APRIL 29, 2016
JAPAN
Zivomezi ku Japan
Pa 14 ndi pa 16 April, 2016, pachilumba cha Kyushu, chomwe chili ku mpoto kwa dziko la Japan, panachitika zivomezi ziwiri zamphamvu kwambiri. Zivomezi zimenezi zitayezedwa ndi chipangizo choyezera mphamvu za chivomezi, choyamba chinali champhamvu 6.5 ndipo chachiwiri chinali champhamvu 7.3. Kuchokera panthawiyi, pachilumbachi pakhala pakuchitika zivomezi zina zing’onozing’ono zambiri. Ku dera limene linakhudzidwa ndi zivomezi zimenezi, kuli mipingo ya Mboni za Yehova pafupifupi 70 koma palibe wa Mboni wina aliyense amene anavulala kwambiri kapena kufa. Komabe nyumba 70 za anthuwa zinawonongeka kwambiri ndipo zokwana 17 zinagweratu. Chifukwa chakuti pachilumbachi pankachitikabe zivomezi zina zing’onozing’ono, a Mboni za Yehova oposa 400 anasamutsidwa kuchoka m’nyumba zawo n’kumakakhala m’Nyumba za Ufumu ndipo ankapatsidwanso chakudya. Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Japan inakhazikitsa komiti ya anthu ongodzipereka omwe ali ndi luso la zomangamanga kuti athandize anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi.
Lankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Japan: Ichiki Matsunaga, tel. +81 46 233 0005