Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 27, 2019
GHANA

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’chinenero cha Chinzema

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’chinenero cha Chinzema

Pa 22 November, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu linatulutsidwa m’chinenero cha Chinzema, pamsonkhano womwe unachitikira ku Bawia, m’chigawo chakumadzulo m’dziko la Ghana. Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka 4. M’bale Samuel M. Kwesie, wa m’Komiti ya Nthambi ndi amene anatulutsa Baibuloli ndipo anthu 3,051 anapezekapo.

Abale ndi alongo 7 anagwira ntchito yomasulira Baibuloli. Mmodzi mwa omasulirawa anati: “Mu Baibulo la Dziko Latsopano muli mawu osavuta kumva ndipo zimenezi zithandiza anthu amisinkhu yonse kuphatikizapo ana kuti asamavutike kumva zomwe akuwerenga. Sitikukayikira kuti liwathandizanso kuyandikira kwambiri Yehova, yemwe ndi Atate wawo wakumwamba.”

M’mbuyomu, ofalitsa omwe amalankhula Chinzema akhala akugwiritsa ntchito Baibulo lomwe linamasuliridwa ndi bungwe la Bible Society of Ghana. Koma m’Baibuloli mulibe dzina la Mulungu ndiponso ndi lovuta kumvetsa. Komanso Mabaibulo ena ndi okwera mtengo ku Ghana choncho ofalitsa ena sankakwanitsa kupeza Baibulo.

Mosiyana ndi Mabaibulo amenewa, mu Baibulo la Dziko Latsopano muli dzina la Mulungu lakuti Yehova, linamasuliridwa momveka bwino ndiponso sitigulitsa. Baibuloli lithandiza kuti ofalitsa 1,532 omwe amalankhula Chinzema azilalikira mosavuta kwa anthu 330,000 olankhula chinenerochi m’gawo la nthambi ya Ghana.

Tikukhulupirira kuti Baibulo latsopanoli lithandiza abale athuwa ‘kukondwera ndi chilamulo cha Yehova.’—Salimo 1:1, 2.