Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 27, 2015
KAZAKHSTAN

A Mboni za Yehova Anagawa Baibulo la Chinenero cha Chikazaki Pamsonkhano Komanso Pamwambo Umene Anaitanira Anthu Ambiri

A Mboni za Yehova Anagawa Baibulo la Chinenero cha Chikazaki Pamsonkhano Komanso Pamwambo Umene Anaitanira Anthu Ambiri

A Gerrit Lösch a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova akutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chikazaki.

ALMATY, Kazakhstan—Pa September 26 mpaka 28, 2014, a Mboni za Yehova anachita msonkhano wachigawo ndipo anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chikazaki. Anthu 3,721 omwe anasonkhana analandira Baibulo latsopanoli.

Katswiri wina wa zinenero za Chitheke, Dr. Alexander Garkavets, anafotokozapo zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano la Chikazaki. Iye anati: “A Mboni anagwira ntchito yotamandika zedi ngakhale kuti anali ndi zipangizo zochepa zothandiza kumasulira Baibulo m’Chikazaki. Tikuwayamikira kwambiri chifukwa chakuti mfundo zochokera m’Baibulo la Chingelezi azimasulira m’njira yomveka bwino m’Baibulo la Chikazaki. Baibulo la Dziko Latsopano alimasulira mogwizana ndi m’mene anthu akulankhulira chinenerochi panopa ndipo anthu ambiri akulimvetsa mosavuta.”

Tsiku lapadera lokaona malo: A Mboni anakonza kanyumba ndipo anakagwiritsa ntchito pogawa chakudya kwa anthu amene anabwera kudzaona malowa.

Ofesi ya Mboni za Yehova m’dzikoli inakonza zoti mlungu wotsatira pa October 3, anthu adzaone malo pa ofesiyi ndipo patsikulo anagawanso Baibulo latsopanoli. Wailesi ina ya m’dzikoli inaulutsa zokhudza tsiku lapaderali ndipo inati: “Kumalowa kunapita akuluakulu a mzinda wa Akimat, motsogoleredwa ndi bambo Nurzhan Zhaparkul omwe ndi woyang’anira zinthu zokhudza zipembedzo, kunapitanso oimira akazembe, akatswiri amaphunziro azipembedzo ndi anthu enanso.” (Radio Azattyq) Bambo Zhaparkul ananena kuti: “A Mboni za Yehova anatilandira ndi manja awiri ku ofesi yawo ya ku Almaty. Tikuyamikira kwambiri zimene a Mboni anachitazi ndipo zitithandiza pa ntchito yathu.”

Bambo Nurzhan Zhaparkul (pakati), yemwe ndi mkulu wa Bungwe Loona za Zipembedzo, ndiponso akuluakulu a Komiti ya Bungwe Loona za Zipembedzo akuona malo pa Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova patsikuli.

A Mboni mumzinda wa Almaty anagawa mapepala oitanira anthu ku mwambowu.

Bambo Polat Bekzhan omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Kazakhstan, ananena kuti: “Tinasangalala kwambiri kuona anthu ambiri atabwera ku msonkhano wachigawo chaka chino ndiponso kuona mmene asangalalira atalandira Baibulo la m’chinenero cha Chikazaki. Tinkafuna kuti akuluakulu aboma, atolankhani ndiponso anthu ena akhale ndi mwayi wodziwa bwino zimene a Mboni za Yehova amachita ndipo tinasangalala kwambiri kuona kuti cholinga chathuchi chinakwaniritsidwa.”

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Kazakhstan: Polat Bekzhan, tel. +7 727 232 36 62