzidwa ndi ulamuliro wina wankhanza ku Germany.

M’chaka cha 1933, chipani cha Nazi chinayamba kulamulira ndipo ntchito ya a Mboni za Yehova inaletsedwa m’madera ambiri ku Germany. Zimenezi zinachititsa kuti chipanichi chimange anthu a Mboni okwana 11,300. Pa anthu amenewa, 4,200, kuphatikizapo Bambo Rudolph, anaponyedwa m’ndende zozunzirako anthu ndipo anthu 1,500 anafera kundende komweko. Pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi, Bambo Rudolph anakhala zaka 9 ali m’ndende zosiyanasiyana. Iwo anazunzidwa m’ndende 5 zosiyanasiyana, kuphatikizapo ndende zoopsa zotchedwa Sachsenhausen ndiponso Neuengamme. Anthu oposa 300,000 anaponyedwa m’ndendezi ndipo anthu ochuluka mpaka kufika pa 140,000, anafera komweko.

A Richard Rudolph (akuoneka padenga la nyumba chakumanja) iwo anali m’gulu la akaidi amene anamanga nawo ndende ya Neuengamme mu 1940.

Mu 1944, Bambo Rudolph anawasamutsira kundende yaing’ono yotchedwa Neuengamme m’dera la Salzgitter-Watenstedt. Bambowa anakana kugwira ntchito yopanga zida za nkhondo chifukwa cha mfundo za m’Baibulo zimene iwo ankatsatira. Choncho zimenezi zinachititsa kuti aziopsezedwa kuti anyongedwa. Komabe msilikali wina yemwe anachita chidwi ndi mmene a bambowa ankatsatirira mfundo za m’Baibulo, anawabisa m’chigalimoto chonyamula zakudya ndipo sanaphedwe.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, a Rudolph anapitiriza ntchito yolalikira monga wa Mboni za Yehova m’dera la Soviet Occupation Zone lomwe kenako linayamba kudziwika kuti German Democratic Republic (GDR). Mu 1950, a Rudolph anaponyedwanso m’ndende. Choncho zaka zonse zimene bambowa anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo zinakwana 19.

Ann-Jacqueline Frieser ali ndi a Richard Rudolph. Mtsikanayu analemba nkhani yokhudza bambowa ndipo anapatsidwa mphoto mu 2009.

Kwa zaka zambiri Bambo Rudolph ankachita khama polalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu ena ndiponso ankauza ena zinthu zimene zinawachitikira pa moyo wawo zokhudza kuipa kwa tsankho. Mu 2009, mtsikana wina dzina lake Ann-Jacqueline Frieser, wa pasukulu ina ku Germany, analandira mphoto ziwiri pa mpikisano wa ana asukulu wokhudza mbiri yakale, umene anauyambitsa ndi pulezidenti wina wa dzikolo. Mtsikanayu analemba mbiri yokhudza a Richard Rudolph. Iye anachita bwino pa mpikisanowu moti anakhala nambala wani m’dera la Rheinland-Palatinate komanso anali m’gulu la ana asukulu atatu amene anachita bwino m’dziko lonseli ndipo anapatsidwa mphoto.

Bambo Wolfram Slupina omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Germany, anati: “Bambo Richard Rudolph sanali mnzathu chabe amene timalambira naye Mulungu pamodzi, koma analinso nkhokwe ya mbiri yakale. Chikhulupiriro chawo komanso kulimba mtima kumene anasonyeza pa moyo wawo ndi zothandiza kwa tonsefe.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110